NKHANI YOPHUNZILA 20
NYIMBO 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu
Yang’anani kwa Yehova Kuti Akulimbikitseni
“Atamandike . . . Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.”—2 AKOR. 1:3.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Maphunzilo amene titengapo poona mmene Yehova analimbikitsila Ayuda amene anali ku ukapolo.
1. Kodi Ayuda amene anali mu ukapolo ku Babulo anali mumkhalidwe wotani?
KWA zaka zambili, Ayuda mobwelezabweleza sanamvele Yehova. Zotsatilapo zake n’zakuti iye analola Ababulo kuwononga dziko lawo ndi kuwatenga kupita nawo ku ukapolo. Kodi zinthu zinali bwanji kwa iwo? (2 Mbiri 36:15, 16, 20, 21) N’zoona kuti Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo anali ndi ufulu wocita zilizonse zimene anali kufuna pa umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku. (Yer. 29:4-7) Komabe, umoyo unali wovuta ndipo n’zoonekelatu kuti si umoyo umene akanasankha kukhala. Kodi iwo anamva bwanji cifukwa ca mkhalidwe umene analimo? Onani mawu amene mmodzi wa Ayuda okhulupilika amene anali ku ukapolo anakamba: “Tinakhala pansi mʼmphepete mwa mitsinje ya ku Babulo. Tinalila titakumbukila Ziyoni.” (Sal. 137:1) Ayuda acisoniwo anafunika cilimbikitso. Koma kodi ndani akanawalimbikitsa?
2-3. (a) Kodi Yehova anawacitila ciyani Ayuda amene anali ku ukapolo? (b) Tikambilane ciyani m’nkhani ino?
2 Yehova ndi “Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse.” (2 Akor. 1:3) Pokhala Mulungu wacikondi, iye amakhala wofunitsitsa kuthandiza atumiki ake. Yehova anadziwa kuti ena mwa Ayuda amene anali ku ukapolo adzamva cisoni pa zoipa zimene anacita, ndipo adzayambanso kum’tumikila. (Yes. 59:20) Conco, zaka zoposa 100 Ayuda asanatengedwe kupita ku ukapolo, iye anauzila mneneli Yesaya kulemba buku la m’Baibo lodziwika ndi dzina lake. N’colinga canji? Yesaya anati: “‘Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,’ akutelo Mulungu wanu.” (Yes. 40:1) Inde, kudzela mwa mneneli wake Yesaya, Yehova analimbikitsa Ayudawo.
3 Mofanana ndi Ayuda amene anali ku ukapolo, nafenso timafunikila cilimbikitso nthawi ndi nthawi. M’nkhani ino, tikambilane njila zitatu zimene Yehova anagwilitsa nchito polimbikitsa Ayudawo: (1) Analonjeza kuti adzakhululukila anthu olapa, (2) anawapatsa ciyembekezo, ndiponso (3) anawathandiza kuti asakhale ndi mantha. Pokambilana mfundozi, tidzaonanso mmene Yehova amatilimbikitsila monga mmene anacitila ndi Ayuda.
YEHOVA AMATIKHULULUKILA MWACIFUNDO
4. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti ndi Mulungu wacifundo? (Yesaya 55:7)
4 Yehova ndi “Tate wacifundo cacikulu.” (2 Akor. 1:3) Anaonetsa khalidwe limeneli pamene analonjeza kuti adzakhululukila Ayuda olapa. (Welengani Yesaya 55:7.) Iye anati: “Cifukwa ca cikondi canga cokhulupilika cimene sicidzatha ndidzakucitila cifundo.” (Yes. 54:8) Kodi Yehova anali kudzawaonetsa bwanji cifundo cimeneco? Ngakhale kuti Ayuda anali kudzakumana ndi mavuto cifukwa ca zolakwa zawo, Yehova anawalonjeza kuti sadzakhala akapolo ku Babulo mpaka kalekale. (Yes. 40:2) Mawu amenewa ayenela kuti anawalimbikitsa kwambili Ayuda amene analapa.
5. N’cifukwa ciyani tili ndi zifukwa zambili kuposa Ayuda zokhulupilila kuti Mulungu ndi wacifundo?
5 Tiphunzilapo ciyani? Yehova ndi wokonzeka kukhululukila atumiki ake ndi mtima wonse. Masiku ano tili ndi zifukwa zambili kuposa Ayudawo zotipangitsa kukhulupilila kuti Yehova amatikhululukila. Cifukwa ciyani? Cifukwa tidziwa zimene Yehova wacita kuti atikhululukile. Patapita zaka mahandiledi Yesaya atakamba za kukhululuka kwa Yehova, Yehova anatumiza Mwana wake wokondeka kudzapeleka moyo wake dipo m’malo mwa anthu onse olapa. Nsembe imeneyo imapangitsa kuti macimo athu “afafanizidwe” kothelatu. (Mac. 3:19; Yes. 1:18; Aef. 1:7) Zoonadi, Yehova ndi Mulungu wacifundo!
6. Kodi kuganizila za cifundo ca Yehova kumatithandiza motani? (Onaninso cithunzi.)
6 Mawu ouzilidwa a Yehova a pa Yesaya 55:7, angatithandize ngati timadziimbabe mlandu pa zolakwa zimene tinacita m’mbuyomu ngakhale kuti tinalapa. Tingamadziimbebe mlandu makamaka ngati tikali kukumana ndi mavuto cifukwa ca zolakwa zimenezo. Koma ngati tinaulula macimo athu ndi kusintha njila zathu, sitiyenela kukaikila kuti Yehova anatikhululukila. Ndipo Yehova akakhululuka, sakumbukilanso macimo athu. (Yelekezelani ndi Yeremiya 31:34.) Conco, ngati Yehova sakumbukila macimo athu akumbuyo, nafenso sitiyenela kuwakumbukila. Cofunika kwambili kwa Yehova ndi zimene tikucita palipano, osati zolakwa zimene tinacita kumbuyo. (Ezek. 33:14-16) Ndipo posacedwa, Atate wathu wacifundo cacikulu adzacotselatu mavuto onse amene timakumana nawo cifukwa ca zolakwa zathu.
Cofunika kwambili kwa Yehova ndi zimene tikucita palipano, osati zolakwa zimene tinacita kumbuyo (Onani ndime 6)
7. N’ciyani cingatilimbikitse kuulula chimo lathu kwa akulu?
7 Tiyenela kucita ciyani ngati cikumbumtima cathu cimativutitsa cifukwa tinabisa chimo lalikulu? Baibo imatilimbikitsa kuti tifunika kupempha thandizo kwa akulu. (Yak. 5:14, 15) Koma nthawi zambili cimativuta kuuza akulu zimene tinalakwitsa. Komabe, tiyenela kukumbukila kuti Yehova amagwilitsa nchito amuna acikondi amenewa kuti atithandize mwacifundo. Conco ngati ndife olapa, ndipo timakumbukila mfundo imeneyi, tidzakhala ofunitsitsa kuwafikila. Onani mmene cifundo ca Yehova cinalimbikitsila m’bale wina dzina lake Arthur,a amene cikumbumtima cake cinali kumuvutitsa kwambili. Iye anati: “Pafupifupi kwa caka cimodzi n’nali kuonelela zamalisece. Koma pambuyo pomvetsela nkhani yokamba za cikumbumtima, n’naulula chimo langa kwa mkazi wanga komanso kwa akulu. N’tacita izo n’namvako bwino. Koma n’nali kudziimbabe mlandu pa chimo langalo. Akulu anandikumbutsa kuti Yehova anali kufuna kuti ndikhalebe bwenzi lake. Iye amatipatsa cilango cifukwa cotikonda. Mawu awo okoma mtima anandifika pamtima kwambili ndipo anandithandiza kuona kuti Yehova anandikhululukiladi.” Tsopano, Arthur ndi mpainiya wa nthawi zonse, ndipo akutumikila monga mtumiki wothandiza. N’zolimbikitsa kwambili kudziwa kuti Yehova amationetsa cifundo tikalapa.
YEHOVA AMATIPATSA CIYEMBEKEZO
8. (a) Kodi Yehova anapeleka ciyembekezo cotani kwa Ayuda amene anali ku ukapolo? (b) Malinga ndi Yesaya 40:29-31, kodi ciyembekezo cimene Yehova anawapatsa cinawakhudza bwanji Ayuda?
8 M’kaonedwe kaumunthu, Ayuda analibiletu ciyembekezo cakuti tsiku lina adzamasulidwa n’kubwelela kwawo. Zinali conco cifukwa Ababulo anali kudziwika kuti sanali kumasula akapolo awo. (Yes. 14:17) Koma Yehova anapatsa anthu ake ciyembekezo. Anawalonjeza kuti adzawamasula ndipo palibe cimene cikanamulepheletsa kucita zimenezi. (Yes. 44:26; 55:12) M’maso mwa Yehova, Ababulo anali ngati fumbi. (Yes. 40:15) Fumbi limauluzika mosavuta. Conco, Yehova anali kudzamasula Ayuda mosavuta ku Babulo. Kodi ciyembekezoci cinawathandiza bwanji Ayuda? Cinawalimbikitsa. Koma cinacita zoposa pamenepo. Yesaya analemba kuti: “Anthu amene amayembekezela Yehova adzapezanso mphamvu.” (Welengani Yesaya 40:29-31.) Ciyembekezoci cinawapatsanso mphamvu. Yesaya anakamba kuti “iwo adzaulukila mʼmwamba ngati kuti ali ndi mapiko a ciwombankhanga.”
9. N’ciyani ciyenela kuti cinathandiza Ayuda kukhulupilila lonjezo lakuti Yehova adzawamasula ku ukapolo?
9 Yehova anapatsa Ayudawo zifukwa zokhulupilila malonjezo ake. Anacita bwanji zimenezi? Ganizilani za maulosi amene anali atakwanilitsidwa kale. Iwo anali kudziwa kuti Asuri anagonjetsa ufumu wakumpoto wa Isiraeli ndi kutenga anthu kupita nawo ku ukapolo, monga anakambila Yehova. (Yes. 8:4) Anaonanso pamene Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu ndi kutengela ku ukapolo anthu ake. (Yes. 39:5-7) Ambili a iwo analipo pamene mfumu ya Babulo inacititsa khungu Mfumu Zedekiya ndi kupita naye ku Babulo. (Yer. 39:7; Ezek. 12:12, 13) Conco, zonse zimene Yehova ananenelatu zinacitikadi. (Yes. 42:9; 46:10) Izi ziyenela kuti zinalimbikitsa kwambili cikhulupililo cawo cakuti lonjezo la Yehova lakuti adzamasulidwa lidzakwanilitsidwa.
10. N’ciyani cingatithandize kusungabe ciyembekezo cathu cili cowala m’masiku ano otsiliza?
10 Tiphunzilapo ciyani? Tikafooka, ciyembekezo cingatilimbikitse ndi kutipatsanso mphamvu. Tikukhala m’nthawi yovuta ndipo tikulimbana ndi adani amphamvu. Koma sitiyenela kutaya mtima. Yehova watipatsa ciyembekezo cosangalatsa codzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso. Mmenemo tidzakhala mwamtendele komanso motetezeka. Tiyenela kusungabe ciyembekezo cathu cimeneci cili cowala m’maganizo mwathu. Tikapanda kutelo ciyembekezo cathu cingakhale ngati windo yagalasi yomwe yacita dothi imene ikutilepheletsa kuona bwino malo okongola. Kodi tingasunge bwanji ciyembekezo cathu cili cowala, komwe kuli ngati kupukuta galasilo? Tizipatula nthawi yoganizila mmene umoyo udzakhalile wabwino kwambili m’dziko latsopano. Tiziwelenga nkhani, kuonelela mavidiyo, komanso kumvetsela nyimbo zokamba za ciyembekezo cathu. Ndipo tikamapemphela, tizimuuza Yehova za malonjezo amene tikuwayembekezela mwacidwi kuti adzakwanilitsike.
11. N’ciyani cimathandiza mlongo Joy amene akudwala matenda aakulu kupezanso mphamvu?
11 Onani mmene ciyembekezo cimatonthozela ndi kulimbikitsila mlongo wina dzina lake Joy, amene akudwala matenda aakulu. Mlongoyu anati: “Mavuto akandiculukila, ndimauza Yehova nkhawa zanga podziwa kuti iye amandimvetsa. Yehova amandiyankha mwa kundipatsa ‘mphamvu yoposa yacibadwa.’” (2 Akor. 4:7) Mlongo Joy amayelekezanso kuti ali m’dziko latsopano, mmene “palibe munthu wokhala mʼdzikolo amene adzanene kuti: ‘Ine ndikudwala.’” (Yes. 33:24) Ifenso tingapezenso mphamvu ngati tikhutulila Yehova zamumtima mwathu ndi kuika maganizo athu pa ciyembekezo cimene tili naco.
12. Tili ndi zifukwa ziti zokhulupilila malonjezo a Yehova? (Onaninso cithunzi.)
12 Monga anacitila ndi Ayuda amene anali ku ukapolo, nafenso Yehova watipatsa zifukwa zambili zokhulupilila malonjezo ake. Ganizilani maulosi amene tikuwaona akukwanilitsidwa. Mwacitsanzo, tikuona ulamulilo wamphamvu wapadziko lonse umene ndi wolimba pa zinthu zina koma wosalimba pa zina. (Dan. 2:42, 43) Timamvanso za “zivomezi m’malo osiyanasiyana,” ndipo timatengako mbali pa nchito yolalikila “ku mitundu yonse.” (Mat. 24:7, 14) Maulosi amenewa komanso ena ambili amene akukwanilitsidwa, amalimbikitsa cikhulupililo cathu cakuti malonjezo a Yehova a zam’tsogolo adzakwanilitsidwa.
Maulosi amene tikuwaona akukwanilitsidwa masiku ano amatipatsa zifukwa zokhulupilila malonjezo a Yehova (Onani ndime 12)
YEHOVA AMATITHANDIZA KUTI TISAKHALE NDI MANTHA
13. (a) N’zovuta zotani zimene Ayuda anali kudzakumana nazo pa nthawi ya kumasulidwa kwawo? (b) Malinga ndi Yesaya 41:10-13, kodi Yehova anawalimbikitsa bwanji Ayuda?
13 Yehova analimbikitsa Ayuda amene anali akapolo ku Babulo mwa kuwapatsa ciyembekezo cosangalatsa cakuti adzamasulidwa. Ngakhale n’telo iye anadziwa kuti iwo adzakumana ndi zovuta pa nthawi ya kumasulidwa kwawo. Yehova anakambilatu kuti kumapeto kwa ukapolo wawo, mfumu yamphamvu idzagonjetsa mzinda wa Babulo komanso mitundu yoyandikana ndi mzindawo. (Yes. 41:2-5) Kodi Ayuda anafunika kucita mantha? Ayi. Cifukwa zaka zambili izi zisanacitike, Yehova analimbikitsa atumiki ake powauza kuti: “Usacite mantha, cifukwa ndili ndi iwe. Usade nkhawa cifukwa ine ndine Mulungu wako.” (Welengani Yesaya 41:10-13.) Kodi Yehova anatanthauza ciyani pokamba kuti “ine ndine Mulungu wako”? Sanali kukumbutsa Ayuda kuti ayenela kumulambila, cifukwa iwo anali kudziwa kale zimenezi. Koma anali kuwakumbutsa kuti iye akali kumbali yawo ndipo adzawathandiza.—Sal. 118:6.
14. N’ciyaninso cina cimene Yehova anacita pothandiza Ayuda kuthetsa mantha?
14 Yehova anathandizanso Ayudawo kuthetsa mantha awo mwa kuwakumbutsa za mphamvu zake zopanda malile komanso cidziwitso cake. Anawauza kuti ayang’ane nyenyezi za kumwamba. Anawauzanso kuti ndiye analenga nyenyezizo ndipo amadziwanso dzina la nyenyezi iliyonse. (Yes. 40:25-28) Popeza Yehova amadziwa dzina la nyenyezi iliyonse, ndiye kuti n’zosakayikitsa kuti amadziwanso dzina la mtumiki wake aliyense. Komanso, popeza Yehova ali ndi mphamvu zolenga nyenyezi, ndiye kuti sangalephele kuthandiza anthu ake. Conco, Ayudawo analibe cifukwa cokhalila ndi nkhawa komanso mantha.
15. Kodi Mulungu anawakonzekeletsa bwanji Ayuda pa zimene zinali kubwela m’tsogolo?
15 Yehova anauza anthu ake zimene anayenela kucita nthawi yoti amasulidwe ikadzafika. Kumayambililo kwa buku la Yesaya, Mulungu anauza anthu akewo kuti: “Mukalowe mʼzipinda zanu zamkati, ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) N’kutheka kuti Ayuda anatsatila malangizowa pamene Mfumu Koresi anagonjetsa mzinda wa Babulo. Wolemba mbili yakale wa Cigiriki ananena kuti pamene Koresi analowa mumzinda wa Babulo, “analamula asilikali ake kuti aphe munthu aliyense amene adzapezeka pabwalo panyumba zawo.” Zimenezi ziyenela kuti zinawacititsa mantha kwambili anthu okhala m’Babulo. Koma n’kutheka kuti Ayuda anapulumuka cifukwa comvela malangizo a Yehova.
16. N’cifukwa ciyani siyenela kuda nkhawa kwambili ndi cisautso cacikulu cimene cikubwela? (Onaninso cithunzi.)
16 Tiphunzilapo ciyani? Posacedwa, tidzayang’anizana ndi cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo m’mbili yonse ya anthu. Cikadzayamba, anthu padziko lapansi adzasokonezeka ndipo adzacita mantha. Koma si mmene zidzakhalile kwa anthu a Yehova. Tidziwa kuti Yehova ndi Mulungu wathu. Tidzaimilila cilili podziwa kuti “cipulumutso [cathu] cikuyandikila.” (Luka 21:28) Ngakhale pamene mgwilizano wa mitundu udzatiukila, sitidzacita mantha. Yehova adzatiteteza pogwilitsa nchito angelo komanso malangizo amene adzatipatsa. Kodi iye adzagwilitsa nchito ciyani potipatsa malangizowo? Palipano sitidziwa mmene adzacitile zimenezi. Komabe, n’kutheka kuti tingadzalandile malangizo amenewa kudzela m’mipingo. Mipingo ndiyo ingadzakhale “zipinda [zathu] zamkati,” mmene tidzakhala otetezeka. Tingazikonzekele bwanji zinthu zimene zikubwela m’tsogolo? Tiyenela kugwilizana kwambili ndi abale ndi alongo athu, komanso kukhala okonzeka kumvela malangizo amene gulu la Yehova limapeleka. Cina, sitiyenela kukaikila kuti Yehova ndiye akutsogolela gulu lathu.—Aheb. 10:24, 25; 13:17.
Podziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu ndipo angakwanitse kutipulumutsa, siticita mantha tikamaganizila za cisautso cacikulu (Onani ndime 16)b
17. Mungapeze bwanji cilimbikitso kwa Yehova?
17 Ngakhale kuti zinthu zinali zovuta kwa Ayuda amene anali ku ukapolo, Yehova anawapatsa cilimbikitso cimene anali kufunikila. Adzacitanso cimodzimodzi kwa ife. Ngakhale kuti sitidziwa mavuto amene tidzakumane nawo m’tsogolo, tiyeni tipilize kuyang’anabe kwa Yehova kuti azitilimbikitsa. Muzikhulupilila kuti iye ndi wacifundo cacikulu. Sungani ciyembekezo canu cili cowala. Ndipo muzikumbukila kuti cifukwa Yehova ndi Mulungu wanu, simuyenela kucita mantha.
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
a Maina ena asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Kagulu ka abale ndi alongo kasonkhana m’cipinda. Iwo ali ndi cidalilo cakuti Yehova ali ndi mphamvu ndipo angakwanitse kuwateteza kulikonse kumene angakhale padziko lapansi.