Yobu akuonetsa cikondi cosasintha kwa anthu ovutika
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mbili Yanu ili Ngati ya Yobu?
Anthu okhala naye pafupi anali kumulemekeza (Yobu 29:7-11)
Yobu anali kudziŵika na khalidwe loonetsa cikondi cosasintha kwa anthu ovutika (Yobu 29:12, 13; w02 5/15 22 ¶19; onani cithunzi ca pacikuto)
Yobu anaonetsa kuti anali wacilungamo (Yobu 29:14; it-1 655 ¶10)
Mbili yabwino ni yamtengo wapatali. (w09 2/1 15 ¶3-4) Mbili yabwino imapangika munthu akakhala akuonetsa khalidwe labwino kwa nthawi yaitali.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimadziŵika na makhalidwe otani?’