NKHANI YOPHUNZILA 30
NYIMBO 97 Moyo Umadalila Mau a Mulungu
Kodi Ziphunzitso Zoyambilila za m’Baibo Zikali Zothandiza kwa Inu?
“Ndikufuna kuti ndizikukumbutsani zinthu zimenezi nthawi zonse, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba mʼcoonadi.”—2 PET. 1:12.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene mungagwilitsile nchito mfundo zofunika za ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo ngakhale kuti papita zaka kucokela pamene munaziphunzila koyamba.
1. Kodi kuphunzila ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo kunakuthandizani motani?
ZIPHUNZITSO zoyambilila zimene tinaphunzila titangoyamba kuphunzila Baibo, zinasintha umoyo wathu. Mwacitsanzo, titaphunzila kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, tinayamba ndife kucitapo kanthu kuti tikhale bwenzi lake. (Yes. 42:8) Titaphunzila za mkhalidwe wa akufa, tinasiya kudela nkhawa kuti okondedwa athu amene anamwalila akuzunzika kwinakwake. (Mlal. 9:10) Ndipo titaphunzila za lonjezo la Mulungu lakuti dziko lapansi lidzakhala Paradaiso, tinasiya kudela nkhawa za tsogolo lathu. Tinakhala ndi cidalilo cakuti tidzakhala ndi moyo, osati kwa nthawi yocepa monga zaka 70 kapena 80, koma kwamuyaya!—Sal. 37:29; 90:10.
2. Kodi 2 Petulo 1:12, 13 ionetsa motani kuti ngakhale Akhristu okhwima angapindule ndi ziphunzitso zoyambilila za m’Malemba?
2 Sitiyenela kuiwala kufunika kwa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo zimene tinaphunzila. Mtumwi Petulo analemba kalata yake yaciwili kwa Akhristu amene anali kale “olimba m’coonadi.” (Welengani 2 Petulo 1:12, 13.) Koma tsopano, mu mpingo munali mavuto oopsa akuuzimu omwe anaphatikizapo aphunzitsi abodza komanso anthu amakhalidwe oipa. (2 Pet. 2:1-3) Conco Petulo anafuna kulimbikitsa abale ndi alongo ake kuti adziteteze ku zoopsazo. Ndipo anatelo mwa kuwakumbutsa zina mwa ziphunzitso zimene Akhristuwo anali ataziphunzila kale. Ziphunzitso zimenezo n’zimene zikanawathandiza kukhalabe okhulupilika mpaka mapeto.
3. Pelekani citsanzo coonetsa cifukwa cake Akhristu onse ayenela kupitiliza kusinkhasinkha ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo.
3 Ngakhale kuti takhala m’coonadi kwa nthawi yaitali, tingapindulebe ndi ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. Ganizilani izi: Wophika waluso komanso wophika wacatsopano angaphike keke pogwilitsa nchito zinthu zofanana. Koma wophika walusoyo angaphike keke pogwilitsa nchito zinthu zofananazo m’njila zina zambili zabwino koposa cifukwa wakhala akuphika kwa nthawi yaitali. Mofananamo, amene akhala m’coonadi kwa nthawi yaitali angatengepo maphunzilo ambili pa mfundo imodzi ya coonadi mosiyana ndi mmene acatsopano angacitile. N’cifukwa ciyani tikutelo? N’kutheka kuti zinthu zinasintha pa umoyo wathu kucokela pamene tinabatizika. N’kuthekanso tili ndi maudindo ena m’gulu la Yehova. Conco, ngati tingaganizilenso ziphunzitso zoyambilila za coonadi zimene tinaphunzila kumbuyoko, tingapeze mfundo zina zatsopano zimene zingatithandize pa umoyo wathu panopa. Tiyeni tione mmene Akhristu okhwima angapindulile ndi ziphunzitso zoyambilila zitatu za m’Baibo zimene tikambilana m’nkhani ino.
YEHOVA NDIYE MLENGI
4. Kodi kudziwa kuti Yehova ndiye Mlengi kwatithandiza motani?
4 Tidziwa kuti dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zinalengedwa ndi Mlengi wanzelu komanso wamphamvu. Baibo imati: “Amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheb. 3:4) Koma palinso zina tingaphunzile pa mfundo ya coonadi imeneyi. Popeza Yehova ndiye anatilenga, iye amatidziwa bwino kwambili. Iye amasamala za ife ndipo amadziwa zimene zili zabwino kwa ife. Conco kudziwa kuti Yehova ndiye Mlengi kwasintha umoyo wathu m’njila zambili, ndipo kwatithandiza kukhala ndi umoyo waphindu.
5. Kodi ndi mfundo ya coonadi iti imene ingatithandize kukhala odzicepetsa? (Yesaya 45:9-12)
5 Mfundo ya coonadi yakuti Yehova ndiye Mlengi ingatithandize kukhala odzicepetsa. Yobu ataika kwambili maganizo ake pa iyemwini komanso pa anthu ena, Yehova anam’kumbutsa kuti Iye ndiye Mlengi wamphamvuyonse. (Yobu 38:1-4) Cikumbutso cimeneci cinathandiza Yobu kudziwa kuti njila za Mulungu ndi zapamwamba kwambili kuposa za anthu. Mogwilizana ndi mfundoyi, patapita zaka, mneneli Yesaya analemba kuti: “Kodi dongo lingafunse woumba mbiya kuti: ‘Kodi ukupanga ciyani?’”—Welengani Yesaya 45:9-12.
6. Ndi pa nthawi iti makamaka pamene tingafunike kuganizila za nzelu za Mlengi wathu ndi ukulu wake? (Onaninso zithunzi.)
6 Mkhristu akatumikila Yehova kwa nthawi yaitali, angayambe kuona kuti maganizo ake ndiwo abwino koposa, m’malo moyang’ana kwa Yehova komanso m’Mawu ake kaamba ka citsogozo. (Yobu 37:23, 24) Nanga bwanji ngati Mkhristuyo angaganizile mozama za nzelu zosayelekezeleka za Mlengi wathu ndi ukulu wake? (Yes. 40:22; 55:8, 9) Kuganizila zimenezi kungam’thandize kukhalabe wodzicepetsa komanso kuti aziona maganizo ake moyenela.
N’ciyani cingatithandize kuti tiziwaona moyenela maganizo athu? (Onani ndime 6)d
7. N’ciyani cinathandiza Rahela kuvomeleza masinthidwe a m’gulu lathu?
7 Rahela wa ku Slovenia waona kuti kuganizila za Mlengi kwam’thandiza kulandila ndi kuvomeleza masinthidwe a m’gulu lathu. Iye anati: “Nthawi zina zimandivuta kuvomeleza zigamulo zimene zapangidwa ndi amene akutitsogolela. Mwacitsanzo, ngakhale kuti n’napenyelela vidiyo ya Ciunikilo Na. 8 ca Bungwe Lolamulila ca mu 2023, n’nadabwa kwambili pomwe koyamba n’naona m’bale wandevu akukamba nkhani. Conco n’napemphela kwa Yehova kuti andithandize kuzolowela masinthidwewa.” Rahela anazindikila kuti Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, Yehova, ndiye woyenela koposa kutsogolela gulu lake. Ngati inunso zimakuvutani kuvomeleza kamvedwe katsopano kapena kutsatila masinthidwe a gulu, bwanji osasinkhasinkha modzicepetsa za kuzama kwa nzelu za Mlengi wathu ndi kukula kwa mphamvu zake?—Aroma 11:33-36.
CIFUKWA CAKE MULUNGU AMALOLA KUTI TIZIVUTIKA
8. Kodi kudziwa cifukwa cake Mulungu amalola zoipa kucitika kwatipindulila motani?
8 N’cifukwa ciyani Mulungu amalola kuti tizivutika? Ena mwa anthu amene amalephela kupeza yankho la funsoli amakwiyila Mulungu ndipo amafika ponena kuti kulibe Mulungu. (Miy. 19:3) Koma inu munaphunzila kuti ucimo umene tinatengela komanso kupanda ungwilo n’zimene zimacititsa kuti tizivutika, osati Yehova. Mwaphunzilanso kuti kuleza mtima kwa Yehova kwathandiza anthu mamiliyoni kum’dziwa bwino komanso kudziwa mmene adzathetsele mavuto. (2 Pet. 3:9, 15) Mfundo zimenezi zakutonthozani ndipo zakuthandizani kumuyandikila.
9. Ndi pa zocitika ziti pamene tingafunike kukumbukila cifukwa cake Yehova amalola zoipa kucitika?
9 Timaona kufunika kokhala oleza mtima pamene tikuyembekezela Yehova kuti athetse mavuto. Koma nthawi zina, ife kapena anthu ena amene tidziwa tikakumana ndi zinthu zolefula, tikacitidwa zopanda cilungamo, kapena tikatayikilidwa okondedwa athu, tingayambe kuona kuti Yehova akucedwa kucotsapo zoipa. (Hab. 1:2, 3) Pa nthawi ngati zimenezi, tingacite bwino kuganizila cifukwa cake Yehova amalola olungama kukumana ndi mavuto.a (Sal. 34:19) Tingaganizilenso za colinga cake cothetsa mavuto kwamuyaya.
10. N’ciyani cimam’thandiza Anne kupilila imfa ya amayi ake?
10 Kumvetsa cifukwa cake Mulungu amalola mavuto kucitika kungatithandize kupilila. Anne amene amakhala pa cilumba ca Mayotte pa nyanja ya Indian Ocean anati: “Zaka zingapo zapitazo n’nataikilidwa amayi anga okondeka. Ndipo zimenezo zinandibweletsela cisoni cacikulu. Komabe nthawi zambili ndimakumbukila kuti Yehova sindiye amacititsa zoipa. Iye ndi wofunitsitsa kucotsapo mavuto a mtundu uliwonse ndi kuukitsa okondedwa athu. Kusinkhasinkha mfundo za coonadi zimenezi kumandibweletsela mtendele wa mumtima ndipo kumandilimbikitsa.”
11. N’zifukwa zina ziti zimene Yehova walolela kuti mavuto azicitika? Nanga kodi kudziwa zimenezo kungatithandize bwanji kupitiliza kulalikila?
11 Kudziwa mfundo ya coonadi yokhudza cifukwa cake Mulungu walola mavuto kucitika kungatilimbikitse kuti tipitilize kulalikila. Pambuyo pofotokoza kuti Yehova amaleza mtima pofuna kuti anthu alape ndi kupulumuka, Petulo analemba kuti: “Ganizilani za mtundu wa anthu amene muyenela kukhala. Muyenela kukhala anthu akhalidwe loyela ndipo muzicita nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu.” (2 Pet. 3:11) Imodzi mwa “nchito zosonyeza kuti [ndife] odzipeleka kwa Mulungu” ndi nchito yolalikila. Monga zilili ndi Atate wathu, nafenso timawakonda anthu. Timafuna kuti nawonso adzakhale m’dziko latsopano lolungama la Mulungu. Yehova wapeleka mpata kwa anthu a m’dela lanu kuti ayambe kum’lambila. Ndi mwayi waukulu kwambili kukhala wanchito mnzake wa Mulungu komanso kuthandiza anthu ambili mmene tingathele kuti aphunzile za iye mapeto asanafike.—1 Akor. 3:9.
TIKUKHALA ‘M’MASIKU OTSILIZA’
12. Kodi kudziwa kuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza’ kwatipindulila motani?
12 Baibo inafotokoza molondola mmene anthu adzakhalile ‘m’masiku otsiliza.’ (2 Tim. 3:1-5) Tikaona mmene anthu amacitila zinthu masiku ano, timaona mmene ulosiwu ukukwanilitsikila. Pamene tikuona anthu akuipilaipila, timakhala otsimikiza kwambili kuti Mawu a Mulungu ndi odalilika.—2 Tim. 3:13-15.
13. Malinga ndi fanizo la Yesu la pa Luka 12:15-21, kodi tingadzifunse mafunso ati?
13 Kudziwa kuti tikukhala m’masiku otsiliza kumatithandiza kuika zinthu zofunika patsogolo. Timaona kufunika kocita zimenezo m’fanizo limene Yesu anakamba pa Luka 12:15-21. (Welengani.) Nʼcifukwa ciyani mwamuna wa mʼfanizoli anachulidwa kuti anali “wopanda nzelu”? Yesu sananene kuti munthuyu anali wopanda nzelu cifukwa cakuti anali wolemela, koma cifukwa cakuti anaika zinthu zolakwika patsogolo. Iye ‘anadziunjikila cuma, koma [sanali] wolemela kwa Mulungu.’ N’cifukwa ciyani tingakambe kuti kucita zimenezo kunali kupanda nzelu? Mulungu anauza munthuyo kuti: “Usiku womwe uno moyo wako aufuna.” Pomwe dongosolo lino la zinthu likufika kumapeto, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolinga zanga zimaonetsa kuti zinthu zofunika kwambili n’ziti kwa ine? Nanga bwanji za zolinga zimene ndimalimbikitsa ana anga kudziikila? Kodi ndimagwilitsa nchito mphamvu zanga, nthawi yanga, komanso cuma canga kuti ndidziunjikile cuma kapena kodi ndimazisewenzetsa kuti ndikhale wolemela kwa Mulungu?’
14. Monga taonela m’citsanzo ca Miki, n’cifukwa ciyani m’pofunika kumasinkhasinkha umboni wa m’Malemba woonetsa kuti tikukhala m’masiku otsiliza?
14 Tingasinthe mmene timaonela zinthu pa umoyo tikaganizila maumboni oonetsa kuti tikukhala m’masiku otsiliza. Izi n’zimene zinacitika kwa mlongo wina dzina lake Miki. Iye anati: “N’tatsiliza sukulu, n’nali kufuna kucita maphunzilo apamwamba kuti ndikaphunzile za zinyama. Koma n’nalinso ndi colinga cotumikila monga mpainiya wa nthawi zonse komanso kukatumikila ku malo osowa. Komabe mabwenzi anga okhwima kuuzimu anandithandiza kuganizila mozama ngati zinalidi zotheka kwa ine kucita maphunzilo apamwamba kenako n’kudzakwanilitsa zolinga zanga zauzimu. Iwo anandikumbutsa kuti dongosolo lino la zinthu lidzatha posacedwa. Ndipo m’dziko latsopano ndidzakhala ndi nthawi yodzaphunzila za zinyama kwamuyaya. Conco n’nasankha kucita kosi imene siinanditengele nthawi yaitali. Izi zinandithandiza kupeza nchito imene inandithandiza kukhala ndi ndalama zocitila upainiya. Ndipo pambuyo pake n’napita ku dziko la Ecuador kukatumikila ku malo osowa.” Tsopano Miki ndi mwamuna wake akucita utumiki wa m’dela m’dziko limenelo.
15. Pelekani citsanzo coonetsa zimene anthu angacite pambuyo pa nthawi akalandila uthenga wabwino? (Onaninso zithunzi.)
15 Sitiyenela kufooka ngati anthu sakuonetsa cidwi mu uthenga wabwino. Anthu angasinthe. Ganizilani citsanzo ca Yakobo, m’bale wake wa Yesu. Iye anamuona Yesu akukula, akukhala Mesiya, komanso akuphunzitsa kuposa mmene munthu wina aliyense anacitila. Ngakhale n’telo, kwa zaka Yakobo sanakhale wotsatila wa Yesu. Koma pambuyo pakuti Yesu waukitsidwa, Yakobo anakhala wophunzila wake wokangalika kwambili.b (Yoh. 7:5; Agal. 2:9) Nkhaniyi itiphunzitsa kuti sitiyenela kuleka kukambilana ndi acibale athu kapena anthu ena amene sanaonetsebe cidwi mu uthenga wa Ufumu. Kumbukilani kuti tikukhala m’masiku otsiliza. Conco nchito yolalikila ndi yofunika kwambili. Zimene mumakambilana nawo palipano zingadzawafike pa mtima tsiku lina, ngakhale pambuyo pakuti cisautso cacikulu cayamba.c
N’ciyani cingatithandize kuti tisaleke kulalikila acibale athu amene si Mboni? (Onani ndime 15)e
MUSALEKE KUYAMIKILA ZIKUMBUTSO ZA YEHOVA
16. Kodi mwapindula motani ndi zikumbutso za Yehova? (Onaninso danga lakuti “Zigwilitseni Nchito Kuthandiza Ena.”)
16 Cina mwa cakudya cauzimu cimene timalandila cimakonzedwela anthu amene akalibe kumvapo ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. Mwacitsanzo, nkhani za onse, nkhani zina komanso mavidiyo a pa jw.org, komanso magazini athu ogawila, amakonzedwa makamaka kuti athandize anthu amene si Mboni. Komabe tonsefe timapindula ndi zikumbutso zimenezi. Zimatithandiza kukulitsa cikondi cathu pa Yehova, kulimbitsa cikhulupililo cathu m’Mawu ake, komanso kutithandiza kukhala aphunzitsi ogwila mtima pamene tikufotokozela ena ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo.—Sal. 19:7.
17. Ndi pa zocitika ziti pamene mungafunike kusinkhasinkha za ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo?
17 Kwa ena a ife amene takhala tikutumikila Yehova kwa nthawi yaitali timasangalala kwambili tikalandila kamvedwe katsopano kofotokoza coonadi ca m’Baibo. Koma timayamikilanso kwambili mfundo zoyambilila za coonadi zimene zinatikokela m’coonadi. Ngati nthawi ina tingayesedwe kuti titsatile maganizo athu m’malo mogonjela citsogozo ca gulu la Yehova, tingacite bwino modzicepetsa kukumbukila amene akutsogolela gulu lathu kuti ndi Mlengi wamphamvuyonse komanso wanzelu zakuya. Ngati ife kapena wokondedwa wathu akupilila mavuto enaake, tingacite bwino kukhala oleza mtima ndi kusinkhasinkha cifukwa cake Yehova walola kuti mavuto azicitika. Ndipo posankha mmene tingagwilitsile nchito nthawi yathu komanso zinthu zathu, tingacite bwino kukumbukila kuti tikukhala m’masiku otsiliza ndi kuti nthawi imene yatsalako kuti mapeto afike ndi yaifupi. Conco lekani kuti zikumbutso za Yehova zipitilize kutilimbikitsa, kutipatsa nzelu, komanso kutisonkhezela kuti tim’tumikilebe mokhulupilika.
NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka
a Onani nkhani yakuti “Mavuto Onse Adzatha Posachedwapa” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2007, mas. 21-25.
c Onani nkhani yakuti “Kodi Tidziŵapo Ciyani za Mmene Yehova Adzaweluzile Anthu M’tsogolo?” mu Nsanja ya Mlonda ya May 2024 mas. 8-13.
d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mkulu wapeleka maganizo, koma bungwe la akulu silinagwilizane nawo. Pambuyo pake, mkuluyo akuyang’ana kumwamba kodzala nyenyezi usiku, ndipo akuganizila kuzama kwa nzelu za Mlengi wathu ndi ukulu wake. Izi zam’thandiza kuti aziona maganizo ake moyenela.
e MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Pocita phunzilo la munthu mwini, mlongo akusinkhasinkha za umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiliza. Izi zamusonkhezela kutumila foni wacibale wake kuti amulalalikile.