LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 September masa. 2-7
  • ‘Itanani Akulu’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • ‘Itanani Akulu’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NDI LITI POMWE TIYENERA ‘KUITANA AKULU’?
  • N’CIFUKWA CIANI TIFUNIKA KUITANA AKULU?
  • KODI AKULU AMATITHANDIZA MOTANI?
  • UDINDO UMENE TILI NAO
  • Mmene Akulu Amaonetsela Cikondi na Cifundo Kwa Munthu Wocita Chimo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Dongosolo la Mpingo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Abale​—Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukayenelele Kukhala Mkulu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Abusa Amene Amagwila Nchito Yothandiza Anthu a Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 September masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZIRA 36

NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna

‘Itanani Akulu’

“Aitane akulu a mpingo.”​—YAK. 5:14.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Cifukwa cake muyenera kuitana akulu a mumpingo mukafunikira thandizo lauzimu.

1. Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti nkhosa zake ndi zamtengo wapatali kwa iye?

NKHOSA za Yehova ndi zamtengo wapatali kwa iye. Anazigula ndi magazi a Yesu, ndipo anapereka udindo kwa akulu mumpingo kuti azizisamalira. (Mac. 20:28) Mulungu amafuna kuti nkhosa zake zizisamalidwa mwacikondi. Pansi pa citsogozo ca Khristu, akulu amatsitsimula nkhosazo ndi kuziteteza ku zinthu zimene zingazibvulaze mwauzimu.​—Yes. 32:​1, 2.

2. Kodi Yehova amasamalira ndani mwapadera? (Ezekieli 34:​15, 16)

2 N’zoona kuti Yehova amasamala kwambiri nkhosa zake zonse. Koma iye amasamalira mwapadera nkhosa zimene zikubvutika. Kudzera mwa akulu, iye amathandiza ao amene akudwala mwauzimu. (Werengani Ezekieli 34:​15, 16.) Komabe iye amafuna kuti tizipempha thandizo pakafunika kutero. Pa nthawi ngati zimenezo, kuonjezera pa mapemphero athu omuconderera Mulungu kuti atithandize, timapemphanso thandizo kwa “abusa ndi aphunzitsi” mumpingo.​—Aef. 4:​11, 12.

3. Timapindula motani tikazindikira udindo wa akulu?

3 Mu nkhani ino, tikambirana makonzedwe amene Yehova walinganiza kuti tizipeza thandizo lauzimu kwa akulu. Tiyankha mafunso awa: Ndi liti pamene tiyenera kupempha thandizo kwa akulu? N’cifukwa ciani tiyenera kupempha thandizo kwa iwo? Nanga kodi iwo amatithandiza motani? Ngakhale kuti palipano sitikudwala mwauzimu, mayankho a mafunso amenewa angatithandize kukulitsa ciyamikiro cathu pa makonzedwe amene Mulungu waika m’malo ogwiritsa nchito akulu kuti azitithandiza. Ndipo tingadzapindule ndi makonzedwe amenewa m’tsogolo.

NDI LITI POMWE TIYENERA ‘KUITANA AKULU’?

4. N’cifukwa ciani tingakambe kuti Yakobo 5:​14-16, 19, 20 imafotokoza za kudwala kwauzimu? (Onaninso zithunzi.)

4 Pofotokoza za makonzedwe amene Mulungu analinganiza kuti tizipeza thandizo lauzimu, wophunzira Yakobo anayamba mwa kufunsa kuti: “Kodi pali aliyense amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo.” (Werengani Yakobo 5:​14-16, 19, 20.) Mavesi ozungulira nkhaniyi amaonetsa kuti Yakobo anali kukamba za kudwala mwauzimu. Mwacitsanzo, wodwala amene akufotokozedwa mu nkhaniyi akuuzidwa kuti aitane akulu, osati dokotala. Ndipo Yakobo anafotokozanso kuti munthu amene akudwala angacire macimo ake akakhululukidwa. Kuwonjezera apo, masitepe amene munthu amatsatira kuti acire kuthupi ndi ofanana ndi masitepe amene munthu amatsatira kuti acire kuuzimu. Tikadwala kuthupi timapita kukaonana ndi dokotala, kumufotokozera mmene tikumvera, ndi kutsatira zimene watiuza kucita. Mofananamo, tikadwala kuuzimu, tizipita kukaonana ndi akulu kuwafotokozera bvuto lathu, ndi kutsatira ulangizi wa m’Malemba umene atipatsa.

Zithunzi: 1. Mwamuna akufotokozera dokotala vuto limene ali nalo paphewa pake. 2. M’bale akufotokozera mkulu bvuto limene ali nalo pomwe akhala pabenci pabwalo.

Tikadwala timakaonana ndi dokotala. Tikadwala kuuzimu tiyenera kukaonana ndi akulu (Onani ndime 4)


5. Tingadziwe bwanji kuti tatsala pang’ono kuyamba kudwala kuuzimu?

5 Makonzedwe ofotokozedwa mu Yakobo caputala 5 amatilimbikitsa kufikira akulu tikaona kuti thanzi lathu lauzimu layamba kufooka. Zimakhala bwino kuwoloka mtsinje madzi akali m’nkhongono. Conco, cimakhala canzeru kufunsira thandizo kwa akulu ubwenzi wathu ndi Mulungu usanaonongeke. Baibo imaticenjeza kuti ngati sitinasamale tingayambe kuganiza kuti tili paubwenzi wolimba ndi Yehova, pomwe m’ceniceni si mmene zilili. (Yak. 1:22) Akhristu ena oyambirira a mumpingo wa Sade, anaganizapo mwanjira imeneyi. Ndipo Yesu anawacenjeza za kaimidwe kao kauzimu. (Chiv. 3:​1, 2) Cimodzi cimene cingatithandize kuona mmene thanzi lathu lauzimu lilili ndi kuyerekezera mmene timacitira palipano pa nkhani ya kulambira ndi mmene tinali kucitira kale. (Chiv. 2:4, 5) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi cimwemwe cimene ndimakhala naco powerenga Baibo ndi kusinkhasinkha cayamba kucepa? Kodi ndabwerera pansi pa nkhani ya kukonzekera misonkhano ndi kupezekapo? Kodi cangu canga pa ulaliki cabwerera pansi? Kodi nthawi yanga yoculuka ndimaigwiritsa nchito pa zosangalatsa ndi kufuna-funa cuma? Kodi ndimaganizira kwambiri za ndalama kuposa mmene ndinali kucitira kale?’ Ngati yankho lanu ndi lakuti inde pa lililonse la mafunsowa, ndi cizindikiro cakuti muli ndi cifooko cinacake cimene muyenera kugwirirapo nchito. Ngati sitingakwanitse kuongolera pa ife eni, kapena ngati taphwanya kale malamulo a Mulungu, tingacite bwino kupempha thandizo kwa akulu.

6. Kodi amene wacita chimo lalikulu afunika kucita ciani?

6 Komabe, munthu amene wacita chimo lalikulu, limene lingacititse kuti acotsedwe mumpingo, ayenera kufikira akulu. (1 Akor. 5:​11-13) Munthuyo afunikira thandizo kuti akonze ubale wake ndi Yehova. Kuti Yehova atikhululukire kudzera mu nsembe ya dipo, tiyenera kucita “zinthu zosonyeza kulapa.” (Mac. 26:20) Cimodzi mwa zinthuzo ndi kufikira akulu tikacita chimo lalikulu.

7. Ndaninso ena angakufunikire thandizo la akulu?

7 Akulu samangothandiza ao amene acita chimo lalikulu. Amathandizanso ao amene afooka mwauzimu. (Mac. 20:35) Mwacitsanzo, mwina mukuona kuti n’zobvuta kugonjetsa zilakolako zoipa. Zingakhale zobvuta kwambiri maka-maka ngati musanaphunzire coonadi munali ndi cizolowezi cogwiritsa nchito amkolabongo, munali kupenyerera zamalisece, kapena munali kukhala umoyo wotayirira. Simuyenera kumva kuti muli nokha polimbana ndi zinthu zimenezi. Mungasankhe kukambirana ndi mkulu amene muona kuti angakumvetsereni ndi kukupatsani thandizo, komanso kukutsimikizirani kuti mungakwanitse kukondweretsa Yehova mwa kupewa kucita zimene zilakolako zoipa zikufuna. (Mlal. 4:12) Ngati mukudziimba mlandu poona kuti mukugonja polimbana ndi zilakolako zoipa, akulu angakukumbutseni kuti mwacionekere ico ndi cizindikiro coonetsa kuti mumaona ubwenzi wanu ndi Yehova kukhala wofunika kwambiri komanso kuti mukupewa kudzidalira.​—1 Akor. 10:12.

8. Ndi macimo monga ati omwe nthawi zina sitiyenera kuuza akulu?

8 Koma si nthawi zonse pamene tingafunike kupita kwa akulu pa bvuto lauzimu limene tingakhale nalo. Mwacitsanzo, ngati nthawi ina munakambapo mau amene anakhumudwitsa wina ndipo munamukwiyira kwambiri, m’malo mokafikira mkulu, mungacite bwino kugwiritsa nchito uphungu umene Yesu anapereka wakuti muyenera kubwezeretsa mtendere ukasokonekera. (Mat. 5:​23, 24) Mungacite bwino kufufuza nkhani zokhudza kufatsa, kuleza mtima, ndi kudziletsa, kuti mukathe kuonetsa makhalidwe amenewa m’tsogolo. Ngati zabvutabe kuti mubwezeretse mtendere, muyenera kupempha thandizo kwa mkulu. M’kalata yake yopita ku mpingo wa Afilipi, mtumwi Paulo anapempha m’bale winawake kuti athandize Eodiya ndi Suntuke kubwezeretsa mtendere pakati pao. Nayenso mkulu wa mumpingo mwanu angakuthandizeni mwa njira imeneyi.​—Afil. 4:​2, 3.

N’CIFUKWA CIANI TIFUNIKA KUITANA AKULU?

9. N’cifukwa ciani sitiyenera kulola manyazi kutilepheretsa kufikira akulu? (Miyambo 28:13)

9 Pamafunika cikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti tipemphe thandizo tikacita chimo lalikulu, kapena tikaona kuti tikugonja ku zilakolako zoipa. Tisalole manyazi kutilepheretsa kuitana akulu. N’cifukwa ciani? Tikatsatira makonzedwe a Yehova ofikira akulu tikakhala ndi bvuto linalake, timaonetsa kuti timam’khulupirira, komanso timakhulupirira malangizo ake otithandiza kulimbitsa cikhulupiriro cathu. Timaonetsanso kuti tikufunikira thandizo lake pamene talephera kucita zinthu zoyenera. (Sal. 94:18) Ndipo ngati tacita chimo, Mulungu adzationetsa cifundo ngati taulula ndi kusiya macimo athu.​—Werengani Miyambo 28:13.

10. Cingacitike n’ciani ngati tabisa macimo athu?

10 Tikaulula macimo athu kwa akulu, timalandira madalitso ambiri. Koma tikawabisira, zinthu zimangoipira-ipira. Pamene Mfumu Davide anayesa kubisa macimo ake anabvutika mwauzimu, m’maganizo, komanso kuthupi. (Sal. 32:​3-5) Tikadwala kapena tikabvulala n’kulephera kupeza thandizo la mankhwala mofulumira, bvutolo limakulirakulira. Ndi mmenenso zilili ndi bvuto lauzimu. Yehova samafuna zaconco kuticitikira. Conco, iye amatiuza kuti tizipempha thandizo kwa akulu kuti atithandize kukhalanso naye pa ubwenzi.​—Yes. 1:​5, 6, 18.

11. Kodi abale ndi alongo zimawakhudza motani tikabisa macimo akulu-akulu?

11 Ngati sitinaulule macimo athu akulu-akulu, zimakhudzanso anthu ena. Tingalepheretse mzimu wa Mulungu kugwira bwino nchito pampingo, ndipo tingasokonezenso mtendere wa abale ndi alongo athu. (Aef. 4:30) Mofananamo, tikadziwa kuti wina mumpingo wacita chimo lalikulu, tifunika kumulimbikitsa kuti akafikire akulu.a Kubisa chimo la munthu wina kungacititse kuti ifenso tikhale ndi mlandu. (Lev. 5:1) Cikondi cathu pa Yehova ciyenera kutisonkhezera kuuza akulu za chimolo ngati wocimwayo sakucitapo kanthu. Tikatero timathandiza kuti mumpingo mukhale ciyero komanso kuti wolakwayo akhalenso paubale wabwino ndi Yehova.

KODI AKULU AMATITHANDIZA MOTANI?

12. Kodi akulu amawathandiza bwanji amene afooka kuuzimu?

12 Akulu amalangizidwa kuthandiza ao amene afooka kuuzimu. (1 Ates. 5:14) Ngati munacita chimo, akulu angakufunseni mafunso mwaluso kuti adziwe maganizo anu ndi mmene mukumvera. (Miy. 20:5) Conco, zingakhale zothandiza kufotokoza mmene zinthu zilili ngakhale kuti zingakhale zobvuta kucita zimenezo cifukwa ca cikhalidwe canu, umunthu wanu, kapena cifukwa ca manyazi amene mungakhale nao kaamba ka bvuto limene muli nalo. Musaope poganiza kuti mau anu adzaoneka ngati ‘mukulankhula mosaganiza bwino.’ (Yobu 6:3) M’malo mofulumira kukupatsani malangizo pa nkhaniyo, akulu adzayesetsa kukumvetserani mwacheru ndi kuimvetsa bwino nkhani yonse. (Miy. 18:13) Akulu amadziwa kuti kuthandiza nkhosa kumalira nthawi. Conco iwo angakambe nanu maulendo angapo kuti akupatseni thandizo lofunikira.

13. Kodi akulu angatithandize bwanji kudzera m’mapemphero ao komanso m’malangizo a m’Malemba? (Onaninso zithunzi.)

13 Mukaitana akulu, iwo adzayesetsa kupewa kuonjezera ululu pa cisoni cimene muli naco kale. M’malomwake, iwo adzakupemphererani. Yehova adzamvetsera mapemphero ao amene amagwira nchito “mwamphamvu kwambiri.” Ndipo mudzalimbikitsidwa komanso kutonthozedwa m’njira imene simunayembekezere. Thandizo lao limaphatikizapo ‘kukupakani mafuta m’dzina la Yehova.’ (Yak. 5:​14-16) “Mafuta” amenewa amatanthauza coonadi ca m’Mau a Mulungu. Iwo amagwiritsa nchito Baibo mwaluso kuti akutsitsimuleni, kukulimbikitsani, ndi kukuthandizani kuti mukhalenso pa ubale wabwino ndi Yehova. (Yes. 57:18) Malangizo a m’Baibo omwe iwo angapereke angakupatseni mphamvu kuti mupitirize kucita zoyenera. Kupitira mwa iwo, mungamve mau a Yehova akukuuzani kuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.”​—Yes. 30:21.

Zithunzi: 1. Dokotala yemwe taona pacithunzi capita akugwira-gwira phewa la wodwala uja pofuna kupeza pomwe pali bvuto. Pakhoma pali ekiselo yoonetsa phewa la wodwalayu. 2. Mkulu yemwe taona pacithunzi capita limodzi ndi mkulu wina akugwiritsa nchito Baibo polimbikitsa m’bale uja ku nyumba kwake. M’baleyu akumvetsera akuluwo mosangalala.

Akulu amasewenzetsa Baibo kuti atonthoze ndi kulimbikitsa odwala kuuzimu (Onani ndime 13-14)


14. Malinga ndi Agalatiya 6:​1, kodi akulu amawathandiza motani ao amene alowera “njira yolakwika”? (Onaninso zithunzi)

14 Werengani Agalatiya 6:1. Mkhristu akalowera “njira yolakwika” ndiye kuti sakuyenda mogwirizana ndi miyeso yolungama ya Mulungu. Njira yolakwika ingatanthauze kupanga cisankho colakwika kapena kuphwanya malamulo a Mulungu. Mosonkhezeredwa ndi cikondi, akulu acikhristu amayesetsa “kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.” Mau a Cigiriki amene anawamasulira kuti “kuthandiza” pa lembali, anali kugwiritsidwa nchito pofotokoza zimene dokotala anali kucita pobwezeretsa fupa limene lathyoka kuti likhalenso bwino. Monga mmene dokotala waluso amacitira pothandiza munthu amene wathyoka fupa popanda kuonjezera ululu, akulu naonso amaona mmene angaticiritsire mwauzimu popanda kuonjezera ululu umene tili nao kale. Amalangizidwanso kuti ayenera ‘kucita zimenezi mosamala.’ Pamene akulu akutithandiza kuongola njira yathu, naonso amazindikira kuti ndi opanda ungwiro ndi kuti angalowere njira yolakwika. M’malo modziona kuti ndi olungama kwambiri, komanso amacita bwino kuposa munthuyo, akulu amakhala odzicepetsa, ndipo amacita naye mwacifundo munthuyo.​—1 Pet. 3:8.

15. Kodi tiyenera kucita ciani tikakhala ndi bvuto linalake?

15 Tili ndi zifukwa zomveka zotipangitsa kuwadalira akulu. Akulu anaphunzitsidwa kutisungira cinsinsi, kupereka uphungu wa m’Baibo m’malo mogwiritsa nchito maganizo ao, komanso kutithandiza mmene tingathetsere mabvuto. (Miy. 11:13; Agal. 6:2) Ngakhale kuti akulu ali ndi maumunthu osiyana-siyana, ndipo ena akhala akulu kwa nthawi yaitali kuposa ena, tiyenera kukhala omasuka kufikira mkulu aliyense kuti atithandize kulimbana ndi mabvuto athu. Conco, tisamacite kuti tafunsira kwa mkulu uyu kenako n’kupita kwa wina pofuna kuti tipeze mkulu amene angatipatse malangizo amene tingakonde kumva. Ngati tingacite zimenezo, tingakhale ngati aja amene amafuna anthu owauza “zowakomera m’khutu” m’malo ‘mophunzitsidwa zolondola’ za m’Mau a Mulungu. (2 Tim. 4:3) Tikauza mkulu za bvuto linalake angatifunse ngati tinauzako akulu ena komanso malangizo amene anatipatsa. Ndipo cifukwa cakuti mkuluyo ndi wodzicepetsa, asanapereke malangizo alionse kwa inu, adzakambirana ndi mkulu wina kuti amuthandize.​—Miy. 13:10.

UDINDO UMENE TILI NAO

16. Kodi tili ndi udindo wotani?

16 Ngakhale kuti akulu ali ndi udindo woyang’anira ife monga nkhosa za Mulungu, iwo alibe mphamvu yotipangira zisankho. Aliyense wa ife ali ndi udindo woonetsa Yehova m’zokamba komanso zocita zake kuti amamukonda, komanso kuti amafuna kucita zom’kondweretsa. Iye angatithandize kuti tipange zisankho zanzeru ndi kukhala okhulupirika kwa iye. (Aroma 14:12) Conco, m’malo motipatsa malamulo ambiri-mbiri amene tiyenera kutsatira, akulu amagwiritsa nchito Baibo potithandiza kumvetsa kaganizidwe ka Mulungu kopezeka m’Mau ake. Mwa kutsatira ulangizi wao wozikika m’Baibo, tingakwanitse ‘kugwiritsa nchito luso [lathu] la kuganiza’ kuti tipange zisankho zanzeru.​—Aheb. 5:14.

17. Kodi tiyenera kutsimikiza kucita ciani?

17 Ndi mwai waukulu zedi kukhala nkhosa ya Yehova. Iye anatumiza “m’busa wabwino,” Yesu, kudzalipira dipo kuti tikhale ndi mwai wodzakhala ndi moyo wosatha. (Yoh. 10:11) Ndipo kudzera mwa akulu mumpingo wacikhristu, Yehova wakwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Ndidzakupatsani abusa amene amacita zinthu zogwirizana ndi zofuna zanga ndipo adzakuthandizani kuti mudziwe zinthu zambiri, ndiponso kuti mukhale omvetsa zinthu.” (Yer. 3:15) Tikafooka kapena tikadwala mwauzimu, tisazengereze kuitana akulu kuti atithandize. Tiyeni tikhale otsimikiza mtima kupitiriza kupindula mokwanira ndi thandizo limene Yehova akutipatsa kudzera mwa akulu mumpingo.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Ndi liti pamene tiyenera kupempha thandizo kwa akulu?

  • N’cifukwa ciani tiyenera kupempha thandizo kwa akulu?

  • Kodi akulu amatithandiza bwanji?

NYIMBO 31 Uziyenda na Mulungu

a Ngati nthawi ikupitapo ndipo wolakwayo sakuuza akulu, kukhulupirika kwanu kwa Yehova kudzakusonkhezerani kukawauza zimene mukudziwapo pa nkhaniyo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani