LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w22 July masa. 8-13
  • Tiyeni Tim’thandizile Yesu Monga Wotiyang’anila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tiyeni Tim’thandizile Yesu Monga Wotiyang’anila
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • YESU AKUYANG’ANILA NCHITO YOLALIKILA
  • YESU ANASANKHA KAPOLO
  • YESU ANAKONZEKELETSA OTSATILA AKE
  • “Kumbukilani Amene Akutsogolela Pakati Panu”
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Kodi Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu Ndani?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Udindo wa “Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu”
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • “Ndani Kweni-kweni Amene Ali Kapolo Wokhulupilika Ndi wanzelu?”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
w22 July masa. 8-13

NKHANI YOPHUNZILA 29

Tiyeni Tim’thandizile Yesu Monga Wotiyang’anila

“Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”—MAT. 28:18.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANEa

1. Kodi cifunilo ca Yehova n’ciyani masiku ano?

CIFUNILO ca Mulungu masiku ano, n’cakuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse lapansi. (Maliko 13:10; 1 Tim. 2:3, 4) Nchito iyi mwini wake ni Yehova. Ndipo m’pake kuti anaiika m’manja mwa Mwana wake wokondeka kuti aziitsogolela. Ndife otsimikiza kuti popeza Yesu ni woyang’anila wosalephela, nchito yolalikila idzamalizika mapeto asanafike, Yehova atakhutila.—Mat. 24:14.

2. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 M’nkhani ino, tione mmene Yesu akugwilitsila nchito “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” popeleka cakudya cauzimu, komanso kukonzekeletsa otsatila ake pa nchito yaikulu yolalikila m’mbili ya anthu. (Mat. 24:45) Tionenso zimene aliiyense wa ife angacite pothandizila Yesu na kapolo wokhulupilika.

YESU AKUYANG’ANILA NCHITO YOLALIKILA

3. Kodi Yesu anapatsidwa udindo wotani?

3 Yesu ndiye akuyang’anila nchito yolalikila. Kodi tidziŵa bwanji zimenezi? Atatsala pang’ono kupita kumwamba, Yesu anakumana na ena mwa otsatila ake okhulupilika pa phili la Galileya. Anawauza kuti: “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Onani cotsatila cimene iye anawauza. Anati: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.” (Mat. 28:18, 19) Motelo, kutsogolela nchito yolalikila ni umodzi mwa maudindo amene Yesu anapatsidwa.

4. N’cifukwa ciyani ndife otsimikiza kuti Yesu akuyang’anila nchito yolalikila?

4 Yesu anakamba kuti nchito yolalikila na kupanga ophunzila idzacitika ku “mitundu yonse,” komanso kuti iye adzakhala pamodzi na otsatila ake “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Mawu amenewa aonetselatu kuti nchito yolalikila idzacitikabe pansi pa uyang’anilo wa Yesu mpaka m’nthawi yathu ino.

5. Kodi timathandizila bwanji kuti mawu a pa Salimo 110:3 akwanilitsidwe?

5 Yesu sanade nkhawa zakuti padzakhala anthu ocepa ogwila nchito yolalikila m’nthawi ya mapeto a dongosolo lino la zinthu. Iye anadziŵa kuti mawu a ulosi a wamasalimo adzakwanilitsidwa. Mawuwo amati: “Anthu ako adzadzipeleka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolela asilikali ako kunkhondo.” (Sal. 110:3) Ngati mumagwilako nchito yolalikila, ndiye kuti mukuthandizila Yesu pamodzi na kapolo wokhulupilika, komanso mukukwanilitsa ulosi umenewo. Nchitoyi ikupitabe patsogolo, koma pali zovuta zina.

6. Kodi alengezi a Ufumu amakumana na vuto lotani masiku ano?

6 Vuto loyamba limene alengezi a Ufumu amakumana nalo, ni kutsutsidwa. Ampatuko, atsogoleli a cipembedzo, komanso andale, amakamba mabodza ponena za nchito yathu. Acibale athu, anthu amene timadziŵa, ndiponso anzathu a kunchito akauzidwa mabodza amenewo, amatikakamiza kuti tileke kutumikila Yehova komanso kulalikila. M’maiko ena, citsutso cimabwela m’njila zosiyana-siyana monga kuopsezedwa, kumangidwa, ngakhale kuponyedwa m’ndende kumene. Koma ife sitidabwa na zimenezi, cifukwa Yesu anakambilatu kuti: “Mitundu yonse idzadana nanu cifukwa ca dzina langa.” (Mat. 24:9) Kuzondewa kumeneko ni umboni wakuti Yehova akutiyanja. (Mat. 5: 11, 12) Mdyerekezi ndiye amapangitsa kuti tizitsutsidwa. Koma iye alibe mphamvu tikamuyelekezela na Yesu. Mothandizidwa na Yesu, uthenga wabwino ukufalikila kwa anthu a mitundu yonse. Tiyeni tione umboni wa zimenezi.

7. Kodi mukuona umboni wotani wotsimikizila kuti Chivumbulutso 14: 6, 7 ikukwanilitsidwa?

7 Pokhala alengezi a Ufumu, vuto lina limene timakumana nalo ni kusiyana kwa zinenelo. M’masomphenya amene mtumwi Yohane anaonetsedwa, Yesu analosela kuti kusiyana kwa zinenelo sikudzalepheletsa uthenga wabwino kulalikidwa. (Ŵelengani Chivumbulutso 14: 6, 7.) Masiku ano, tikupeleka mwayi kwa anthu oculuka womvetsela uthenga wa Ufumu. Anthu padziko lonse angaŵelenge mabuku na nkhani zozikidwa pa Baibo, pa webusaiti yathu ya jw.org cifukwa zimapezeka m’zinenelo zoposa 1,000. Cilolezo cinapelekedwa cakuti buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! limasulidwe. Bukuli ndilo cida cacikulu cotithandiza pa nchito yopanga ophunzila, ndipo lipezeka m’zinenelo zoposa 700. Cakudya cauzimu cimapezekanso m’mavidiyo okonzedwela anthu osakhoza kumva, komanso zofalitsa za anthu osaona. Inde, tikuona kukwanilitsidwa kwa maulosi a m’Baibo. Anthu a “m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina,” amakamba “cilankhulo coyela” ca coonadi ca m’Baibo. (Zek. 8:23; Zef. 3:9) Zonsezi zikucitika cifukwa ca uyang’anilo wabwino wa Yesu Khristu.

8. Kodi pakhala zotulukapo zotani pa nchito yathu yolalikila?

8 Masiku ano, anthu oposa 8,000,000 m’maiko 240 ali m’gulu la Yehova, ndipo caka ciliconse anthu masauzande amabatizika. Komabe, cofunika kwambili si ciŵelengelo, koma makhalidwe acikhristu, inde “umunthu watsopano” umene ophunzila atsopano amenewo akhala nawo. (Akol. 3:8-10) Ambili analeka makhalidwe oipa monga ciwelewele, ciwawa, tsankho, na mzimu wa ‘konda dziko lako.’ Ulosi wa pa Yesaya 2:4 wakuti “sadzaphunzilanso nkhondo” ukukwanilitsidwa. Tikamayesetsa kuvala umunthu watsopano, timakopa anthu kuti abwele m’gulu la Mulungu, komanso timaonetsa kuti tikutsatila wotiyang’anila wathu, Khristu Yesu. (Yoh. 13:35; 1 Pet. 2:12) Zimenezi sizicitika mwangozi. Yesu ndiye akutipatsa thandizo lofunikila.

YESU ANASANKHA KAPOLO

9. Malinga n’kunena kwa Mateyu 24:45-47, kodi Yesu analosela ciyani ponena za nthawi ya mapeto?

9 Ŵelengani Mateyu 24:45-47. Yesu analosela kuti m’nthawi ya mapeto, adzaika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azipeleka cakudya cauzimu. Conco, timayembekezela kapolo ameneyo kugwila nchito molimbika m’masiku athu ano. Ndipo izi n’zimenedi iye akucita. Wotiyang’anila ameneyu, akugwilitsa nchito kagulu kocepa ka abale odzozedwa popeleka “cakudya [cauzimu] pa nthawi yoyenela” kwa anthu a Mulungu, komanso acidwi. Amuna amenewa sadziona kuti ni olamulila cikhulupililo ca ena. (2 Akor. 1:24) M’malo mwake, iwo amadziŵa kuti Yesu Khristu ndiye “mtsogoleli ndi wolamulila” anthu ake.—Yes. 55:4.

Zithunzi: Mabuku osiyana-siyana amene agwilitsidwa nchito kwa zaka zambili pophunzitsa Baibo anthu acidwi. 1. 1946: “Mulungu Akhale Woona.” Mlongo akugaŵila buku mu ulaliki. 2. 1968: “Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya.” Munthu akuŵelenga buku kunyumba kwake. 3. 1982: “Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha M’paradaiso pa Dziko Lapansi.” M’bale akutsogoza phunzilo la Baibo. 4. 1995: “Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.” M’bale akuphunzila Baibo na mnzake wa kunchito panthawi yopumula. 5. 2005 komanso 2015: Buku lakuti “Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni,” komanso lakuti “Zimene Baibulo Ingatiphunzitse.” Mlongo akutsogoza phunzilo la Baibo. 6. 2021: “Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!” Mlongo akutsogoza phunzilo la Baibo kupitila pa vidiyo.

10. Pa mabuku ali pa cithunzipa, ni buku liti linakuthandizani kuyamba kuyenda panjila ya ku moyo wosatha?

10 Kungoyambila mu 1919, kapolo wokhulupilika ameneyu wakhala akukonza zofalitsa zosiyana-siyana zimene zathandiza anthu acidwi kuphunzila coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Mu 1921, kapoloyu anatulutsa buku lakuti Zeze wa Mulungu, pofuna kuthandiza anthu acidwi kuphunzila Baibo. M’kupita kwa nthawi, panatulutsidwanso mabuku ena. Ni buku liti linakuthandizani kudziŵa Atate wathu wakumwamba na kuyamba kum’konda? Kodi ni buku lakuti “Mulungu Akhale Woona,” Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha M’paradaiso pa Dziko Lapansi, Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, kapena ni buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! limene langotuluka posacedwa? Mabuku onsewa anakonzedwa kuti atithandize pa nchito yopanga ophunzila, ndipo anali ofunika panthawi imene anali kutulutsidwa.

11. N’cifukwa ciyani tonsefe tiyenela kulandila cakudya cauzimu?

11 Si anthu acidwi okha amene afunikila cakudya cotafuna cauzimu. Tonsefe timafunikila cakudyaci. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Cakudya cotafuna ndi ca anthu okhwima mwauzimu.” Iye anakambanso kuti kugwilitsa nchito zimene timaphunzila m’Baibo kudzatithandiza “kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.” (Aheb. 5:14) M’nthawi yovuta ino pamene makhalidwe abwino akuloŵela-loŵela pansi, cingakhale covuta kumamatila mfundo za Yehova. Koma Yesu amaonetsetsa kuti cakudya cauzimu cokoma cimene timadya cikulimbitsa cikhulupililo cathu. Cakudya cauzimu cimeneci cimazikika pa Mawu a Mulungu ouzilidwa, Baibo. Kapolo wokhulupilika ameneyu amakonza na kupeleka cakudyaci motsogololedwa na Yesu.

12. Mofanana na Yesu, kodi timalilemekeza bwanji dzina la Mulungu?

12 Mofanana na Yesu, timalemekeza dzina la Mulungu. (Yoh. 17:6, 26) Mwacitsanzo, mu 1931 tinatenga dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova. Kudziŵika na dzina limeneli kumatipangitsa kuyandikana kwambili na Atate wathu wakumwamba. (Yes. 43:10-12) Ndipo kucoka mu October caka cimeneco, dzina la Mulungu lakhala likuonekela pa cikuto cakumaso ca magazini iliyonse ya Nsanja ya Mlonda. Kuwonjezela apo, mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, dzina la Mulungu linabwezeletsedwa pamalo ake oyenelela. Zimenezi n’zosiyana kwambili na Machalichi Acikristu, amene acotsa dzina lakuti Yehova m’ma Baibo ambili amene iwo anamasulila.

YESU ANAKONZEKELETSA OTSATILA AKE

13. N’ciyani cimakupangitsani kutsimikiza kuti Yesu akugwilitsa nchito “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” masiku ano? (Yohane 6:68)

13 Kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” Yesu anakhazikitsa gulu lapadela padziko lapansi limene limalimbikitsa kulambila koyela. Kodi mumamva bwanji kukhala m’gulu limeneli? Poyankha funsoli, mwina mwakumbukila mawu a mtumwi Petulo, amene anauza Yesu kuti: “Tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:68) Kodi umoyo wathu ukanakhala bwanji pali pano sembe kuti sitinabwele m’gulu la Yehova? Kupitila m’gulu limeneli, Yesu amaonetsetsa kuti tikudyetsedwa bwino kuuzimu. Iye amatiphunzitsanso mocitila bwino utumiki wathu. Cina, amatithandiza kuvala “umunthu watsopano” kuti tikondweletse Yehova.—Aef. 4:24.

14. Kodi mwapindula bwanji cifukwa cokhala m’gulu la Yehova panthawi ya mlili wa COVID-19?

14 Yesu amapeleka citsogozo canzelu panthawi yovuta. Ubwino wa citsogozo cimeneco tinauona pamene mlili wa COVID-19 unayamba. Pamene anthu m’dzikoli anasoŵa mtengo wogwila, Yesu anaonetsetsa kuti talandila malangizo omveka bwino kuti tikhale otetezeka. Tinauzidwa kuti tizivala mamasiki tikakhala pagulu, komanso kuti tizikhala motalikilana. Ndipo akulu anakumbutsidwa kuti ayenela kumakambilana na aliyense mu mpingo nthawi zonse, kuti adziŵe umoyo wawo wakuthupi komanso wauzimu. (Yes. 32:1, 2) Tinayambanso kulandila citsogozo na cilimbikitso kupitila m’ziunikilo za Bungwe Lolamulila.

15. Kodi tinalandila malangizo otani a mocitila misonkhano komanso ulaliki mlili utayamba? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

15 Mliliwu utayamba, tinalandilanso malangizo omveka bwino a mocitila misonkhano ya mpingo na ulaliki. Mwamsanga ndithu, tinayamba kucita misonkhano ya mpingo, yadela, komanso yacigawo kupitila pa vidiyo. Cina, tinayamba kucita kwambili ulaliki wa makalata komanso wa pafoni. Yehova anadalitsa khama lathu. Malipoti a maofesi ambili a nthambi aonetsa kuti ciŵelengelo ca ofalitsa cawonjezeka kwambili. Ndipo ambili anakhala na zocitika zolimbikitsa za mu ulaliki panthawi ya mliliwu.—Onani bokosi lakuti, “Yehova Akudalitsa Nchito Yathu Yolalikila.”

Yehova Akudalitsa Nchito Yathu Yolalikila

  • Banja lina la ku Central America lakhala ku Europe zaka zoposa 15. Mlili utayamba, banjali linaganiza zoyamba kulalikila acibale awo, na anthu ena amene anali kuwadziŵa kwawo ku Central America. Kuti akwanitse kuwalalikila, iwo anatumiza makalata oposa 200 pa intaneti. Anacita maulendo obwelelako na kutumiza zofalitsa komanso malinki a mavidiyo kwa aja anaonetsa cidwi. Yehova anadalitsa khama lawo, moti pa miyezo 8 cabe, banjalo linali kutsogoza maphunzilo a Baibo 14!

  • Mu November 2020, pamene tinali kucita kampeni yogaŵila Nsanja ya Mlonda yakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?,” m’bale wina anaganiza zotumila foni mnzake amene anali kuphunzila naye pa sukulu. Mnzakeyo analandila magaziniyo, ndipo anagwilizana kuti akaikambilane na m’baleyo mlungu wotsatila. Pokambilana pa ulendo wobwelelako, mnzakeyo anati: “Usanan’tumile foni, n’nali n’tapemphela kwa Mulungu kuti anithandize kudziŵa zimene iye afuna kuti nizicita.” Iye anavomela kuphunzila Baibo, anayamba kupezeka pa misonkhano, na kuseŵenzetsa zimene anali kuphunzila. Patapita nthawi, iye anauza m’baleyo kuti: “Kale, n’nali kuona kuti cina cake cikusoŵa mu umoyo wanga. Tsopano nadziŵa kuti cosoŵaco cinali Yehova. Tsiku lililonse nimakuyamikila ponithandiza kuyandikana naye.”

16. Kodi ndife otsimikiza za ciyani?

16 Mwina ena anali kuona kuti gulu lathu likukhwimitsa kwambili zinthu panthawi ya mliliwu. Koma nthawi zonse, zinali kuonekelatu kuti malangizo amene talandila ni anzelu. (Mat. 11:19) Ndipo tikamaganizila mmene Yesu amatsogolela anthu ake mwacikondi, timakhala otsimikiza kuti kaya tikumane na zotani kutsogoku, Yehova na Mwana wake wokondeka adzakhalabe nafe.—Ŵelengani Aheberi 13:5, 6.

17. Kodi mumamva bwanji kugwila nchito moyang’anilidwa na Yesu?

17 Ha, ni dalitso lalikulu cotani nanga kugwila nchito moyang’anilidwa na Yesu! Tili m’gulu logwilizana ngakhale kuti timasiyana zikhalidwe, maiko, na zinenelo. Timadyetsedwa bwino kuuzimu, komanso timaphunzitsidwa kuti tigwile bwino nchito yolalikila. Ndipo aliyense payekha amathandizidwa kuvala umunthu watsopano, komanso timaphunzila kukondana. Conco, ndife onyadila kuti tili na Yesu monga wotiyang’anila.

N’CIYANI CIMAKUPANGITSANI KUTSIMIKIZA KUTI YESU NDIYE . . .

  • akuyang’anila nchito yolalikila padziko lonse?

  • akupeleka citsogozo kwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” pokonza cakudya cauzimu?

  • akutsogolela otsatila ake panthawi yovuta?

NYIMBO 16 Tamandani Mwana Wodzozedwa wa Ya

a Padziko lonse lapansi, mamiliyoni a anthu ophatikizapo amuna, akazi, ndiponso ana akulalikila uthenga wabwino mokangalika. Kodi ndinu mmodzi wa iwo? Ngati n’telo, ndiye kuti mukugwila nchito pansi pa uyang’anilo wa Ambuye wathu, Yesu Khristu. M’nkhani ino, tikambilane umboni woonetsa kuti Yesu ndiye akutsogolela nchito yolalikila masiku ano. Tikamaiganizila mfundo imeneyi, tidzakhala ofunitsitsa kum’tumikilabe Yehova motsogoleledwa na Khristu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani