LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsa. 11
  • Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvela Cisoni Mumtima Mwawo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvela Cisoni Mumtima Mwawo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Yehova “Amacilitsa Anthu Osweka Mtima”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • “Kuyandikila kwa Mulungu Ndi Cinthu Cabwino” kwa Ife!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Yehova Adzakuthandizani m’Nthawi Zovuta
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 September tsa. 11

UMOYO WATHU WACIKHRITU

Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvela Cisoni Mumtima Mwawo

Aliyense wa ife amamva cisoni nthawi zina. Ndipo kumva cisoni si cizindikilo cakuti ndife ofooka mwauzimu. Malemba amaonetsa kuti ngakhale Yehova amene, amamva cisoni nthawi zina. (Gen. 6:​5, 6) Koma bwanji ngati timakhala na cisoni cacikulu kaŵili-kaŵili kapena nthawi zonse?

Pemphani thandizo kwa Yehova. Yehova amacita cidwi kwambili na mmene timamvela. Amadziŵa ngati ndife osangalala kapena acisoni. Komanso amadziŵa cifukwa cake timamva mwanjila imeneyo. (Sal. 7:9b) Coposa zonse, Yehova amasamala za ife, ndipo angatithandize tikakhala na cisoni ngakhale tikapsinjika maganizo.—Sal. 34:18.

Tetezani maganizo anu. Maganizo olefula angatilande cimwemwe komanso angasokoneze kulambila kwathu. Ndiye cifukwa cake tiyenela kuteteza mtima wathu, kapena kuti umunthu wathu wamkati.—Miy. 4:23.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI MMENE ABALE AKUKHALILABE PA MTENDELE OLO KUTI ALI NA VUTO LA KUPSINJIKA MAGANIZO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Ni zinthu ziti zimene Nikki anacita polimbana na vuto lake la kupsinjika maganizo?

  • N’cifukwa ciyani Nikki anaona kuti ayenela kulandila thandizo la ku cipatala?—Mat. 9:12

  • Kodi Nikki anaonetsa m’njila ziti kuti anali kudalila thandizo la Yehova?

“Nsanja ya Mlonda” ya Na. 1 2023, ya mutu wakuti “Baibo Ingathandize Odwala Matenda a Maganizo.”

Kodi mudziŵako aliyense amene angapindule na Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya Na. 1 2023?

Ni zinthu zina ziti zimene tingacite kuti titeteze maganizo athu?

(Pansipa, congani zizoloŵezi zimene mufuna kukulitsa.)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani