MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWELENGA KWANU
Muziwelenga Kuti Mugawileko Ena
Kuwelenga kumatitsitsimula. Koma timapindula mokulilapo tikagawilako ena mfundo za coonadi zimene tapeza. Miyambo 11:25 imati: “Amene amatsitsimula ena nayenso adzatsitsimulidwa.”
Tikafotokozelako ena zimene tapeza, zimakhala zosavuta kwa ifeyo kukumbukila zimene tawelenga ndipo timazamitsanso cidziwitso cathu. Timakhala osangalala kugawilako ena mfundo zimene tapeza podziwa kuti zingawalimbikitse.—Mac. 20:35.
Yesani kucita izi: Mlungu ukubwelawu, yesani kupeza mpata wofotokozelako ena zimene mwaphunzila. Mungacite izi kwa wacibale wanu, kwa m’bale kapena mlongo wa mu mpingo mwanu, kwa mnzanu wa ku nchito kapena wa ku sukulu, kwa aneba anu, kapenanso kwa amene mungakumane nawo mu ulaliki. Yesani kufotokoza zimenezo m’mawu anuanu, m’njila yosavuta kumva, komanso momveka bwino.
Kumbukilani: Muzigawilako ena zimene mwaphunzila n’colinga cowalimbikitsa osati pofuna kudzionetsela.—1 Akor. 8:1.