LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 September tsa. 3
  • Pezani Nzelu Zothandiza pa Umoyo pa JW.ORG

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pezani Nzelu Zothandiza pa Umoyo pa JW.ORG
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Thandizo Ilipo
    Galamuka!—2020
  • Mfundo Yothandiza Yokhudza Webusaiti Yathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Colinga ca Webu Saiti Yathu Ndi Kuthandiza Ife ndi Anthu Ena
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2012
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 September tsa. 3

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pezani Nzelu Zothandiza pa Umoyo pa JW.ORG

Mawu a Mulungu amatikonzekeletsa mokwanila kupilila mavuto amene timakumana nawo masiku ano otsiliza. (2 Tim. 3:1, 16, 17) Ngakhale n’conco, nthawi zina timafunika thandizo kuti tipeze mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize pa mbali inayake. Mwacitsanzo, kodi ndinu kholo ndipo mufuna malangizo amene angakuthandizeni kulela bwino ana? Kodi ndinu wacinyamata amene mukukumana na mavuto oyesa cikhulupililo canu? Kapena kodi mukuvutika na cisoni cifukwa munatayikilidwa mwamuna kapena mkazi wanu? Mungapeze nkhani pa jw.org zimene zingakuunikileni mfundo za m’Baibo zothandiza pa mavuto amenewa na ena ambili.—Miy. 2:3-6.

Webusaiti ya jw.org pa tabuleti. Pali kacithunzi koonetsa mbali yakuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA.

Patsamba loyambila la jw.org ku Chichewa, pitani pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA. (Onani cithunzi 1.) Pa mndandanda umene uli pamenepo, sankhani zimene mufuna. Kapena pitani pa LAIBULALE, kenako pa NKHANI ZOSIYANASIYANA, na kusankha zimene mufuna. (Onani cithunzi 2.) Nkhanizi zimapezekanso pa JW Laibulale®.a Mungafufuze zimene mufuna pa malo amene tachulawa. Komanso ngati mungafune, mungafufuze mwacindunji nkhani imene mufuna pogwilitsa nchito danga lofufuzila pa jw.org.

Webusaiti ya jw.org pa tabuleti. Pali zithunzi zoonetsa mbali yakuti LAIBULALE komanso yakuti NKHANI ZOSIYANASIYANA.

Fufuzani mfundo zili m’munsimu pa jw.org poseŵenzetsa danga lofufuzila. Ndiyeno lembani nkhani zimene mwapeza, zimene mufuna kukaŵelenga.

  • Kulela ana

  • Kupsinjika maganizo kwa acinyamata

  • Imfa ya mnzanu wa mu ukwati

a Dziŵani kuti nkhani zina palipano zimapezeka cabe pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani