NKHANI YOPHUNZIRA 34
NYIMBO 3 Ndimwe Mphamvu zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu
Muzikhulupirira Kuti Yehova Anakukhululukirani
“Inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi macimo anga.”—SAL. 32:5.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Cifukwa cake tiyenera kukhulupirira kuti Yehova anatikhululukira komanso mmene Baibo imatitsimikizira kuti iye amakhululukira ocimwa amene alapa.
1-2. Kodi timamva bwanji Yehova akatikhululukira macimo athu? (Onaninso cithunzi .)
MFUMU Davide anali kudziwa mmene zimamvekera kukhala ndi cikumbumtima cobvutitsidwa kaamba ka macimo amene wacita. (Sal. 40:12; 51:3; tumau twapamwamba) Iye anacitapo macimo akulu-akulu mu umoyo wake. Ngakhale n’tero, iye analapa mocokera pansi pa mtima, ndipo Yehova anam’khululukira. (2 Sam. 12:13) Kaamba ka ici, Davide anakhala wacimwemwe podziwa kuti Yehova wam’khululukira.—Sal. 32:1.
2 Monga zinalili kwa Davide, ifenso timakhala ndi cimwemwe Yehova akaticitira cifundo ndi kutikhululukira macimo athu. N’zokhazika mtima pansi kudziwa kuti Yehova nthawi zonse ndi wokonzeka kutikhululukira macimo athu ngakhale aja akulu-akulu, malinga ngati talapa mocokera pansi pa mtima, taulula macimo athu, ndi kuyesetsa kuti tisakabwerezenso zolakwazo. (Miy. 28:13; Mac. 26:20; 1 Yoh. 1:9) N’zokhazikanso mtima pansi kudziwa kuti iye akakhululuka, amatero ndi mtima wonse moti zimakhala ngati chimolo silinacitike.—Ezek. 33:16.
Mfumu Davide analemba masalimo ambiri onena za kukhululuka kwa Yehova (Onani ndime 1-2)
3-4. Kodi mlongo wina anamva bwanji atabatizika? Nanga tikambirana ciani m’nkhani ino?
3 Koma nthawi zina, ena zimawabvuta kukhulupirira kuti Yehova anawakhululukira. Citsanzo pa nkhaniyi ndi Jennifer amene anakulira m’banja la Mboni. Ali mtsikana, iye anayamba kucita zinthu zoipa ndipo anali kuwabisa makolo ake. Patapita zaka, anabwerera kwa Yehova ndipo anabatizika. Iye anati: “Ndisanabatizike, umoyo wanga unali wodzala ndi makhalidwe oipa monga ciwerewere, kumwa kwambiri, ndi kukonda kwambiri cuma. Ndipo ndinali waukali kwambiri. Ndinali kudziwa zimene Baibo imanena kuti nsembe ya Khristu imapangitsa kuti Yehova atikhululukire. Koma ndinali kukaikirabe zakuti Yehova anandikhululukira ngakhale kuti ndinalapa ndi kum’conderera kuti andikhululukire.”
4 Kodi nanunso nthawi zina zimakubvutani kukhulupiriradi kuti Yehova anakukhululukirani macimo amene munacita kumbuyo? Yehova samafuna kuti tizikhala ndi mantha cifukwa ca macimo amene tinacita, koma amafuna kuti tizikhulupirira kuti anatikhululukira monga anacitira ndi Davide. M’nkhani ino, tikambirana cifukwa cake tiyenera kukhulupirira kuti Yehova anatikhululukira komanso zimene zingatithandize kucita zimenezo.
N’CIFUKWA CIANI TIYENERA KUKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA ANATIKHULULUKIRA?
5. Kodi Satana amafuna kuti tizikhulupirira ciani? Perekani citsanzo.
5 Tikabvomereza kuti Yehova anatikhululukira, timapewa kugwera mu msampha wa Satana. Muzikumbukira kuti Satana adzacita zilizonse zotheka kuti atilepheretse kutumikira Yehova. Amacita zimenezi mwa kutipangitsa kukhulupirira kuti macimo athu sangakhululukidwe. Ganizirani zimene zinacitikira munthu wa ku Korinto amene anacotsedwa mu mpingo cifukwa ca ciwerewere. (1 Akor. 5:1, 5, 13) Mwamunayo atalapa, Satana anali kufuna kuti abale ndi alongo amucite nkhanza munthuyo mwa kupewa kumukhululukira ndi kumulandiranso mu mpingo. Pa nthawi imodzi-modziyo, Satana anali kufuna kuti munthu wolapayo azimva kuti sangakhululukidwe. Izi zikanapangitsa munthuyo kukhala ndi “cisoni copitirira malire mpaka kutaya mtima” moti akanasiya kutumikira Yehova. Ngakhale masiku ano, Satana amafuna kuti tizikhulupirira kuti macimo athu sangakhululukidwe. Koma “tikudziwa bwino ziwembu zake.” Conco tikudziwa mocitira naye.—2 Akor. 2:5-11.
6. Tingacite ciani kuti tileke kudziimba mlandu pa macimo amene tinacita?
6 Tikamakhulupirira kuti Yehova anatikhululukira, tingakhalenso acimwemwe ndi kupewa kudziimba mlandu. Tikacimwa, mwacibadwa timadziimba mlandu. (Sal. 51:17) Zimenezo si zolakwika. Cikumbumtima cathu cingatisonkhezere kuti titenge masitepe ofunikira kuti tikonze zimene zinalakwika. (2 Akor. 7:10, 11) Koma ngati tapitiriza kudziimba mlandu pambuyo pakuti talapa, tingaleke kutumikira Yehova. Tikabvomereza kuti Yehova anatikhululukira, tingaleke kudziimba mlandu. Kenako tingam’tumikire Yehova tili ndi cikumbumtima coyera komanso tili ndi cimwemwe coculuka. (Akol. 1:10, 11; 2 Tim. 1:3) Ndiye tingautsimikizire motani mtima wathu kuti Mulungu anatikhululukira?
N’CIANI CINGATITHANDIZE KUBVOMEREZA KUTI YEHOVA ANATIKHULULUKIRA?
7-8. Kodi Yehova anadzifotokoza motani kwa Mose? Nanga zimenezo ziyenera kutitsimikizira ciani? (Ekisodo 34:6, 7)
7 Muzisinkhasinkha mmene Yehova anadzifotokozera m’Mau ake. Mwacitsanzo, onani mmene Yehova anadzifotokozera kwa Mose pa Phiri la Sinai.a (Werengani Ekisodo 34:6, 7.) Ngakhale kuti Yehova ali ndi makhalidwe ambiri abwino, iye anaona kuti m’poyenera kudzifotokoza kuti ndi “Mulungu wacifundo ndi wokoma mtima.” Kodi Mulungu wotero angalephere kukhululukira mlambiri wake amene walapadi macimo ake? Ai! Kucita zimenezo kungakhale kupanda cifundo komanso kuipa mtima, omwe ndi makhalidwe amene Yehova alibe.
8 Ndife otsimikiza kuti pomwe Yehova ananena kuti ndi wacifundo, ndiye kuti ndi mmene alilidi, cifukwa iye sanganame. (Sal. 31:5) Conco tiyenera kukhulupirira zimene amakamba m’Mau ake. Ngati zimakubvutani kuleka kudziimba mlandu pa macimo amene munacita kumbuyo, mungacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupiriradi kuti Yehova ndi Mulungu wacifundo komanso wokoma mtima ndi kuti sangalephere kukhululukira wocimwa aliyense amene walapa? Ndiye kodi sindiyenera kukhulupirira kuti iye anandikhululukiradi?’
9. Kodi Salimo 32:5 imatiphunzitsa ciani za mmene Yehova amakhululukira macimo athu?
9 Muziganizira zimene Baibo imatiphunzitsa za kukhululuka kwa Yehova. Mwacitsanzo, onani zimene Davide analemba zokhudza kukhululuka kwa Yehova. (Werengani Salimo 32:5.) Davide analemba kuti, “Inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi macimo anga.” Mau aciheberi amene anawamasulira kuti “kukhululukira” pa vesili, angatanthauzenso “kunyamula” kapena “kucotsa.” Pamene Yehova anakhululukira Davide, zinali ngati Yehova wanyamula macimowo n’kuwacotsa. Conco Davide anamva kupepukidwa Yehova atam’khululukira macimo ake, zomwe zinali ngati wamutula katundu wolemera n’kuucotsa. (Sal. 32:2-4) Izi zingacitikenso kwa ife. Tikalapa macimo athu, sitiyenera kupitiriza kunyamula katundu wolemera mwa kudziimba mlandu pa macimo amene Yehova anawanyamula n’kuwacotsa pa ife.
10-11. Kodi mau akuti “wokonzeka kukhululuka” amatiphunzitsa ciani za Yehova? (Salimo 86:5)
10 Werengani Salimo 86:5. Davide pa lembali anafotokoza kuti Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka.” Izi zitanthauza kuti Yehova sakwiya msanga tikalakwitsa zinazake, ndipo nthawi zonse ndi wokonzeka kukhululukira aliyense amene walapa. N’cifukwa ciani amacita zimenezo? Mbali yotsatira ya Salimo 86:5 imati: “Mumasonyeza cikondi cokhulupirika coculuka kwa onse amene amaitana inu.” Monga tinaphunzirira m’nkhani yapita, cikondi cokhulupirika cimasonkhezera Yehova kukhala pa ubale wolimba ndi alambiri ake okhulupirika. Conco cikondi cake cokhulupirika n’cimene cimam’sonkhezera ‘kukhululukira ndi mtima wonse’ ocimwa onse amene alapa. (Yes. 55:7) Ngati zimakubvutani kukhulupirira kuti Mulungu anakukhululukirani, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakhulupirira kuti Yehova ndi wokonzeka kukhululukira wocimwa aliyense amene amam’pempha kuti am’citire cifundo? Kodi inenso sindiyenera kukhulupirira kuti iye anandikhululukira pomwe ndinam’conderera kuti andicitire cifundo?’
11 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa kuti ndife opanda ungwiro. (Sal. 139:1, 2) Davide anaimveketsa bwino mfundoyi mu salimo lina limene analemba ndipo mau ake angatithandize kukhulupirira kuti Yehova anatikhululukira.
MUSAMAIWALE ZIMENE YEHOVA AMAKUMBUKIRA
12-13. Malinga ndi Salimo 103:14, kodi Yehova amakumbukira ciani? Nanga kodi zimenezo zimam’sonkhezera kucita ciani?
12 Werengani Salimo 103:14. Davide ananena kuti Yehova “amakumbukira kuti ndife fumbi.” Ponena mauwa, iye anachula cimodzi mwa zifukwa zimene zimapangitsa Yehova kukhululukira alambiri ake amene alapa. Iye nthawi zonse amakumbukira kuti ndife ocimwa. Kuti timvetse bwino zimenezi, tiyeni tiwakambirane mwacifatse mau a Davide amenewa.
13 Davide anakamba kuti Yehova “amadziwa bwino mmene anatipangira.” Iye anapanga munthu wangwiro Adamu “kucokera ku dothi” ndipo anali kudziwa bwino zimene munthu wangwiroyo anali kufunikira kuti akhalebe ndi moyo. Mwacitsanzo, iye anali kufunikira kudya, kugona, komanso kupuma. (Gen. 2:7) Koma cifukwa cakuti Adamu ndi Hava anacimwa, mau akuti “ndife fumbi” amaonetsanso kuti tili ndi zofooka cifukwa ca ucimo umene tinatengera kwa iwo. Ucimowo umapangitsa kuti tikhale ndi mtima wolakalaka kucita zoipa. Kuonjezera pa kukamba kuti Yehova amadziwa bwino kuti ndife ocimwa, Davide anaonjezeranso kuti Iye “amakumbukira” zimenezo. Mau aciheberi amene anawamasulira kuti “amakumbukira,” amapereka lingaliro lakuti Yehova amacita nafe mwacifundo tikacimwa. Conco mwacidule, Davide anali kutanthauza kuti Yehova amamvetsa tikam’cimwira. Ndipo tikalapa mocokera pansi pa mtima, Iye amaticitira cifundo ndi kutikhululukira.—Sal. 78:38, 39.
14. (a) Kodi Davide anakamba kuti n’ciani cimacitika Yehova akatikhululukira macimo athu? (Salimo 103:12) (b) Kodi tiphunzirapo ciani tikaona mmene Yehova anakhululukira Davide? (Onaninso danga lakuti “Yehova Amakhululuka komanso Kuiwala Macimo.”)
14 N’cianinso cina cimene tingaphunzire mu Salimo 103 cokhudza kukhululuka kwa Yehova? (Werengani Salimo 103:12.) Davide anakamba kuti Yehova akakhululuka, amaika macimo athu kutali ndi ife “mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa [kum’mawa] kwatalikirana ndi kolowera dzuwa [kumadzulo].” Kum’mawa ndi kotalikirana kwambiri ndi kumadzulo. Ndipo n’zosatheka malo awiriwa kuyandikirana. Kodi mfundoyi ionetsa kuti n’ciani cimacitika Yehova akatikhululukira? Yehova akatikhululukira, zimakhala ngati watenga macimo athu n’kuwataira kutali kwambiri ndi ife. Amawataira kutali kwambiri moti palibe ciliconse cingam’pangitse kuwakumbukira, kutikumbutsa za macimowo, kutiimba nao mlandu kapena kutilanga cifukwa ca macimowo.—Ezek. 18:21, 22; Mac. 3:19.
15. Tiyenera kucita ciani ngati nthawi zonse timadziimba mlandu pa zimene tinalakwitsa kumbuyo?
15 Kodi mau a Davide a mu Salimo 103 angatithandize bwanji kukhulupirira kuti Yehova anatikhululukira? Ngati nthawi zonse timadziimba mlandu pa macimo amene tinacita kumbuyoku, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuiwala kuti Yehova amakumbukira kuti ndine wocimwa ndi kuti adzakhululukira munthu amene walapa monga ine? Kodi ndimakumbukira macimo amene Yehova anawakhululuka ndipo anawaiwala moti sangandilange cifukwa ca macimowo?’ Yehova samangokhalira kuganizira zolakwa zimene tinacita kumbuyo. N’zimene nafenso tiyenera kucita. (Sal. 130:3) Tikakhulupirira kuti Yehova anatikhululukiradi, tidzaleka kudziimba mlandu ndipo tidzapitiriza kum’tumikira tili acimwemwe.
16. Perekani citsanzo coonetsa ngozi imene ingakhalepo ngati timangokhalira kuganizira za macimo amene tinacita kumbuyo. (Onaninso cithunzi.)
16 Ganizirani citsanzo ici. Munthu akamayendetsa galimoto, angayang’aneko pa galasi loyang’anira zinthu zakumbuyo kuti aone zimene zikubwera kumbuyo kwake. Iye angamacite zimenezi mwa apa ndi apo. Koma zingakhale zoopsya kwambiri ngati iye wangokhalira kuyang’ana pa galasiyo. Kuti asacite ngozi, ayenera kupitiriza kuyang’ana kutsogolo kumene akupita. Mofananamo, nthawi zina zimakhala bwino kuganizira za zolakwa zimene tinacita kumbuyoku kuti titengepo phunziro ndi kupewa kuzibwereza. Koma ngati nthawi zonse timangokhalira kuganizira za zolakwa zimene tinacita kumbuyo n’kumaganiza kuti Yehova sanatikhululukire, tingaleke kum’tumikira mwacimwemwe. Conco tiyeni tipitirize kuika maganizo athu pa kutumikira Yehova ndi kuganizira za tsogolo limene Iye watilonjeza pomwe zinthu zoipa “sizidzakumbukiridwanso.”—Yes. 65:17; Miy. 4:25.
Dalaivala ayenera kuyang’ana kwambiri kutsogolo osati kumbuyo. Nafenso tifunika kuganizira kwambiri za kutsogolo osati zimene tinalakwitsa kumbuyo (Onani ndime 16)
PITIRIZANI KUTSIMIKIZIRA MTIMA WANU
17. N’cifukwa ciani tiyenera kupitiriza kutsimikizira mtima wathu kuti Yehova amatikonda komanso kuti anatikhululukira?
17 Tiyenera kupitiriza kutsimikizira mtima wathu kuti Yehova amatikonda komanso kuti anatikhululukira. (1 Yoh. 3:19) N’cifukwa ciani tiyenera kukhulupirira zimenezo? Satana sadzaleka kutipangitsa kukhulupirira kuti Yehova satikonda komanso kuti sangatikhululukire. Colinga cake n’cofuna kutilepheretsa kutumikira Yehova. Tikudziwa kuti Satana adzaonjezera khama lake pocita zimenezi cifukwa akudziwa bwino kuti nthawi yamutsalira yocepa. (Chiv. 12:12) Koma tisamulole kuti apambane!
18. Mungacite ciani kuti mutsimikizire mtima wanu kuti Yehova amakukondani komanso kuti anakukhululukirani?
18 Kuti mulimbikitse cidaliro canu cakuti Yehova amakukondani, mungacite bwino kugwiritsa nchito mfundo zimene tinakambirana m’nkhani yapita. Kuti mutsimikizire mtima wanu kuti Yehova anakukhululukirani, sinkhasinkhani za mmene Yehova anadzifotokozera m’Mau ake. Muzipatula nthawi yosinkhasinkha mmene Baibo imafotokozera mmene Iye amakhululukira. Musamaiwale kuti Iye amadziwa bwino kuti ndinu wocimwa ndi kuti adzacita nanu mwacifundo. Ndipo muzikumbukiranso kuti Iye akakukhululukirani, amacita zimenezo ndi mtima wonse. Ndiyeno ndi cidaliro cofanana ndi cimene Davide anali naco cakuti Yehova ndi wacifundo, mudzatha kunena kuti, “Zikomo Yehova pondikhululukira ‘zolakwa zanga ndi macimo anga’!”—Sal. 32:5.
NYIMBO 1 Makhalidwe a Yehova
a Onani nkhani yakuti “Yandikirani Mulungu—Yehova Anafotokoza Makhalidwe Ake” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2009.