NKHANI YOPHUNZIRA 32
NYIMBO 38 Adzakulimbitsa
Mmene Yehova Amatithandizira Kupirira
“Mulungu yemwe amatisonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu . . . adzakupatsani mphamvu, adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika, komanso adzakulimbitsani.”—1 PET. 5:10.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Zimene Yehova watipatsa pofuna kutithandiza kupirira komanso zimene tingacite kuti tipindule nazo.
1. N’cifukwa ciani tifunika kupirira? Nanga ndi thandizo lotani limene tili nalo? (1 Petulo 5:10)
M’MASIKU otsiriza ano obvuta, anthu a Yehova amafunika kupirira. Ena akudwala matenda osapolerapo msanga. Ena ali ndi cisoni cifukwa cotayikiridwa okondedwa ao mu imfa. Kuonjezera apo, ena akukumana ndi citsutso kucokera ku boma kapena kwa a m’banja lao. (Mat. 10:18, 36, 37) Musakaikire kuti Yehova adzakuthandizani kupirira zobvuta zilizonse zimene inu mukukumana nazo.—Werengani 1 Petulo 5:10.
2. Kodi Mkhristu amadalira ndani kuti apirire?
2 Kupirira kumatanthauza kukhalabe olimba ndi kusungabe ciyembekezo cakuti zinthu zidzakhala bwino tikakumana ndi mabvuto, tikamazunzidwa, komanso tikamakumana ndi mayeso kapena mayesero. Mkhristu samadalira mphamvu zake kuti apirire. M’malomwake, amadalira Yehova amene amatipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akor. 4:7) M’nkhani ino, tikambirana njira zinai zimene Yehova watipatsa pofuna kutithandiza kuti tipirire. Ndipo tionanso zimene tingacite kuti tipindule ndi njira zimenezi.
PEMPHERO
3. N’cifukwa ciani tingati pemphero ndi cozizwitsa?
3 Yehova wapanga makonzedwe ozizwitsa amene angatithandize kupirira. Iye wacititsa kuti zikhale zotheka kuti tizilankhula naye, ngakhale kuti ndife ocimwa. (Aheb. 4:16) Tangoganizirani: Tingapemphere kwa Yehova nthawi ina iliyonse ndipo tingamuuze ciliconse. Iye angamve pemphero m’cinenero ciliconse, ndipo angatimvetsere kulikonse kumene tingakhale, kaya tili kwatokha kapena tili m’ndende. (Yona 2:1, 2; Mac. 16:25, 26) Ngati nkhawa yatikulira ndipo tikulephera kufotokoza mmene tikumvera, Yehova amadziwa zimene tikufuna kulankhula. (Aroma 8:26, 27) Zoonadi, pemphero ndi cozizwitsa!
4. N’cifukwa ciani tingakambe kuti mapemphero athu opempha Yehova kuti atithandize kupirira ndi ogwirizana n’cifuniro cake?
4 Kudzera m’Mau ake, Yehova amatitsimikizira kuti “ciliconse cimene tingamupemphe mogwirizana ndi zimene amafuna, amatimvera.” (1 Yoh. 5:14) Kodi Yehova angayankhe pemphero lotithandiza kupirira? Inde! Zili conco cifukwa n’zogwirizana n’cifuniro cake. N’cifukwa ciani tikutero? Tikamapirira mayeso, timapangitsa kuti Yehova ayankhe Satana Mdyerekezi amene amamunyoza. (Miy. 27:11) Kuonjezera apo, Baibo imakamba kuti Yehova ndi wofunitsitsa ‘kuonetsa mphamvu zake kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.’ (2 Mbiri 16:9) Conco sitikaikira kuti Yehova ali ndi mphamvu komanso cifuno cakuti atithandize kuti tipirire.—Yes. 30:18; 41:10; Luka 11:13.
5. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kukhala ndi mtendere wa mu mtima? (Yesaya 26:3)
5 Baibo imatiuza kuti tikamacita khama kupemphera pa zinthu zimene zimatibvutitsa, “mtendere wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima [yathu] ndi maganizo [athu].” (Afil. 4:7) Ndipo uwu ndi mwai waukulu. Anthu amene satumikira Yehova naonso amakumana ndi zobvuta, ndipo amayesa njira zosiyana-siyana kuti apeze mtendere wa mu mtima. Mwacitsanzo, ena amakhala phee n’kusinkhasinkha kuti acotse zimene zili m’maganizo mwao kuphatikizapo nkhawa zao. Koma kucita zimenezi n’koopsya mwauzimu. (Yerekezerani ndi Mateyu 12:43-45.) Ngakhale kuti anthu amagwiritsa nchito njira ngati zimenezi kuti apeze mtendere wa mu mtima, iwo sakhala ndi mtendere weniweni wocokera kwa Yehova, womwe umaposa wina ulionse. Tikamapemphera kwa Yehova, timaonetsa kuti timam’dalira ndi mtima wonse ndipo amatipatsa “mtendere wosatha.” (Werengani Yesaya 26:3.) Njira imodzi imene Yehova amacitira zimenezi ndi kutithandiza kukumbukira mfundo zokhazika mtima pansi za coonadi zimene tinaphunzira m’Mau ake. Mfundo za coonadi zimenezi zimakhazika mtima wathu pansi cifukwa tidziwa kuti Yehova amasamala za ife komanso amafuna kuti tikhale ndi umoyo wabwino.—Sal. 62:1, 2.
6. Kodi mungacite ciani kuti mupindule mokwanira ndi pemphero? (Onaninso cithunzi.)
6 Zimene mungacite. Pamene mukupirira zinthu zoyesa cikhulupiriro canu, ‘muzitulira Yehova nkhawa zanu’ kuti akupatseni mtendere wa mu mtima. (Sal. 55:22) Muzimupemphanso kuti akupatseni nzeru kuti mukwanitse kuthana ndi mabvuto amene mukukumana nao. (Miy. 2:10, 11) Kuonjezera pa kum’conderera kuti akuthandizeni kupirira, musamaiwale kuikamo mau oyamikira m’mapemphero anu. (Afil. 4:6) Muziganizira njira zimene Yehova akukuthandizirani tsiku lililonse kuti mupirire, ndipo muziyamikira thandizo lake komanso zabwino zimene akukupatsani. Musalole mayesero amene mukukumana nao kukuphimbani m’maso n’kukupangitsani kuti musaone madalitso amene muli nao kale.—Sal. 16:5, 6.
Mukamapemphera, mumalankhula ndi Yehova. Yehova amalankhula nanu mukamawerenga Baibo (Onani ndime 6)b
MAU A MULUNGU
7. Kodi kuwerenga Baibo kungatithandize motani kupirira?
7 Yehova watipatsa Mau ake kuti atithandize kupirira. M’Baibo muli mau ambiri amene amatitsimikizira kuti Yehova adzatithandiza. Onankoni citsanzo cimodzi ici. Mateyu 6:8 imati: “Atate wanu amadziwa zimene mukufunikira musanam’pemphe nʼkomwe.” Yesu ndiye anakamba mau amenewa, ndipo amam’dziwa bwino Yehova kuposa wina aliyense. Conco, tilibe cifukwa cokaikirira kuti Yehova amasamala za ife pamene tikukumana ndi zobvuta. M’Baibo muli mavesi ambiri amene ali ndi mfundo imeneyi omwe angatithandize kupirira.—Sal. 94:19.
8. (a) Perekani citsanzo ca mfundo ya m’Baibo imene ingatithandize kupirira. (b) Tikafunikira mfundo za m’Baibo, n’ciyani cingatithandize kuzikumbukira?
8 Mfundo za m’Baibo zingatithandize kupirira. Mfundozo zili ndi nzeru zimene zingatithandize kupanga zisankho zabwino. (Miy. 2:6, 7) Mwacitsanzo, imodzi mwa mfundo za m’Baibo imatilimbikitsa kuti tisamadere nkhawa za mawa koma kuti tizidalira Yehova nthawi zonse. (Mat. 6:34) Ngati tili ndi cizolowezi cowerenga Malemba ndi kuwasinkhasinkha, zidzakhala zosabvuta kukumbukira mfundo zimene zingatithandize tikakumana ndi mabvuto.
9. Kodi zitsanzo za m’Baibo zimalimbitsa bwanji cidaliro cathu cakuti Yehova adzatithandiza?
9 M’Baibo mumapezekanso zocitika zenizeni za anthu amene anadalira Yehova ndi kulandira thandizo lake. (Aheb. 11:32-34; Yak. 5:17) Tikamaganizira zitsanzo zimenezi, timalimbitsa cidaliro cathu cakuti Yehova “Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosabvuta pa nthawi ya mabvuto.” (Sal. 46:1) Tikamaganizira zitsanzo za kukhulupirika kwa atumiki a Yehova, tidzalimbikitsidwa kutengera cikhulupiriro ndi kupirira kwao.—Yak. 5:10, 11.
10. Kodi mungacite ciani kuti muzipindula mokwanira ndi Mau a Mulungu?
10 Zimene mungacite. Muziwerenga Baibo tsiku lililonse ndi kusunga mavesi amene muona kuti ndi othandiza kwambiri kwa inu. Ambiri apeza kuti kucita lemba la tsiku m’mawa kumawathandiza kukhala ndi mfundo inayake ya m’Baibo imene angaganizirepo kwa tsiku lonse. Mlongo wina dzina lake Mariea anaona mfundoyi kukhala yoona pomwe makolo ake anapezeka ndi khansa. N’ciani cinamuthandiza kupirira pomwe anali kuwadwazika atatsala pang’ono kumwalira? Iye anati: “M’mawa mulimonse n’nali kuwerenga ndi kusinkhasinkha lemba la tsiku m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku. Izi zinali kundithandiza kuganizira kwambiri za Yehova komanso zinthu zabwino zimene amatiphunzitsa m’Mau ake m’malo moganizira kwambiri mabvuto amene n’nali nao.”—Sal. 61:2.
OKHULUPIRIRA ANZATHU
11. N’cifukwa ciani n’zolimbikitsa kudziwa kuti sindife tokha amene tikupirira mayeso?
11 Yehova watipatsa apaubale wathu kuzungulira dziko lonse kuti azitithandiza kupirira. Kudziwa kuti “abale [athu] padziko lonse akukumananso ndi mabvuto” ngati athu, kumatitsimikizira kuti sitili tokha. (1 Pet. 5:9) Ndithudi, zobvuta zilizonse zimene tingakumane nazo, abale athu ena anakumanapo nazo kale ndipo anapirira. Izi zionetsa kuti nafenso tingathe kupirira!—Mac. 14:22.
12. Kodi okhulupirira anzathu angatithandize motani? Nanga n’ciani cimene tingacite kuti tiwathandize? (2 Akorinto 1:3, 4)
12 Pamene tikupirira, okhulupirira anzathu angatithandize. Izi n’zimene zinacitika kwa mtumwi Paulo. Nthawi zambiri iye anali kuyamikira amene anam’thandiza pomwe anali pa ukaidi wosacoka pa nyumba mwa kuwachula maina ao. Iwo anali kum’tonthoza, kum’limbikitsa, komanso kum’patsa zimene anali kufunikira. (Afil. 2:25, 29, 30; Akol. 4:10, 11) Nafenso zaconco zingaticitikire masiku ano. Tikafunikira thandizo kuti tipirire, abale ndi alongo alipo kuti atithandize ndipo akafunikira thandizo, ifenso tilipo kuti tiwathandize.—Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.
13. N’ciani cinathandiza mlongo Maya kupirira?
13 Abale ndi alongo athu anam’limbikitsa kwambiri mlongo wathu wa ku Russia dzina lake Maya. Mu 2020, apolisi anapita kukafufuza m’nyumba mwake, ndipo anam’patsa mlandu cifukwa couzako ena zimene amakhulupirira. Iye anati: “Pa nthawi imeneyo, ndinali wofooka, wankhawa, komanso wacisoni. Koma abale ndi alongo anali kunditsimikizira kuti amandikonda kudzera pa foni, m’makalata, komanso m’mameseji. Kumbuyo konseku n’nali kudziwa kuti abale ndi alongo amandikonda komanso kuti ndiwo banja langa. Koma kucokera mu 2020, ndaona umboni wa zimenezi.”
14. Tingacite ciani kuti tipindule ndi thandizo la okhulupirira anzathu pamene tikupirira mabvuto? (Onaninso cithunzi.)
14 Zimene mungacite. Pamene mukupirira mabvuto enaake, musatalikirane nao Akhristu anzanu. Musazengereze kupempha thandizo kwa akulu. Iwo angakhale ngati “malo obisalirapo mphepo, malo othawirapo mvula yamkuntho.” (Yes. 32:2, mawu a m’munsi.) Muzikumbukiranso kuti Akhristu anzanu naonso akupirira mabvuto enaake. Mukacitira zabwino munthu winawake amene akufunikira thandizo, zidzacititsa kuti mukhale wacimwemwe ndipo zingakuthandizeni kuti mupirire mabvuto anu.—Mac. 20:35.
Musatalikirane nao abale ndi alongo anu (Onani ndime 14)c
CIYEMBEKEZO CATHU
15. Kodi ciyembekezo cinam’thandiza bwanji Yesu kupirira? Nanga kodi nafenso cimatithandiza motani? (Aheberi 12:2)
15 Yehova watipatsa ciyembekezo cotsimikizika cimene cimatithandiza kupirira. (Aroma 15:13) Kumbukirani mmene ciyembekezo cinathandizira Yesu ali padziko lapansi kuti apirire tsiku lake lowawa koposa. (Werengani Aheberi 12:2.) Iye anadziwa kuti kukhulupirika kwake kudzacititsa kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. Yesu anali kuyembekezera mwacidwi kukhaliranso limodzi ndi Atate wake. Ndipo anali kuyembekezeranso nthawi pamene anali kudzakhala Mfumu ndi kudzalamulira limodzi ndi abale ake odzodzedwa. Mofananamo, ciyembekezo cathu codzakhala kwamuyaya m’dziko latsopano, cimatithandiza kupirira mabvuto alionse amene tingakumane nao m’dziko la Satanali.
16. Kodi ciyembekezo cimam’thandiza motani mlongo Alla kupirira? Ndipo mwaphunzirapo ciani pa zimene anakamba?
16 Onani mmene ciyembekezo codzakhala m’dziko latsopano cinathandizira mlongo wa ku Russia dzina lake Alla, amene mwamuna wake anamangidwa poyembekezera kuzengedwa mlandu. Izi zitacitika, Alla anati: “Kupempherera za ciyembekezo cathu ca zamtsogolo komanso kusinkhasinkha za ciyembekezoco kumandithandiza kuti ndisakhale wofooka kwambiri. Ndimadziwa kuti mabvutowa si mapeto a zonse. Yehova adzagonjetsa adani ake ndipo adzatipatsa mphoto.”
17. Tingaonetse bwanji kuti timayamikira ciyembekezo cathu cozikika m’Baibo? (Onaninso cithunzi.)
17 Zimene mungacite. Muzipatula nthawi yoganizira za tsogolo labwino limene Yehova watisungira. Muzidziona kuti muli m’dziko latsopano la Mulungu ndipo mukusangalala ndi madalitso amene tidzakhala nawo. Mayeso alionse amene tikukumana nao palipano adzaoneka “akanthawi komanso aang’ono” tikawayerekezera ndi madalitso amene tikuyembekezera m’tsogolo. (2 Akor. 4:17) Kuonjezera apo, muzicita zonse zimene mungathe kuti muziuzako ena zimene mumakhulupirira. Ganizirani mmene umoyo ulili wobvuta kwa anthu amene satumikira Yehova. Naonso amakumana ndi mabvuto ambiri, koma iwo sadziwa zinthu zosangalatsa zimene Yehova watilonjeza. Ngakhale mutakambirana nao kwa nthawi yocepa, mungadzutse cidwi cao cofuna kumva zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu ndi malonjezo amene udzabweretsa.
Muzipatula nthawi yosinkhasinkha za tsogolo losangalatsa limene Yehova wakusungirani (Onani ndime 17)d
18. N’ciani cimatithandiza kukhulupirira malonjezo a Yehova?
18 Pambuyo popirira mayeso ambiri, Yobu anauza Yehova kuti: “Tsopano ndadziwa kuti inu mumatha kucita zinthu zonse, ndiponso kuti palibe ciliconse cimene mukufuna kucita cimene simungakwanitse.” (Yobu 42:2) Yobu anaphunzira kuti kulibe cingalepheretse Yehova kukwaniritsa cifuniro cake. Mfundo yoona imeneyi ingatilimbikitse pamene tikupirira. Mwacitsanzo, tiyerekeze kuti mzimai wina wakhala akudwala kwa nthawi yaitali. Iye anatairatu ciyembekezo cakuti adzacira cifukwa cakuti wakhala akupita kwa madokotala ambiri koma sakupeza thandizo. Ndiye tinene kuti wapeza dokotala waluso komanso wodalirika amene akudziwa cimene cikum’dwalitsa ndipo akum’fotokozera mmene adzam’thandizira. Kodi mzimaiyo adzamva bwanji? Adzasangalala ngakhale kuti akudziwa kuti padzatengako nthawi kuti acire. Iye tsopano adzapirira matenda ake podziwa kuti tsogolo lake n’lowala cifukwa ca ciyembekezo cakuti adzacira. Mofananamo, tingapitirize kupirira cifukwa ndife otsimikiza kuti lonjezo la Mulungu la Paradaiso lidzakwaniritsika.
19. Tifunikira zinthu ziti kuti tipirire?
19 Monga taonera, Yehova amatithandiza kupirira mayeso kupitira m’pemphero, m’Mau ake, mwa okhulupirira anzathu, komanso m’ciyembekezo cathu. Tikamagwiritsa nchito njira zimenezi mokwanira, Yehova adzatithandiza kupirira mabvuto alionse amene tingakumane nao mpaka pamene adzacotsapo mabvuto a m’dziko la Satanali.—Afil. 4:13.
NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako
a Maina ena asinthidwa m’nkhani ino.
b MAU OFOTOKOZERA CITHUNZI: M’bale wacikulire akupirira mokhulupirika kwa zaka zambiri.
c MAU OFOTOKOZERA CITHUNZI: M’bale wacikulire akupirira mokhulupirika kwa zaka zambiri.
d MAU OFOTOKOZERA CITHUNZI: M’bale wacikulire akupirira mokhulupirika kwa zaka zambiri.