MFUNDO YOTHANDIZA PA KUWERENGA KWANU
Pindulani ndi Danga la Malifalensi
Danga la malifalensi ya mu Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano limaonetsa kugwirizana kwa uthenga wa m’Baibo mwa kuonetsa malemba ena ofotokoza mfundo zina zokhudza nkhani imene mukuwerenga. Malifalensi olozera ku malemba ena amaonetsedwa ndi kacilembo kakang’ono kamene kamapezeka patsogolo pa liu. Ngati mugwiritsa nchito Baibo yopulintidwa, muzipeza kacilembo kofanana ndi kamene munapeza kutsogolo kwa liu m’danga lapakati kuti mupeze malemba ena ogwirizana ndi nkhaniyo. Pa jw.org kapena mu JW Library®, dinizani pa kacilembo kuti mupeze malifalensi a malemba.
Malifalensi a m’danga lapakati angakuthandizeni kuti mupeze zotsatirazi komanso zina:
Nkhani yofanana: Lifalensi limeneli limakuperekani ku malemba ena amene ali ndi nkhani imodzi-modzi. Mwacitsanzo, onani 2 Samueli 24:1 ndi 1 Mbiri 21:1.
Malemba ogwidwa mau: Lifalensi limeneli limaonetsa malemba ena kumene mau anatengedwako. Mwacitsanzo, onani Mateyu 4:4 ndi Deuteronomo 8:3.
Kukwaniritsidwa kwa ulosi: Ili ndi lifalensi limene limaonetsa lemba lofotokoza ulosi komanso kukwaniritsidwa kwake. Mwacitsanzo, onani Mateyu 21:5 ndi Zekariya 9:9.