NKHANI YOPHUNZIRA 37
NYIMBO 114 “Khalani Oleza Mtima”
Kulimbana ndi Zopanda Cilungamo m’Njira Yabwino Koposa
“Iye ankayembekezera cilungamo, koma pankacitika zinthu zopanda cilungamo.”—YES. 5:7.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene citsanzo ca Yesu cingatithandizire kulimbana ndi zopanda cilungamo m’njira yokondweretsa Mulungu.
1-2. Kodi anthu ambiri amatani pakacita zopanda cilungamo? Nanga tingadzifunse mafunso ati?
TIKUKHALA m’dziko lopanda cilungamo. Anthu amacitidwa zopanda cilungamo cifukwa cakuti ndi osauka, cifukwa ca mtundu wao, mmene aonekera, kapena pa zifukwa zina. Ambiri amakumana ndi mabvuto cifukwa ca zocita za amalonda olemera, kapena akulu-akulu a boma omwe amangoganizira zofuna zao. Zopanda cilungamo zimenezi zingacitikire ife kapena munthu amene timadziwa.
2 N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amakwiya akaona kupanda cilungamo komwe kuliko masiku ano. Tonsefe timafuna kukhala m’dziko la mtendere komanso la cilungamo. Ena amayesa kusintha zinthu. Amatero mwa kucita zionetsero zosonyeza kusakondwa ndi boma kapena malamulo omwe alipo, ndi kucirikiza atsogoleri andale omwe amalonjeza kuti adzathetsa kupanda cilungamo. Koma ife monga Akhristu timaphunzitsidwa kuti tisakhale “a dziko.” M’malomwake, timayembekezera Ufumu wa Mulungu umene udzathetsa kupanda cilungamo konse. (Yoh. 17:16) Ngakhale n’tero, timakhumudwa, ngakhale kukwiya kumene nthawi zina, tikaona anthu ena akucitidwa zopanda cilungamo. Tingadzifunse kuti: ‘Ndingacite ciani za conco zikacitika? Kodi pali zimene ndingacitepo palipano polimbana ndi zopanda cilungamo?’ Tisanayankhe mafunsowa, coyamba tikambirane mmene Yehova ndi Yesu amamvera akamaona zopanda cilungamo.
YEHOVA NDI YESU AMADANA NDI ZOPANDA CILUNGAMO
3. N’cifukwa ciani timamva kuipa tikacitidwa zopanda cilungamo? (Yesaya 5:7)
3 Baibo imafotokoza cifukwa cake timamva kuipa tikacitidwa zopanda cilungamo. Imafotokoza kuti Yehova anatilenga m’cifaniziro cake ndi kuti iye “amakonda cilungamo ndipo amaweruza mosakondera.” (Sal. 33:5; Gen. 1:26) Iye sacita zopanda cilungamo, ndipo safuna kuti wina aliyense azicita ena zopanda cilungamo. (Deut. 32:3, 4; Mika 6:8; Zek. 7:9) Mwacitsanzo, m’nthawi ya mneneri Yesaya, Yehova “ankangomva anthu akulira cifukwa cozunzidwa” ndi Aisiraeli anzao. (Werengani Yesaya 5:7.) Yehova anacitapo kanthu mwa kulanga ao amene anali kunyalanyaza Cilamulo cake ndi kucitira ena mopanda cilungamo.—Yes. 5:5, 13.
4. Kodi nkhani ya pa Maliko 3:1-6 ionetsa motani mmene Yesu anali kuonera kupanda cilungamo? (Onaninso cithunzi.)
4 Monga zilili ndi Yehova, nayenso Yesu amakonda cilungamo, ndipo amadana ndi zopanda cilungamo. Tsiku lina Yesu akucita utumiki wake pa dziko lapansi, anaona munthu wolemala dzanja. Yesu anamumvera cifundo munthuyo ndipo anamuciritsa, koma atsogoleri a cipembedzo amene anali ouma mtima anakwiya kwambiri. Iwo anali kulimbikira zokakamiza anthu kuti azitsatira malamulo ena amene iwo anaonjezera okhudza Sabata, m’malo mofuna kuthandiza munthu wobvutikayo. Kodi Yesu anamva bwanji ndi zimenezi? Iye “anamva cisoni kwambiri cifukwa ca kuuma mtima kwao.”—Maliko 3:1-6.
Mosiyana ndi Yesu, atsogoleri a cipembedzo Aciyuda sanali kucitira cifundo anthu obvutika (Onani ndime 4)
5. Kodi tizikumbukira ciani tikaona zopanda cilungamo?
5 Popeza kuti Yehova ndi Yesu amakwiya akaona zopanda cilungamo, ndiye kuti sikulakwa nafenso kukwiya tikaona zinthu za conco. (Aef. 4:26) Komabe, tizikumbukira kuti mkwiyo ulionse umene tingakhale nao cifukwa ca zinthu zopanda cilungamo, sungathetse zopanda cilungamozo. Ndi iko komwe, kukhala okwiya kwa nthawi yaitali kapena kulephera kulamulira mkwiyo wathu kungaononge thanzi lathu ndiponso kungacititse kuti tibvutike maganizo. (Sal. 37:1, 8; Yak. 1:20) Conco tiyenera kucita ciani ndi zopanda cilungamo? Tipeza yankho poona citsanzo ca Yesu.
MMENE YESU ANACITIRA NDI ZOPANDA CILUNGAMO
6. Ndi zopanda cilungamo ziti zimene zinali kucitika pamene Yesu anali pa dziko lapansi? (Onaninso cithunzi.)
6 Yesu ali pa dziko lapansi anaona anthu ambiri akucitidwa zopanda cilungamo. Iye anaona mmene atsogoleri a cipembedzo anali kuponderezera anthu wamba. (Mat. 23:2-4) Analinso kudziwa mmene Aroma anali kuponderezera anthu. Ndipo Ayuda ambiri anali kulakalaka kuti amasuke ku ulamuliro wa Aroma. Ena monga Azeloti, anafika ngakhale pomenyana ndi Aroma kuti amasuke ku ulamuliro wao. Komabe Yesu sanayambitsepo gulu lililonse lofuna kusintha ulamuliro, kapena kulowa magulu otero omwe analipo akale. Ndipo iye atadziwa kuti anthu akufuna kumulonga ufumu, iye anacoka n’kupita kwa yekha.—Yoh. 6:15.
Yesu anathawa anthu amene anali kufuna kumulowetsa m’nkhani za ndale (Onani ndime 6)
7-8. N’cifukwa ciani Yesu sanayambitsepo gulu lililonse lofuna kuthetsa zopanda cilungamo, kapena kulowa magulu otero omwe analipo kale? (Yohane 18:36)
7 Yesu ali pa dziko lapansi sanalowe m’ndale kuti athetse zopanda cilungamo zimene zinali kucitika pa nthawiyo. N’cifukwa ciani sanatero? Iye anadziwa kuti anthu sanalengedwe kuti azidzilamulira okha komanso kuti alibe mphamvu zocitira zimenezo. (Sal. 146:3; Yer. 10:23) Ndiponso anthu sangakwanitse kuthetsa zimene zimacititsa kuti pazicitika zopanda cilungamo. Dzikoli likulamulidwa ndi Satana Mdyerekezi yemwe ndi colengedwa cauzimu comwe cimagwiritsa nchito mphamvu zake kusonkhezera anthu kuti azicita zinthu zopanda cilungamo. (Yoh. 8:44; Aef. 2:2) Kuonjezera apo, ngakhale anthu amakhalidwe abwino sangakwanitse kuthetsa mabvuto a m’dzikoli cifukwa ndi opanda ungwiro ndipo naonso nthawi zina amacita zinthu zopanda cilungamo.—Mlal. 7:20.
8 Yesu anali kudziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokhawo umene ungakwanitse kucotsa zinthu zimene zimacititsa zopanda cilungamo. Ndiye cifukwa cake iye anali “kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” mwakhama. (Luka 8:1) Iye analimbikitsa ‘anthu amene anali kumva njala ndi ludzu la cilungamo’ mwa kuwatsimikizira kuti zacinyengo komanso zopanda cilungamo zidzatha. (Mat. 5:6; Luka 18:7, 8) Boma la kumwamba la Mulungu limene siili “mbali ya dziko lino” ndi limene lidzathetsa mabvuto amenewa, osati maboma a anthu.—Werengani Yohane 18:36.
TENGERANI YESU MUKAONA ZOPANDA CILUNGAMO
9. N’ciani cimakutsimikizirani kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzacotsapo kupanda cilungamo kwa mtundu uliwonse?
9 Tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ Conco zopanda cilungamo zaculuka kwambiri kuposa mmene zinalili m’nthawi ya Yesu. Koma monga zinalili pa nthawiyo, amene amacititsa zopanda cilungamo ndi Satana komanso anthu oipa. (2 Tim. 3:1-5, 13; Chiv. 12:12) Mofanana ndi Yesu, nafenso timadziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzacotsepo Satana ndi kuthetsa zoipa zonse. Cifukwa cakuti timacirikiza Ufumuwo ndi mtima wonse, timakana kutengamo mbali m’zionetsero za kusakondwa komanso zoyesa-yesa za anthu pofuna kuthetsa zopanda cilungamo. Ganizirani za mlongo wina dzina lake Stacy.a Asanaphunzire coonadi, iye anali kucita nao zionetsero za kusakondwa ndi zopanda cilungamo. Koma anayamba kukaikira ngati zimene anali kucita zinali zoyenera. Iye anati: “Pamene tinali kucita zionetserozo, ndinali kudzifunsa ngati zimene tinali kucitazo zinali zothandiza. Koma tsopano ndimacirikiza Ufumu wa Mulungu, ndipo sindikaikira kuti udzathetsa mabvuto onse. Ndidziwa kuti Yehova adzathandiza munthu wina aliyense amene amaponderezedwa kuposa mmene ine ndingacitire.”—Sal. 72:1, 4.
10. Kodi zimene anthu amacita pofuna kusintha zinthu zisemphana motani ndi malangizo a Yesu a pa Mateyu 5:43-48? (Onaninso zithunzi.)
10 Anthu ambiri amene amalowa m’magulu ofuna kusintha zinthu amakhala aukali, osamvera malamulo, komanso ofuna kubvulaza ena. Koma izi n’zosiyana ndi zimene Yesu anaphunzitsa. (Aef. 4:31) M’bale wina dzina lake Jeffrey anati: “Anthu amene akucita zionetsero zooneka ngati zamtendere, angasinthe m’kanthawi kocepa n’kuyamba kucita zaciwawa, kuyamba kuba zinthu, komanso kubvulaza ena.” Komabe, Yesu anaphunzitsa kuti tizicita zinthu mwacikondi ndi anthu onse, ngakhale amene amatitsutsa kapena kutizunza. (Werengani Mateyu 5:43-48.) Pokhala Akhristu, timayesetsa kupewa kucita ciliconse cosemphana ndi zimene Yesu anaphunzitsa kapena citsanzo cake.
Timafunika kulimba mtima kuti tisatengemo mbali m’zocitika za m’dzikoli (Onani ndime 10)
11. N’cifukwa ciani zingakhale zobvuta nthawi zina kutengera citsanzo ca Yesu?
11 Ngakhale kuti tidziwa kuti Ufumu wa Mulungu udzacotseratu kupanda cilungamo, nthawi zina zingatibvute kutengera citsanzo ca Yesu tikacitidwa zopanda cilungamo. Ganizirani zimene zinacitikira mlongo wina dzina lake Janiya amene anthu anali kumusala cifukwa ca khungu lake. Iye ananena kuti: “Zimenezi zinali kundikhumudwitsa kwambiri. Ndinali kukhala wokwiya moti ndinali kufunitsitsa kuti anthuwo alandire cilango. Kenako ndinaganiza zoyamba kucirikiza gulu linalake limene silinali kugwirizana ndi mcitidwe wa tsankho komanso kusalana mitundu. Ndinali kuganiza kuti imeneyo inali njira yabwino yothetsera mkwiyo wanga. Ndipo ikanakonzako zinthu.” M’kupita kwa nthawi, Janiya anazindikira kuti anafunika kusintha kaganizidwe kake. Iye anati: “N’nazindikira kuti m’malo modalira Yehova, ndinayamba kukhulupirira anthu ndi kuwadalira kwambiri kuti angasinthe zinthu. Conco ndinaleka kugwirizana ndi gulu limenelo.” N’zoona kuti timakwiya tikacitidwa zopanda cilungamo kapena tikaona ena akucitidwa zopanda cilungamo. Komabe tiyenera kusamala kuti mkwiyowo usaticititse kutengamo mbali m’zandale.—Yoh. 15:19.
12. N’cifukwa ciani n’canzeru kusankha zimene timaonerera, kuwerenga kapena kumvetsera?
12 N’ciani cingatithandize kukhalabe odekha tikacitidwa zopanda cilungamo kapena zikacitikira anthu ena? Cimodzi cimene cingatithandize ndico kusamala ndi zimene timawerenga, kuonerera, kapenanso kumvetsera. Nkhani zina za pa intaneti komanso za pa masoshomidiya zimalembedwa mokokomeza pofuna kukopa cidwi ca anthu kuti aone zopanda cilungamo zimene zikucitika komanso pofuna kulimbikitsa anthu kuti azicirikiza magulu ofuna kusintha zinthu. Nthawi zambiri, oulutsa nkhani amaikapo maganizo ao-ao pofotokoza zimene zacitika m’malo mofotokoza zenizeni. Ngakhale kuti nkhani yafotokozedwa molondola, kodi kungokhalira kumaiganizira nkhaniyo kungatipindulire mwa njira ina iliyonse? Ngati timathera nthawi yathu yoculuka kuonerera kapena kumvetsera nkhani za conco, zingacititse kuti tikhale ankhawa kwambiri, okhumudwa, komanso okwiya. (Miy. 24:10) Ndipo coipa kwambiri kuposa pamenepa n’cakuti tingasiye kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wathu n’kuiwala kuti Ufumuwo ndiwo wokha umene udzacotsepo mabvuto onse.
13. Kodi kuwerenga Baibo tsiku lililonse kungatithandize motani kuti tiziziona moyenera zopanda cilungamo?
13 Kuwerenga Baibo tsiku lililonse komanso kusinkhasinkha kungatithandize kudziwa mmene tingacitire nazo zopanda cilungamo. Mlongo wina dzina lake Alia anakhumudwa kwambiri poona zopanda cilungamo zimene zinali kucitikira anthu a m’dera lake. Iye anali wokhumudwa cifukwa anthu amene anali kucita zopanda cilungamozo sanali kupatsidwa cilango. Iye anati: “Ndinaiganizira mofatsa nkhaniyi ndipo ndinafika pa mfundo yakuti, ‘Ngati ndimakhulupiriradi kuti Yehova adzathetsa mabvuto onsewa, ndiye kuti ndiyenera kusintha kaganizidwe kanga.’ Panthawiyo ndinawerenga lemba la Yobu 34:22-29. Mavesi amenewa anandikumbutsa kuti Yehova amaona zonse zimene zimacitika. Ndiye yekha amene adziwa mmene cilungamo ceniceni ciyenera kukhalira. Ndiponso ndiye yekha amene adzathetsa mabvuto onse mofikapo.” Koma pamene tikuyembekezera Ufumu wa Mulungu kuti ubweretse cilungamo ceniceni, kodi tiyenera kucita nazo motani zopanda cilungamo?
ZIMENE TINGACITE TIKAONA ZOPANDA CILUNGAMO
14. Kodi tingatani kuti tipewe kuonjezera zopanda cilungamo zimene zikucitika m’dzikoli? (Akolose 3:10, 11)
14 Tilibe mphamvu zoletsa anthu ena kucita zinthu zopanda cilungamo, koma tili nazo mphamvu zolamulira zocita zathu. Monga taonera kale, tingathe kuonetsa ena cikondi potengera Yesu. Cikondi coteroco cimatisonkhezera kucitira ena ulemu, ngakhale aja amene amacita zopanda cilungamo. (Mat. 7:12; Aroma 12:17) Yehova amakondwera tikamacita ndi ena mokoma mtima komanso mwacilungamo.—Werengani Akolose 3:10, 11.
15. Cimacitika n’ciani tikamagawirako ena coonadi ca m’Baibo?
15 Njira yabwino koposa imene tingathandizire anthu ndi kuwaphunzitsa coonadi ca m’Baibo. Tikunena zimenezi cifukwa cakuti munthu wankhanza komanso waciwawa akaphunzira za Yehova, amasintha n’kukhala munthu wokoma mtima komanso wokonda mtendere. (Yes. 11:6, 7, 9) Jemal asanaphunzire coonadi, anali kuona kuti boma limene linali kuwalamulira linali kupondereza anthu. Conco analowa gulu la zigawenga limene linali kulimbana ndi bomalo. Ataphunzira coonadi iye anati: “Sungakakamize anthu kusintha. Palibe munthu anandikakamiza kusintha. Koma coonadi cimene ndinali kuphunzira m’Baibo n’cimene cinandisintha.” Zimene Jemal anaphunzira zinamulimbikitsa kuti asiye kugwirizana ndi gulu la zigawenga. Tikathandiza anthu kusintha makhalidwe ao mwa kuphunzira nao Baibo, ciwerengero ca anthu amene amacita zopanda cilungamo cimacepa.
16. N’ciani cimakulimbikitsani kugawirako ena uthenga wa Ufumu?
16 Mofanana ndi Yesu, nafenso mofunitsitsa timauzako anthu ena kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo mankhwala okhawo othetsera zinthu zopanda cilungamo. Uthenga umenewu umapatsa ciyembekezo anthu amene anacitidwa zopanda cilungamo. (Yer. 29:11) Stacy, amene tam’chula m’ndime 9 anakamba kuti: “Coonadi cimene ndaphunzira cimandithandiza kupirira zopanda cilungamo zimene zandicitikira komanso zimene ndimaona. Yehova amapereka citonthozo pogwiritsa nchito mfundo za m’Baibo.” Muyenera kukhala okonzeka kuti muthe kutonthoza ena ndi malonjezo a m’Baibo. Mukakhala otsimikiza kuti mfundo za m’Malemba zimene takambirana m’nkhani ino n’zoona, cidzakhala cosabvuta kukambirana ndi ena nkhaniyi mosamala kusukulu kapena kunchito.b
17. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kupirira zopanda cilungamo?
17 Malinga ngati Satana ndiye “wolamulira wa dzikoli” tidzapitirizabe kuona zopanda cilungamo. Koma pamene tikuyembekezera kuti Satana ‘aponyedwe kunja,’ tizikumbukira kuti Yehova analonjeza kuti adzatithandiza. (Yoh. 12:31) Kudzera m’Malemba, Yehova samangotiuza cifukwa cake pali zopanda cilungamo zoculuka conci padzikoli. Koma amatiuzanso mmene amamvera akaona kusautsika kwathu. (Sal. 34:17-19) Kudzera mwa Mwana wake, Yehova amatiphunzitsa mmene tiyenera kucitira ndi zopanda cilungamo palipano, komanso kuti posacedwa Ufumu wake udzacotsapo zopanda cilungamo zonse. (2 Pet. 3:13) Tiyeni tipitirize kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mokangalika pamene tikuyembekezera mwacidwi nthawi pomwe dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu acilungamo komanso owongoka mtima.—Yes. 9:7.
NYIMBO 158 “Silidzacedwa!”
a Maina ena asinthidwa.
b Onani zakumapeto A mfundo 24-27 m’bulosha yakuti Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila.