LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w21 October masa. 29-31
  • 1921—Zaka 100 Zapitazo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 1921—Zaka 100 Zapitazo
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ALALIKI OLIMBA MTIMA
  • PHUNZILO LAUMWINI KOMANSO LA BANJA
  • BUKU LATSOPANO
  • NCHITO YOFUNIKA KUIGWILA
  • Kucita Zimene Yehova Watilamula Kumabweletsa Madalitso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • 1922—Zaka 100 Zapitazo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • 1923​—Zaka 100 Zapitazo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
w21 October masa. 29-31

1921 Zaka 100 Zapitazo

MAGAZINI ya Nsanja ya Mlonda ya January 1, 1921, inali na funso lopita kwa oŵelenga lakuti: “Conco, tili na nchito yanji patsogolo pathu caka cino?” Poyankha funsoli, inagwila mawu lemba la Yesaya 61:1, 2, imene inawakumbutsa za nchito yawo yolalikila. Lembali limati: “Yehova wandidzoza kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa . . . kuti ndikalengeze za caka ca Yehova cokomela anthu mtima, ndi za tsiku lobwezela la Mulungu wathu.”

ALALIKI OLIMBA MTIMA

Kuti akwanilitse nchito yawo, Ophunzila Baibo anafunika kukhala olimba mtima. Iwo anayenela kulengeza “uthenga wabwino” kwa anthu ofatsa, komanso za “tsiku lobwezela” anthu oipa.

M’bale J. H. Hoskin, wa ku Canada, analalikila molimba mtima olo kuti anali kutsutsidwa. Mu 1921, iye anakumana na m’busa wina wacipembedzo. M’bale Hoskin anayambitsa makambilano mwa kunena kuti: “Tikambilane mwamtendele nkhani za m’Baibo. Koma tikalephela kugwilizana, makambilano athu tiwathetsenso mwamtendele.” Koma zimene anagwilizana sizinacitike. M’bale Hoskin anati: “Titakambitsilana kwa mphindi zocepa, [m’busayo] anamenya pa citseko mwamphamvu cakuti n’naona monga galasi ya pa citsekopo idzagwa n’kupwanyika.”

Mwaukali m’busayo anati, “N’cifukwa ciani simulalikila anthu amene si Akhristu?” M’bale Hoskin anangokhala cete, koma atasiyana na m’busayo, mu mtima anati, ‘M’busayu akucita zinthu monga si Mkhristu!’

Tsiku lotsatila, pamene m’busayo anali kulalikila m’chalichi, anakamba zoipa zokhudza m’bale Hoskin. M’baleyu anati: “M’busayo anauza anthu ake kuti n’nali kulankhula mabodza a mkunkhuniza, komanso kuti n’nayenela kuphedwa. M’bale wathu sanabwelele m’mbuyo, koma anapitiliza kulalikila anthu ambili. Iye anati: “N’nali kusangalala kulalikila kumeneko. Anthu ena anafika pokamba kuti, ‘Tidziŵa kuti ndinu munthu wa Mulungu!’ Cina, iwo anadzipeleka kuti azinipatsa zofunikila pa umoyo.”

PHUNZILO LAUMWINI KOMANSO LA BANJA

Pofuna kuthandiza anthu kumvetsa Baibo, Ophunzila Baibo anali kukonza mafunso na mayankho ake, m’magazini imene tsopano imachedwa Galamuka! M’magazini imeneyo munali mafunso a m’Baibo okonzedwela acicepele, amene makolo anali kukambilana na ana awo. Makolowo anali kufunsa ana awo mafunsowo, na kuwathandiza kupeza mayankho m’Baibo. Mafunso ena monga lakuti, “Kodi m’Baibo muli mabuku angati?,” anali kuphunzitsa mfundo zosavuta za m’Baibo. Funso lina linali lakuti, “Kodi Mkhristu woona aliyense ayenela kuyembekezela cizunzo?” Funsoli linakonzekeletsa acicepele kukhala alaliki olimba mtima.

Panalinso mafunso ena na mayankho ake, okonzedwela aja amene anali na cidziŵitso cokulilapo ca m’Baibo. Mayankhowo anali kupezeka m’buku la Cizungu lakuti, Studies in the Scriptures voliyumu yoyamba. Anthu masauzande ambili anapindula na pulogilamu imeneyi. Koma m’magazini ya The Golden Age ya December 21, 1921, munali cilengezo cakuti pulogilamu imeneyi yatha. N’cifukwa ciani panakhala kusintha?

BUKU LATSOPANO

Buku la Zeze wa Mulungu

Makadi oonetsa mbali yoŵelenga

Makadi okhala na mafunso

Amene anali kutsogolela anaona kuti maphunzilo a Baibo atsopano, afunika kuphunzila coonadi mwadongosolo. Conco, mu November 1921, buku lakuti Zeze wa Mulungu linatulutsidwa. Anthu acidwi amene analandila bukuli, naonso analembedwa kuti ayambe kucita maphunzilo a Baibo pa okha poseŵenzetsa bukuli. Maphunzilo amenewo, anathandiza anthu kudziŵa colinga ca Mulungu cakuti adzapatsa anthu moyo wosatha. Kodi anali kucitika motani?

Wophunzila Baibo akalandila bukulo, anali kupatsidwa kakhadi koonetsa masamba amene ayenela kuŵelenga. Mlungu wotsatila, anali kupatsidwa khadi yokhala na mafunso ozikidwa pa mbali imene anali kuŵelenga. Khadiyo inali kukhalanso na mbali imene iye adzaŵelenge mlungu wotsatila.

Mlungu uliwonse kwa milungu 12, wophunzila anali kulandila khadi yatsopano kucokela ku mpingo. Kambili, amene anali kutumiza makadiwo anali okalamba, kapena aja amene sanali kukwanitsa kulalikila nyumba na nyumba. Mwacitsanzo, mlongo Anna K. Gardner, wa ku Millvale, Pennsylvania, U.S.A., anati: “Buku la Zeze wa Mulungu litatulutsidwa, mkulu wanga Thayle, amene sanali kukwanitsa kuyenda anakhala na nchito yaikulu yotumiza makadi a mafunso mlungu uliwonse.” Munthu akatsiliza maphunzilowo, wina mu mpingo anali kupita kwa iye kukam’thandiza kuphunzila zowonjezeleka za m’Baibo.

Mlongo Thayle Gardner pa njinga ya olemala

NCHITO YOFUNIKA KUIGWILA

Kumapeto kwa caka, M’bale J. F. Rutherford anatumiza kalata ku mipingo. Iye anati “nchito yolalikila za Ufumu yayenda bwino kwambili caka cino kuposa zaka za m’mbuyomu.” Anakambanso kuti: “Koma pali nchito yaikulu yofunika kuigwila. Limbikitsani ena kuti agwile nafe nchito yabwino ngako imeneyi.” Ophunzila Baibo anamvela malangizo amenewa. Conco, mu 1922, iwo analengeza uthenga wa Ufumu mopanda mantha kuposa kale lonse.

Mabwenzi Opanda Mantha

Ophunzila Baibo anali kuonetsa cikondi ca paubale mwa kuthandizana. Iwo anali mabwenzi opanda mantha, “obadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto,” monga mmene nkhani yotsatila ionetsela.—Miy. 17:17.

Pa Ciŵili, May 31, 1921, m’tauni ya Oklahoma ku America, munayamba cipolowe pambuyo pakuti munthu wakuda waponyedwa m’ndende pa mlandu wovulaza mkazi waciyela. Gulu la anthu aciyela oposa 1,000, linayamba kumenyana na gulu laling’ono la anthu akuda. Kumenyana kumeneko kunafika mpaka m’tauni ya Greenwood, kumene nyumba zoposa 1,400 zinatenthedwa, ndipo katundu wambili anabedwa. Lipoti linaonetsa kuti anthu amene anafa anali 36, koma m’ceniceni anali kufika m’mahandiledi.

M’bale Richard J. Hill, Wophunzila Baibo wakuda komanso nzika ya m’tauni ya Greenwood, anafotokoza zimene zinacitika. Iye anati: “Tsiku limene kunacitika cipolowe cimeneci, tinali kuphunzila Baibo. Titatsiliza kuphunzila, tinamva anthu akuombelana mfuti. Izi zinacitika mpaka pakati pa usiku.” Pofika pa Citatu m’maŵa pa June 1, zinthu zinafika poipa kwambili. Iye anati: “Gulu la anthu linabwela na kutiuza kuti tithaŵile ku bwalo lalikulu la boma kuti titetezedwe.” Conco, M’bale Hill na mkazi wake, pamodzi na ana awo asanu anathaŵila ku bwalo limenelo. Kumeneko, amuna na akazi akuda okwana ngati 3,000 anali kutetezedwa na asilikali amene boma linawatuma kuti akathetse cipolowe cimeneco.

Pa nthawi imodzi-modziyo, M’bale Arthur Claus, amene anali waciyela, anacita zinthu mopanda mantha. Iye anati: “N’tamvela kuti anthu ocita cipolowe ali paliponse m’tauni ya Greenwood, kuba katundu, komanso kutentha nyumba za anthu, n’naganiza zopita ku nyumba ya bwenzi langa M’bale Hill kukamuona kuti ali bwanji.”

UM’bale Arthur Claus, anaphunzitsa ana 14 m’buku la Zeze wa Mulungu

Atafika kunyumba kwake, anakumana na munthu waciyela ali na mfuti m’manja. Munthuyo anali kukhala moyandikana na m’bale Hill, komanso anali bwenzi lake. Iye anaganiza kuti m’bale Claus anali m’gulu la anthu ocita cipoloweco. Conco, mwaukali anafunsa kuti, “Wabwela kudzacita ciani pa nyumba ya mwini?”

M’bale Claus anati: “Sembe sin’napeleke yankho lokhutilitsa, iye akananiombela. N’namutsimikizila kuti n’nali bwenzi la M’bale Hill, komanso kuti nthawi zambili n’nali kubwela panyumbapo.” M’bale Claus pamodzi na munthuyo anateteza katundu wa m’bale Hill kwa akawalala.

Posakhalitsa, m’bale Claus anamva zakuti m’bale Hill na banja lake anathaŵila ku bwalo la citetezo. M’bale Claus anauzidwa kuti anthu akuda sakanacoka kumeneko popanda kalata ya cilolezo ca mkulu wa asilikali. M’bale Claus anati: “Cinali covuta kwambili kupita kukaonana na mkulu wa asilikali ameneyo. N’tapita na kumuuza colinga canga, ananifunsa kuti: ‘Kodi udzakwanitsa kuteteza banjali, na kulipezela zofunikila?’ Mwacimwemwe, n’nayankha kuti inde.”

Ali na kalatayo m’manja, m’bale Claus anathamangila ku bwalo limenelo. Iye anapeleka kalatayo kwa msilikali wolondela. Msilikaliyo anati: “Kalatayi yasainidwa na mkulu wa asilikali! Kodi udziŵa kuti ndiwe woyamba kucotsa munthu muno?” M’bale Claus na msilikaliyo anafuna-funa m’bale Hill na banja lake, ndipo anawapeza. Onse anakwela motoka ya m’bale Claus n’kupita ku nyumba.

“Tonse ndife ofanana pokhala atumiki odzipatulila a Mulungu”

M’bale Claus anaonetsetsa kuti m’bale Hill na banja lake ni otetezeka. Kulimba mtima kwake pothandiza abale ake, kunakhala na zotulukapo zabwino. M’bale Claus anati: “Munthu uja amene ananithandiza kuteteza katundu wa m’bale Hill, anayamba kulemekeza kwambili Mboni za Yehova. Ndipo anthu ambili anayamba kucita cidwi na coonadi, poona kuti sitinali kusankhana mitundu cifukwa pakati pathu panalibe woposa mnzake.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani