LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 March masa. 8-13
  • Pitilizani Kutsatila Yesu Pambuyo pa Ubatizo Wanu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pitilizani Kutsatila Yesu Pambuyo pa Ubatizo Wanu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • PITILIZANI KUTSATILA YESU OLO MUKUMANE NA MAYESO, NGAKHALE MAYESELO
  • ZIMENE MUNGACITE KUTI MUPITILIZE KUMUTSATILA YESU
  • “PITILIZANI KUDZIYESA”
  • Kodi Ndinu Wokonzeka Kudzipatulila kwa Yehova?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 March masa. 8-13

NKHANI YOPHUNZILA 10

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

Pitilizani Kutsatila Yesu Pambuyo pa Ubatizo Wanu

“Ngati munthu akufuna kunditsatila, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikilapo tsiku ndi tsiku ndi kunditsatila mosalekeza.”—LUKA 9:23.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Nkhani ino itithandiza kuona mmene kudzipatulila kwathu kwa Yehova kumakhudzila umoyo wathu. Koma idzathandiza maka-maka amene anabatizika caposacedwa kuti apitilize kukhala okhulupilika.

1-2. Kodi munthu akabatizika amapeza madalitso otani?

NI CINTHU cokondweletsa ngako kubatizika na kuloŵa m’banja la Yehova! Awo amene ali kale m’banja limeneli angavomeleze zimene wamasalimo Davide analemba kuti: “Wodala ndi munthu amene inu [Yehova] mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu, kuti akhale m’mabwalo anu.”—Sal. 65:4.

2 Yehova samangotenga munthu aliyense n’kumuloŵetsa m’mabwalo ake. Monga tinaonela m’nkhani yapita, iye amayandikila anthu amene amaonetsa kuti akufunadi kukhala naye pa ubale wabwino. (Yak. 4:8) Mukadzipatulila kwa Yehova na kubatizika, mumamuyandikila m’njila yapadela. Dziŵani kuti pambuyo pake iye ‘adzakukhutulilani madalitso oti mudzasoŵa powalandilila.’—Mal. 3:10; Yer. 17:​7, 8.

3. Ni udindo waukulu uti umene Akhristu amene anadzipatulila na kubatizika ali nawo? (Mlaliki 5:​4, 5)

3 Komabe, ubatizo ni poyambila cabe. Mukatenga sitepe imeneyi, mudzafuna kucita zonse zotheka kuti musunge lumbilo la kudzipatulila kwanu. Mudzacita zimenezi olo mutakumana na mayeselo, ngakhale mayeso. (Ŵelengani Mlaliki 5:​4, 5.) Monga wophunzila wa Yesu, muyenela kutsatila citsanzo cake na malamulo ake mosamala kwambili. (Mat. 28:​19, 20; 1 Pet. 2:21) Nkhani ino ikuthandizani kuona mmene mungacitile zimenezi.

PITILIZANI KUTSATILA YESU OLO MUKUMANE NA MAYESO, NGAKHALE MAYESELO

4. Kodi ophunzila a Yesu amanyamula “mtengo . . . wozunzikilapo” m’lingalilo lotani? (Luka 9:23)

4 Mukabatizika sikuti mudzakhala na umoyo wopanda mavuto ayi. Ndipo Yesu ananena momveka bwino kuti ophunzila ake adzanyamula “mtengo . . . wozunzikilapo.” Ndipo adzacita zimenezi “tsiku ndi tsiku.” (Ŵelengani Luka 9:23.) Kodi Yesu anali kutanthauza kuti otsatila ake azingokhalila kuvutika? Kutali-tali. Iye anali kugogomeza mfundo yakuti kuwonjezela pa madalitso omwe ophunzila ake anali kudzapeza, adzakumananso na zokhoma. Zina mwa zokhoma zimenezi zimakhala zoŵaŵa zedi.—2 Tim. 3:12.

5. Kodi Yesu anawalonjeza ciyani anthu amene adzimana zinazake?

5 Mwina acibale anu akukutsutsani, kapena munasiya zolinga zanu za kuthupi kuti muike za Ufumu patsogolo pa umoyo wanu. (Mat. 6:33) Ngati n’telo, dziŵani kuti Yehova amaona nchito za kukhulupilika kwanu. (Aheb. 6:10) Mwacionekele, mwapeza madalitso amene Yesu anachula ponena kuti: “Palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda cifukwa ca ine, ndi cifukwa ca uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, limodzi ndi mazunzo, ndipo m’nthawi imene ikubwelayo, adzapeza moyo wosatha.” (Maliko 10:​29, 30) Madalitso amene mwapezawo ni oculuka kwambili kuposa zimene munasiya.—Sal. 37:4.

6. N’cifukwa ciyani mudzafunika kupitilizabe kulimbana na “cilakolako ca thupi” pambuyo pa ubatizo?

6 Mudzafunika kupitilizabe kugwebana na “cilakolako ca thupi” ngakhale pambuyo pa ubatizo. (1 Yoh. 2:16) Zili conco cifukwa mudzapitiliza kukhala mbadwa yopanda ungwilo ya Adamu. Nthawi zina mungadzimve mmene Paulo anamvela pamene analemba kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambili ndi cilamulo ca Mulungu, koma ndimaona cilamulo cina m’ziwalo zanga cikumenyana ndi cilamulo ca m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa cilamulo ca ucimo cimene cili m’ziwalo zanga.” (Aroma 7:​22, 23) Mwina mungalefuke poona kuti mumakhala na zilakolako zoipa. Komabe kuganizila lonjezo limene munapeleka kwa Yehova podzipatulila kudzakuthandizani kutsimikiza mtima kugonjetsa mayeselo. Ndipo zoona zake n’zakuti lumbilo lanu la kudzipatulila lidzakuthandizani kugonjetsa mayeselo. Motani?

7. Kodi kudzipatulila kwanu kwa Yehova kudzakuthandizani bwanji kukhalabe wokhulupilika kwa iye?

7 Mukadzipatulila kwa Yehova mumadzikana nokha. Izi zikutanthauza kunena kuti ng’ang’a ku zikhumbo zanu, na zolinga zanu zimene sizingakondweletse Yehova. (Mat. 16:24) Conco, mukakumana na mayeso simudzacedwa na kuganizilapo zimene muyenela kucita. Mudzakhala mutadziwilatu zocita, zomwe ni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Mudzakhalabe wosasunthika pa kukondweletsa Yehova. Mudzakhala ngati Yobu amene ngakhale pambuyo pokumana na mavuto aakulu ananena motsimikiza kuti: “Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.

8. Kodi kusinkhasinkha pemphelo lanu la kudzipatulila kungakuthandizeni bwanji kukaniza mayeselo?

8 Kusinkhasinkha pemphelo limene munapeleka podzipatulila kwa Yehova, kudzakuthandizani kugonjetsa mayeselo alionse amene mungakumane nawo. Mwacitsanzo, kodi mungayambe kuceza mokopana na mkazi wa mwini kapena mwamuna wa mwini? M’pang’ono pomwe! Cifukwa munasankhilatu kuti simungacite za mtundu umenewu. Ngati simulola zilakolako zoipa kuzika mizu mwa inu, simudzafunika kulimbana nazo mtsogolo. Ndipo mudzapewa kuyenda “panjila yoipa.”—Miy. 4:​14, 15.

9. Kodi kusinkhasinkha pemphelo lanu la kudzipatulila kungakuthandizeninso motani kutsogoza zauzimu?

9 Bwanji ngati mwapeza nchito, koma imene izikulepheletsani kupezeka ku misonkhano nthawi zina? Mudziŵa kale zoyenela kucita. Ngakhale mukalibe kupeza nchito imeneyo, munanena kale kuti ng’ang’a mumtima mwanu ku nchito zotelozo. Conco, simudzayamba kuganiza kuti niloŵabe nchitoyi,koma niziona mocitila kuti niziikabe zauzimu patsogolo. Kuganizila citsanzo ca Yesu kungakuthandizeni. Iye anali wofunitsitsa kukondweletsa Atate ake. Nanunso muyenela kukana nthawi yomweyo komanso mosasunthika ciliconse cimene cingakhumudwitse Mulungu amene munadzipatulila kwa Iye.—Mat. 4:10; Yoh. 8:29.

10. Kodi Yehova adzakuthandizani motani kuti mupitilize kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo wanu?

10 Kwenikweni, mayeso na mayeselo amakupatsani mpata woonetsa kuti ndinu wofunitsitsa kum’tsatilabe Yesu. Mwa kutelo, dziŵani kuti Yehova adzakuthandizani. Baibo imati: “Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile, koma pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.”—1 Akor. 10:13.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUPITILIZE KUMUTSATILA YESU

11. Kodi imodzi mwa njila zabwino koposa zimene tingatsatilile Yesu ni iti? (Onaninso cithunzi.)

11 Yesu anali wokangalika potumikila Yehova ndipo anali kupemphela kwa Iye kaŵili-kaŵili. (Luka 6:12) Ndipo cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili cimene mungacite kuti mupitilize kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo wanu, ni kukhala na pulogilamu imene ingakuthandizeni kuyandikila Yehova. Baibo imati: “Mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenela m’njila yomweyo.” (Afil. 3:16) Nthawi na nthawi, mumamva zocitika za abale na alongo amene adzipeleka kuti awonjezele utumiki wawo wopatulika. Mwina analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu, kapena anasamukila ku malo osoŵa. Ngati mungathe kudziikila zolinga ngati zimenezi, teloni. Anthu a Yehova ni ofunitsitsa kuwonjezela utumiki wawo. (Mac. 16:9) Nanga bwanji ngati pali pano simungakwanitse kucita zimenezi? Musamadzione kuti ndinu wolephela podziyelekezela na amene angakwanitse. Cofunika kwambili kwa Akhristu ni kupitilizabe kutumikila mokhulupilika. (Mat. 10:22) Musaiŵale kuti Yehova amakondwela ngako ngati mum’patsa zonse zimene mungathe malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wanu. Iyi ndiyo njila yabwino kwambili imene mungapitilizile kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo wanu.—Sal. 26:1.

Mlongo wacitsikana wokondwela amene wangobatizika kumene m’dziŵe. Tuzithunzi twa mkati tuonetsa: 1. Akulalikila mu utumiki. 2. Waloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu. 3. Akuika mawaya amagetsi pa nchito zamamangidwe za gulu lathu.

Pambuyo pa ubatizo wanu, dziikileni colinga cocita zinthu zimene zingakuthandizeni kuyandikila Yehova (Onani ndime 11)


12-13. Kodi muyenela kutani cangu canu cikayamba kucepa? (1 Akorinto 9:​16, 17) (Onaninso danga lakuti, “Pitilizani Kuthamanga.”)

12 Nanga bwanji ngati mwaona kuti mapemphelo anu komanso utumiki wanu zikungocitika mwamwambo cabe? Bwanji ngati mwaona kuti simukupindula na kuŵelenga Baibo kwanu monga munali kucitila kale? Ngati zaconco zakucitikilani pambuyo pa ubatizo, musaganize kuti basi mzimu wa Yehova wakucokelani. Ndinu wopanda ungwilo, ndipo nthawi zina mungamamve conco. Ngati cangu canu cayamba kucepa, muzisinkhasinkha citsanzo ca mtumwi Paulo. Ngakhale kuti anali kuyesetsa kutengela citsanzo ca Yesu, iye anadziŵa kuti nthawi zina sangakhale na cikhumbo cofuna kucita zimenezo. (Ŵelengani 1 Akorinto 9:​16, 17.) Anati: “Koma ndikacita motsutsana ndi kufuna kwanga, sindingacitile mwina, ndinebe woyang’anila mogwilizana ndi udindo umene unaikidwa m’manja mwanga.” M’mawu ena, Paulo anali wotsimikiza mtima kukwanilitsa utumiki wake mosasamala kanthu za mmene anali kumvela pa nthawiyo.

13 Mofananamo, musadalile maganizo anu opanda ungwilo popanga zisankho. Khalani otsimikiza kucita zoyenela mosasamala kanthu za mmene mukumvela. Mukatelo, m’kupita kwa nthawi mudzayamba kukondwela nako kucita zinthu zauzimu. Kukhala na pulogilamu yocita zinthu zauzimu pa mlingo uliwonse kudzakuthandizani kupitiliza kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo. Kulimbikila kwanu kucita zinthu zauzimu kudzalimbikitsa alambili anzanu kucita cimodzi-modzi.—1 Ates. 5:11.

Pitilizani Kuthamanga

Cithunzi: 1. Munthu amene amathamanga pa mpikisano akudya cakudya copatsa thanzi; kacithunzi ka mkati kaonetsa m’bale akuŵelenga Baibo. 2. Wothamanga pa mpikisano uja akudzinyolola; kacithinzi ka mkati kaonetsa m’baleyo akupeleka ndemanga pa msonkhano. 3. Wothamanga pa mpikisano uja akuthamanga; kacithunzi ka mkati kaonetsa m’bale uja akucita ulaliki wapoyela.

Munthu wothamanga pa mpikisano ayenela kukhalabe wathanzi kuti apitilize kuthamanga. Mofananamo, inunso muyenela kukhalabe athanzi mwauzimu kuti mupitilize kutumikila Yehova pambuyo pa ubatizo wanu.

“PITILIZANI KUDZIYESA”

14. Kodi muyenela kudzisanthula mobweleza-bweleza pa zinthu ziti? Nanga n’cifukwa ciyani? (2 Akorinto 13:5)

14 Zimakhalanso zothandiza kudzisanthula pafupi-pafupi pambuyo pa ubatizo. (Ŵelengani 2 Akorinto 13:5.) Nthawi na nthawi, muzidzisanthula kuona ngati mumapemphela tsiku lililonse, kuŵelenga Baibo mwakhama, kupezeka pa misonkhano, komanso kulalikila. Pezani njila zomwe zingakuthandizeni kuti muzikondwela pocita zimenezi, komanso kuti muzipindula. Mwacitsanzo, mungadzifunse mafunso monga akuti: ‘Kodi ningakwanitse kufotokozela ena ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo? Kodi pali zimene ningacite kuti nizikondwela na utumiki wanga? Kodi mapemphelo anga amakhala ochula zinthu mwachuchuchu, ndipo amaonetsa kuti nimadalila Yehova? Kodi nimapezeka pa misonkhano ya Cikhristu nthawi zonse? Kodi ningacite ciyani kuti nizimvetsela mwachelu pa misonkhano, komanso kuti nizitengako mbali mokwanila?’

15-16. Mwaphunzila ciyani pa cocitika ca m’bale wina pa nkhani yokaniza mayeselo?

15 Mungacitenso bwino kudziunika moona mtima pa zifooko zanu. M’bale wina dzina lake Robert anafotokoza cocitika cimene cifotokoza bwino mfundo imeneyi. Anati: “Nili na zaka 20 n’nali kugwila nchito inayake. Tsiku lina n’takomboka mtsikana wina amene n’nali kuseŵenza naye ananiitanila kunyumba kwake. Ananena kuti tidzakhalako aŵili-ŵili, ndipo tidzasangalatsana. Poyamba sin’nakane mwamphamvu. Koma pambuyo pake n’nakana ndipo n’namufotokozela cifukwa cake.” Robert anakana ciyesoco, ndipo zimenezi n’zabwino. Komabe, akaganizila zimene zinacitikazo, amaona kuti akanacita bwino kwambili kuposa mmene anacitila. Anati: “Sin’nakanize ciyesoco mwamsanga kapena mwamphamvu mmene Yosefe anacitila kwa mkazi wa Potifara. (Gen. 39:​7-9) Ndipo n’nadabwa kuona kuti cinali covuta kwa ine kukana. Cocitikaci cinanithandiza kuona kuti nifunika kulimbitsa ubale wanga na Yehova.”

16 Inunso mungapindule ngati mwadzisanthula monga anacitila Robert. Ngakhale mutakwanitsa kukaniza ciyeso, mungadzifunsebe kuti, ‘Kodi zinanitengela utali wanji kuti nikane?’ Ngati mwaona kuti simunacite bwino, musadziimbe mlandu. M’malo mwake, kondwelani kuti mwazindikila cifooko cimeneco. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni, ndipo citani zonse zotheka kuti mukhale ofunitsitsa kutsatila miyeso yake ya makhalidwe abwino.—Sal. 139:​23, 24.

17. Kodi kukhulupilika kwa Robert kunakhudza bwanji dzina la Yehova?

17 Palinso zina zimene tingaphunzile pa cocitika ca Robert. Ananenanso kuti: “N’takana ciitano ca mtsikanayo, ananiuza kuti ‘wakhoza mayeso!’ Ndiyeno n’namufunsa kuti anali kutanthauza ciyani. Anafotokoza kuti mnzake wina yemwe kale anali Mboni anamuuza kuti acinyamata ambili a Mboni amakhala umoyo wa paŵili. Ndipo akapeza mpata wocita zosayenela sazengeleza. Conco anauza mnzakeyo kuti adzayesa zimenezo pa ine. N’nakondwela ngako podziŵa kuti n’nalemekezetsa dzina la Yehova.”

18. Kodi ndinu wofunitsitsa kucita ciyani pambuyo pa ubatizo? (Onaninso mbali yakuti “Nkhani Ziŵili Zimene Zingakuthandizeni.”)

18 Mukadzipatulila kwa Yehova na kubatizika, mumaonetsa kuti mufuna kuyeletsa dzina lake, kaya mukumane na zotani. Khalani otsimikiza kuti Yehova amadziŵa mavuto amene mumakumana nawo, komanso mayeselo amene mumakaniza. Adzakudalitsani pa khama lanu kuti mukhalebe wokhulupilika. Khalani na cidalilo cakuti kupyolela mwa mzimu wake woyela adzakupatsani mphamvu zocita zimenezi. (Luka 11:​11-13) Na thandizo la Yehova mudzapitilizabe kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo wanu.

Nkhani Ziŵili Zimene Zingakuthandizeni

Ngati ndinu wacinyamata ndipo mukuleledwa m’coonadi, mudzasangalala na nkhani ya mbali ziŵili za m’Cingelezi pa jw.org za mutu wakuti “Young People Ask . . . What Will I Need to Do After Baptism?” Mbali yoyamba idzakuthandizani kuona zimene mungacite kuti muyandikilebe Yehova. Mbali yaciŵili idzakuthandizani kuona zimene mungacite kuti mukhalebe okhulupilika mukakumana na mavuto kapena mayeselo.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Akhristu amanyamula “mtengo wozunzikilapo tsiku ndi tsiku” m’lingalilo lotani?

  • Muyenela kutani kuti mupitilizebe kutsatila Yesu pambuyo pa ubatizo wanu?

  • Kodi kusinkha-sinkha pemphelo lanu la kudzipatulila kungakuthandizeni motani kukhalabe wokhulupilika?

NYIMBO 89 Mvela Udalitsike

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani