Mawu Oyamba
Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko lopanda nkhondo komanso ciwawa? N’zimene ambili amafuna. Koma amaona kuti n’zosatheka. Baibo imatiuza cifukwa cake anthu alephela kuthetsa nkhondo. Imapelekanso maumboni otsimikizila kuti n’zotheka kukhala ndi mtendele padziko lonse, ndiponso kuti zimenezi zidzacitikadi posacedwa.
M’magazini ino, mawu akuti “nkhondo” akukamba za kumenyana pakati pa magulu a nkhondo pa zifukwa za ndale. Maina a anthu ena amene achulidwa m’magazini ino asinthidwa.