NKHANI YOPHUNZILA 36
Anthu a Yehova Amakonda Cilungamo
“Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu la cilungamo.”—MAT. 5:6.
NYIMBO 9 Yehova Ndiye Mfumu Yathu!
ZIMENE TIKAMBILANEa
1. Kodi Yosefe anakumana na mayeso otani? Nanga anacita ciyani?
YOSEFE mwana wa Yakobo anakumana na mayeso ovuta. Mkazi wa mbuye wake Potifara anali kumuuza kuti: “Ugone nane.” Koma Yosefe anali kukana. Ena angafunse kuti, Kodi n’ciyani cinam’thandiza Yosefe kuti asagonje ku mayeselo amenewo? Potifara anali atacokapo. Kuwonjezela apo, Yosefe anali kapolo m’nyumba ya Mbuye wake. Conco akanakana pempho lake, mkaziyo akanamuvutitsa kwambili Yosefe. Koma Yosefe anali kukana pamene mkaziyo anali kumukakamiza mobweleza-bweleza kuti agone naye. Cifukwa ciyani? Iye anati: “Ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?”—Gen. 39:7-12.
2. Kodi Yosefe anadziŵa bwanji kuti kucita cigololo n’kucimwila Mulungu?
2 Kodi Yosefe anadziŵa bwanji kuti Mulungu wake anali kuona kuti cigololo ni “coipa cacikulu”? Cilamulo ca Mose, cimene cinaphatikizapo lamulo lomveka bwino lakuti “usacite cigololo” cinali cisanalembedwe kufikila patapita zaka pafupifupi 200. (Eks. 20:14) Koma Yosefe anali kudziŵa bwino kuti Yehova amadana nalo kwambili khalidwe laciwelewele. Mwacitsanzo, Yosefe anali kudziŵa kuti Yehova anakonza zakuti ukwati uzikhala pakati pa mwamuna mmodzi na mkazi mmodzi. Ndipo ayenelanso kuti anamva kuti kaŵili konse, Yehova anateteza Sara ambuye ŵake kuti asacitidwe zaciwelewele. Mofananamo, Mulungu anateteza Rabeka, mkazi wa Isaki. (Gen. 2:24; 12:14-20; 20:2-7; 26:6-11) Yosefe poganizila nkhani ngati zimenezi, anadziŵa cimene cinali coyenela komanso cosayenela pamaso pa Mulungu. Cifukwa cokonda Mulungu wake, Yosefe anali kukondanso malamulo olungama a Yehova, ndipo anali wofunitsitsa kuwatsatila.
3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?
3 Kodi inu cilungamo mumacikonda? Mosakayika konse. Koma popeza kuti tonse ndife opanda ungwilo, ngati sitingasamale tingayambe kuona cilungamo mmene dzikoli limacionela. (Yes. 5:20; Aroma 12:2) Conco, tikambilane kuti cilungamo n’ciyani, komanso mmene timapindulila tikamakonda cilungamo. Kenako, tikambilane masitepe atatu amene tingatenge kuti tizikonda kwambili malamulo a Yehova.
KODI CILUNGAMO N’CIYANI?
4. Ni maganizo olakwika ati amene anthu ambili ali nawo pa nkhani ya cilungamo?
4 Anthu ambili amaganiza kuti munthu wolungama ni munthu wonyada, wokonda kuweluza ena, kapena amene amadziona kuti ni wocita bwino kwambili kuposa ena. Koma Mulungu sakondwela nawo makhalidwe amenewa. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anadzudzula mwamphamvu atsogoleli acipembedzo cifukwa cokhazikitsa malamulo awo-awo pa nkhani ya cilungamo. (Mlal. 7:16; Luka 16:15) Munthu amene amacita zimene Yehova amati n’zoyenela, saona kuti amacita bwino kuposa ena.
5. Kodi Baibo imati cilungamo n’ciyani? Fotokozani zitsanzo.
5 Cilungamo ni khalidwe labwino ngako. Mwacidule, tingati cilungamo cimatanthauza kucita zoyenela pamaso pa Yehova Mulungu. M’Baibo, mawu otanthauzila “cilungamo” amapeleka lingalilo la kutsatila mfundo zapamwamba kwambili za Yehova. Mwacitsanzo, Yehova analamula kuti amalonda azigwilitsa nchito “muyezo . . . woyenela.” (Deut. 25:15) Mawu oyambilila a Ciheberi amene anawamasulila kuti “woyenela,” angatanthauzenso kuti “wolungama.” Conco, Mkhristu amene amafuna kukhala wolungama pamaso pa Mulungu, ayenela kukhala woona mtima pocita malonda ake. Munthu wokonda cilungamo sakondwela ena akamacitidwa zinthu mopanda cilungamo. Ndipo kuti ‘azikondweletsa [Yehova] pa ciliconse,’ munthu wolungama zenizeni amaganizila mmene Mulungu amaonela zisankho zake.—Akol. 1:10.
6. N’cifukwa ciyani ndife otsimikiza kuti Yehova ndiye woyenela kuika malamulo a coyenela na cosayenela? (Yesaya 55:8, 9)
6 Baibo imafotokoza kuti Yehova ndiye Gwelo la cilungamo. Mpake kuti iye amachedwa “malo okhalamo cilungamo.” (Yer. 50:7) Pokhala Mlengi, Yehova ndiye yekha ali na ufulu woika malamulo a coyenela na cosayenela. Popeza Yehova ni wangwilo, amadziŵa bwino-bwino coyenela na cosayenela. Koma kwa ife n’covuta kudziŵa coyenela na cosayenela cifukwa ndife ocimwa komanso opanda ungwilo. (Miy. 14:12; ŵelengani Yesaya 55:8, 9) Komabe, cifukwa tinapangidwa m’cifanizilo ca Mulungu, timatha kutsatila malamulo ake olungama pa umoyo wathu. (Gen. 1:27) Ndipo timakondwela kucita zimenezo. Kukonda Atate wathu kumatilimbikitsa kutengela citsanzo cake mmene tingathele.—Aef. 5:1.
7. N’cifukwa ciyani timafunika malamulo okhazikitsidwa? Fotokozani citsanzo.
7 Timapindula tikamatsatila malamulo a Yehova a cabwino na coipa. Kodi mudziŵa cifukwa cake? Tangoganizilani zimene zingacitike banki iliyonse itadziikila malamulo ake-ake okhudza mphamvu ya ndalama. Pakanakhala msokonezo wokha-wokha. Kapena, ngati azacipatala akulephela kutsatila malangizo popeleka cithandizo kwa odwala, odwala ena angamwalile. N’zoonekelatu kuti malamulo okhazikitsidwa amateteza. Mofananamo, malamulo a Mulungu a cabwino na coipa amatiteteza.
8. Kodi okonda kucita zacilungamo adzalandila madalitso otani?
8 Yehova amadalitsa anthu amene amayesetsa kutsatila malamulo ake. Iye analonjeza kuti: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:29) Tangoganizilani mmene anthu adzakhalile ogwilizana, a mtendele, komanso acimwemwe pamene aliyense azidzatsatila malamulo a Yehova! Iye amafuna kuti mukasangalale na umoyo umenewo. Kukamba zoona, aliyense wa ife ali na zifukwa zabwino zokondela cilungamo. Ndiye tingacite ciyani kuti tizilikonda kwambili khalidwe limeneli? Tiyeni tikambilane masitepe atatu amene tingatenge.
TIZIWAKONDA KWAMBILI MALAMULO A YEHOVA
9. N’ciyani cingatithandize kuti tizikonda cilungamo?
9 Sitepe yoyamba: Tizikonda amene anaika malamulo. Kuti tizikonda cilungamo, tiyenela kukulitsa cikondi cathu pa uyo amene anapanga malamulo a cabwino na coipa. Tikamam’konda kwambili Yehova, timakhala ofunitsitsa kwambili kutsatila malamulo ake olungama. Mwacitsanzo, Adamu na Hava akanakonda kwambili Yehova, sakanaphwanya lamulo lake.—Gen. 3:1-6, 16-19.
10. Kodi Abulahamu anacita ciyani kuti adziŵe kaganizidwe ka Yehova?
10 Sitifuna olo pang’ono kucita zinthu monga anacitila Adamu na Hava. Tingapewe zotsatilapo zoipa za kusamvela malamulo mwa kupitiliza kuphunzila za Yehova, kutengela makhalidwe ake, na kuyesetsa kudziŵa kaganizidwe kake. Tikatelo, cikondi cathu pa Yehova cidzakula. Ganizilani za Abulahamu. Iye anali kum’kondadi Yehova. Ngakhale pamene iye sanamvetse zisankho za Yehova, Abulahamu sanapanduke. M’malo mwake, anayesetsa kum’dziŵa bwino Yehova. Mwacitsanzo, iye atadziŵa kuti Yehova afuna kuwononga mizinda ya Sodomu na Gomora, poyamba anada nkhawa kuti “Woweluza wa dziko lonse lapansi” adzawononga olungama pamodzi na oipa. Abulahamu anaona kuti kucita zimenezo si cilungamo. Conco, modzicepetsa anafunsa Yehova mafunso ambili. Ndipo Yehova anamuyankha moleza mtima. Potsilizila pake, Abulahamu anazindikila kuti Yehova amasanthula mtima wa munthu aliyense, komanso kuti iye sangalange anthu abwino pamodzi na oipa.—Gen. 18:20-32.
11. Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kum’konda Yehova na kum’khulupilila?
11 Abulahamu anakhudzika mtima kwambili na makambilano amene anali nawo na Yehova okhudza mizinda ya Sodomu na Gomora. Ndipo n’kutheka kuti makambilanowo anamupangitsa kukonda kwambili Atate wake, na kum’lemekeza kuposa kale. Patapita zaka zambili, kukhulupilila kwake Yehova kunaikidwa pa mayeso aakulu. Yehova anam’pempha kuti apeleke nsembe Isaki, mwana wake yekhayo wapamtima pake. Koma panthawiyi, Abulahamu anali atamudziŵa bwino Mulungu wake, moti sanamufunse mafunso. Iye anangocita zimene Yehova anam’pempha. Tangoganizani cisoni cimene anali naco mumtima pokonzekela kukapeleka mwana wake nsembe. Abulahamu ayenela kuti anaganizila mozama zimene anali ataphunzila ponena za Yehova. Iye anadziŵa kuti Yehova sangacite zinthu mopanda cilungamo kapena mopanda cikondi. Malinga n’zimene mtumwi Paulo analemba, Abulahamu anadziŵa kuti Yehova adzamuukitsa Isaki mwana wake wokondekayo. (Aheb. 11:17-19) Ndi iko komwe, Yehova anali atalonjeza kuti Isaki adzakhala tate wa mitundu ya anthu. Koma panthawiyo, iye analibe ana. Abulahamu anali kum’konda Yehova. Conco anakhulupilila kuti Atate wake adzacita zinthu mwacilungamo. Mwa cikhulupililo iye anamvela, ngakhale kuti cinali covuta kutelo.—Gen. 22:1-12.
12. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Abulahamu? (Salimo 73:28)
12 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Abulahamu? Mofanana na iye, tiyenela kupitiliza kuphunzila za Yehova. Tikatelo, tidzamuyandikila kwambili, komanso tidzamukonda kwambili. (Ŵelengani Salimo 73:28.) Cina, cikumbumtima cathu cidzaphunzitsidwa kuona zinthu mmene Mulungu amazionela. (Aheb. 5:14) Zotulukapo n’zakuti, wina akatisonkhezela kucita zinthu zoipa tidzakana. Tidzapewa ngakhale kuganizila zocita ciliconse cimene cingakhumudwitse Atate wathu, na kuwononga ubale wathu na iye. N’ciyani cina cimene tingacite kuti tionetse kuti timakonda cilungamo?
13. Kodi tingatani kuti tikhale anthu ocita zacilungamo? (Miyambo 15:9)
13 Sitepe yaciŵili: Tiziyesetsa kukonda cilungamo tsiku na tsiku. Ngati munthu afuna kulimbitsa thupi lake, amafunika kucita maseŵela olimbitsa thupi mwakhama. Mofananamo, kukonda malamulo a Yehova olungama kumafuna khama, ndipo n’kosavuta. Yehova amatiganizila, ndipo satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse. (Sal. 103:14) Iye amatitsimikizila kuti “amakonda munthu wocita cilungamo.” (Ŵelengani Miyambo 15:9.) Tikadziikila colinga mu utumiki wa Yehova, timayesetsa kuti ticikwanilitse. N’cimodzimodzinso ngati tikufuna kukhala anthu ocita zacilungamo. Ndipo Yehova adzatithandiza moleza mtima kuti pang’ono-m’pang’ono tikulitse khalidwe limeneli.—Sal. 84:5, 7.
14. Kodi “codzitetezela pacifuwa cacilungamo” n’ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani n’cofunika kwambili?
14 Mwa cikondi cake, Yehova amatikumbutsa kuti kucita cilungamo si kolemetsa. (1 Yoh. 5:3) M’malo mwake, kumatiteteza, ndipo timafunikila citetezo cimeneco tsiku lililonse. Kumbukilani zida zankhondo zauzimu zimene mtumwi Paulo anafotokoza. (Aef. 6:14-18) Kodi ni cida citi cimene cinali kuteteza mtima wa msilikali? Cinali “codzitetezela pacifuwa cacilungamo,” cimene cimaimila malamulo a Yehova olungama. Monga mmene codzitetezela pacifuwa cacilungamo cimatetezela mtima weniweniwo, nawonso malamulo a Yehova olungama amateteza mtima wathu wophiphilitsa, umene ni umunthu wathu wamkati. Conco pa zida zathu zankhondo, tizionetsetsa kuti tavalanso codzitetezela pacifuwa cacilungamo.—Miy. 4:23.
15. Kodi tingavale motani codzitetezela pacifuŵa cacilungamo?
15 Kodi tingavale motani codzitetezela pacifuŵa cacilungamo? Tingacite zimenezo mwa kuganizila zimene Mulungu amafuna kuti ticite pa zisankho zimene timapanga tsiku lililonse. Posankha zokamba, nyimbo, zosangalatsa zimene tifuna kutamba, kapena mabuku oŵelenga, coyamba tizidzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zidzanikhudza bwanji? Kodi Yehova amakondwela nazo? Kapena kodi zimalimbikitsa zaciwelewele, ciwawa, dyela, kudzikonda—zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zosalungama?’ (Afil. 4:8) Ngati zisankho zathu zimagwilizana na cifunilo ca Yehova, ndiye kuti malamulo ake olungama adzateteza mtima wathu.
Cilungamo cathu cidzakhala “ngati mafunde a m’nyanja” (Onani ndime 16-17)
16-17. Kodi Yesaya 48:18 imatitsimikizila bwanji kuti n’zotheka kutsatila malamulo a Yehova kwamuyaya?
16 Kodi mumada nkhawa kuti simudzapitiliza kutsatila malamulo a Yehova olungama tsiku lililonse kapena caka ciliconse? Onani citsanzo ici cimene Yehova anagwilitsa nchito, copezeka pa Yesaya 48:18. (Ŵelengani.) Yehova analonjeza kuti cilungamo cathu cidzakhala “ngati mafunde a m’nyanja.” Yelekezani kuti mwaimilila m’mbali mwa nyanja, ndipo mukuona mafunde akugavila mosalekeza. Kodi mumada nkhawa kuti tsiku lina mafunde amenewo adzaleka kugavila? Iyai. Mumadziŵa kuti mafundewo akhala akugavila m’mbali mwa nyanjayo kwa zaka zambili, ndipo sadzaleka.
17 Mofananamo, cilungamo cathu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja. Motani? Mukafuna kupanga cisankho, coyamba muziganizila zimene Yehova amafuna kuti mucite. Ndiyeno, citani zimenezo. Kaya cisankhoco n’cakulu motani, Atate wathu wacikondi adzatithandiza kuimabe nji, komanso kuti tizitsatilabe malamulo ake olungama tsiku lililonse.—Yes. 40:29-31.
18. N’cifukwa ciyani sitiyenela kuweluza ena?
18 Sitepe yacitatu: Tizilola Yehova kuweluza. Pamene tikuyesetsa kutsatila malamulo a Yehova olungama, tizipewa kuweluza ena na kudziona kukhala olungama. M’malo mokonda kuweluza anthu anzathu, tizikumbukila kuti Yehova ndiye “Woweluza wa dziko lonse lapansi.” (Gen. 18:25) Yehova sanatipatse udindo woweluza ena. Ndiye cifukwa cake Yesu anati: “Lekani kuweluza ena kuti inunso musaweluzidwe.”—Mat. 7:1.b
19. Kodi Yosefe anasiya kuweluza konse m’manja mwa Yehova motani?
19 Tiyeni tikambilanenso za Yosefe munthu wolungama. Iye anapewa kuweluza ena, ngakhale anthu amene anam’cita zoipa. Abale ake enieniwo anamuukila, anamugulitsa ku ukapolo, ndipo anaonetsa atate awo umboni wakuti Yosefe wamwalila. Patapita zaka, Yosefe anakumananso na banja lake. Panthawiyo, iye anali wolamulila wamphamvu, ndipo akanaweluza abale akewo mwankhaza pofuna kuwabwezela. Abale ake a Yosefe anaopa kuti mwina adzawacita zimenezo, ngakhale kuti panthawiyi iwo anali atalapa pa zimene anacita. Koma Yosefe anawauza kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu?” (Gen. 37:18-20, 27, 28, 31-35; 50:15-21) Modzicepetsa, Yosefe anasiila Yehova kuti aweluze abale akewo.
20-21. Kodi tingapewe bwanji kudziona kuti ndife olungama?
20 Mofanana na Yosefe, ifenso kuweluza timakusiya m’manja mwa Yehova. Mwacitsanzo, tiyenela kupewa kuwaganizila zolinga zoipa abale na alongo athu akacita zinthu mwa njila ina yake. Ife singadziŵe za mu mtima mwa munthu, koma “Yehova [yekha ndiye] amafufuza zolinga zake.” (Miy. 16:2) Iye amakonda anthu onse, mosasamala kanthu za cikhalidwe cawo. Ndipo Yehova amatilimbikitsa ‘kufutukula mtima wathu.’ (2 Akor. 6:13) Conco, tiziyesetsa kuwakonda abale na alongo athu, osati kuwaweluza.
21 Izi zitanthauzanso kuti sitiyenela kuweluza ngakhale anthu amene si Mboni. (1 Tim. 2:3, 4) Kodi mungaweluze wacibale wanu amene si Mboni, n’kunena kuti, “Amene uja sangaphunzile coonadi”? Ayi, kucita zimenezo kungakhale kudzikuza, kapena kudziona wolungama. Yehova akupatsabe “anthu kwina kulikonse” mwayi wakuti alape. (Mac. 17:30) Nthawi zonse tizikumbukila kuti tikamadziona olungama, ndiye kuti ndife osalungama.
22. N’cifukwa ciyani tiyenela kuyesetsa kukonda cilungamo?
22 Ngati timakonda malamulo a Yehova olungama, tidzakhala acimwemwe komanso citsanzo cabwino kwa ena. Izi zidzathandiza kuti atikonde komanso kuti ayandikile kwambili Mulungu. Conco tisaleke ‘kumva njala na ludzu la cilungamo.’ (Mat. 5:6) Dziŵani kuti Yehova amakondwela tikamayesetsa kucita cilungamo. Pamene anthu m’dzikoli akupitila-pitila pa kucita zosalungama, tisataye mtima. Nthawi zonse tizikumbukila kuti “Yehova amakonda anthu olungama.”—Sal. 146:8.
NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano
a N’kovuta kupeza anthu acilungamo m’dziko loipali. Ngakhale n’telo, masiku ano pali anthu mamiliyoni amene akutsatila njila yacilungamo. Ndipo sitikukayika kuti ndinu mmodzi wa iwo. Mumatsatila njila ya cilungamo cifukwa mumakonda Yehova, amene amakonda cilungamo. Kodi tingacite ciyani kuti tizilikonda kwambili khalidwe labwino limeneli? M’nkhani ino, tione kuti cilungamo n’ciyani, komanso mmene timapindulila tikamacikonda cilungamo. Tikambilanenso masitepe amene tingatenge kuti tizilikonda kwambili khalidwe limeneli.
b Nthawi zina, akulu mu mpingo amaweluza nkhani zokhudza macimo aakulu komanso kulapa. (1 Akor. 5:11; 6:5; Yak. 5:14, 15) Komabe, modzicepetsa iwo amakumbukila kuti sangadziŵe za mu mtima mwa munthu, ndiponso kuti akuweluzila Yehova. (Yelekezelani na 2 Mbiri 19:6.) Iwo mosamala amapanga zigamulo motsatila cifundo ca Mulungu na mfundo zake zolungama.