LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 September masa. 26-30
  • Yehova Anatithandiza Kuphuka Kulikonse Komwe Tinabzalidwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Anatithandiza Kuphuka Kulikonse Komwe Tinabzalidwa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Wanidalitsa Kwambili Kuposa Mmene N’nali Kuyembekezela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Yehova ‘Wawongola Njila Zanga’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Zimene Zingakuthandizeni Ngati Utumiki Wanu Watha
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Mlangizi Wathu Wamkulu Watiphunzitsa kwa Moyo Wathu Wonse
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 September masa. 26-30
Mats ndi Ann-Catrin ali kumudzi ndipo aimirira pafupi ndi galimoto yao yochedwa SUV.

MBIRI YANGA

Yehova Anatithandiza Kuphuka Kulikonse Komwe Tinabzalidwa

YOSIMBIDWA NDI MATS NDI ANN-CATRIN KASSHOLM

“PHUKA kumene wabzalidwa.” Ulangiziwu ungamveke wacilendo. Koma Mats ndi mkazi wake Ann-Catrin, a ku Sweden, “anabzalidwa” mobwereza-bwereza. Kodi zinacitika motani, ndipo kodi ulangizi umenewo unawapindulira bwanji?

Awiriwa analowa Sukulu ya Giliyadi mu 1979 ndipo pa zaka zonsezi akhala “akubzalidwa-bzalidwa,” kapena kuti kutumizidwa kukatumikira ku Iran, Mauritius, Myanmar, Tanzania, Uganda, ndi ku Zaire. Ku Giliyadi n’komwe mlangizi wa sukuluyo, Jack Redford, anawapatsa malangizo omwe anawathandiza pamene anali “kubzalidwa,” “kuzulidwa,” ndi “kubzalidwanso” mobwereza-bwereza. Tiyeni tiwalole afotokoze okha.

M’bale Mats, tiuzen’koni mmene munapezera coonadi.

Mats: Nkhondo yaciwiri yapadziko lonse ili mkati, atate anali kukhala ku Poland. Pa nthawiyo anaona zacinyengo zambiri zikucitika m’chalichi ca Katolika. Komabe, kambiri anali kukonda kukamba kuti, “Coonadi ciyenera kukhalapo ndithu kwinakwake.” M’kupita kwa nthawi, n’natsimikiza kuti zimene anali kukambazo zinali zoona. N’nagula mabuku akale ambiri. Limodzi linali la cikuto cabuluu lochedwa Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Mutu wake unandikopa cidwi kwambiri moti ndinaliwerenga lonse usiku womwewo. Podzafika m’mawa, n’nali n’tazindikira kuti ndapeza coonadi!

Kucokera mu April 1972, ndinawerenganso mabuku ena ambiri a Mboni za Yehova ndipo n’napeza mayankho pa mafunso anga okhudza Baibo. Ndinamva ngati wamalonda wa m’fanizo la Yesu amene, atapeza ngale yamtengo wapatali, anagulitsa zonse zimene anali nazo kuti akagule ngaleyo. Mofananamo, “ndinagulitsa” colinga canga cokacita maphunziro a ku yunivesite kuti ndikhale dokotala, nditero kunena kwake, conseco kuti ndigule “ngale” ya coonadi imene ndinapeza. (Mat. 13:​45, 46) N’nabatizika pa December 10, 1972.

M’caka cimodzi cabe, makolo anga komanso mng’ono wanga analandira coonadi n’kubatizika. Mu July 1973, n’nayamba utumiki wa nthawi zonse. Mumpingo mwathu munali apainiya okangalika. Mmodzi wa iwo anali mlongo wokongola komanso wokonda zinthu zauzimu, Ann-Catrin, amene ananditenga mtima. Tinagwa m’cikondi ndipo tinakwatirana mu 1975. Kwa zaka zinai, tinali kukhala m’tauni ya Strömsund, ku Sweden. Tauniyi inali yokongola komanso inali gawo la conde.

Ann-Catrin: Atate anaphunzira coonadi atatsala pang’ono kumaliza maphunziro a ku yunivesite mumzinda wa Stockholm. Pa nthawiyo n’nali khanda la miyezi itatu yokha koma anali kundinyamula kuti ndipite nao kumisonkhano ndi muutumiki. Amai sanazikonde zimenezi ndipo anayesetsa kuonetsa kuti Mboni za Yehova n’zabodza. Koma zoyesa-yesa zao zinalephera moti m’kupita kwa nthawi iwonso anabatizika. N’nabatizika ndili ndi zaka 13, ndipo n’tafika zaka 16 n’nayamba upainiya. N’tatumikira ku Umeå, ku malo osowa, n’naikidwa kukhala mpainiya wapadera.

Ine ndi Mats titakwatirana, tinali osangalala kuthandiza anthu ambiri kuphunzira coonadi. Izi zinatibweretsera cimwemwe cacikulu. Mmodzi wa iwo anali Maivor, mtsikana amene anasiya nchito yake monga katswiri wa zamasewera ndipo anayamba kucitira limodzi upainiya ndi mng’ono wanga. Awiriwa analowa Sukulu ya Giliyadi mu 1984 ndipo akutumikira monga amishonale ku Ecuador.

Kodi ulangizi wakuti “phuka kumene wabzalidwa” munautsatira bwanji m’nchito zanu zambiri zaumishonale?

Mats: Mobwereza-bwereza tinali “kubzalidwa,” kapena kuti kusinthidwa mautumiki athu. Ngakhale n’tero, tinayesetsa kukhalabe “ozika mizu” mwa Yesu pocita zonse zimene tikanatha kuti titengere makhalidwe ake, maka-maka kudzicepetsa kwake. (Akol. 2:​6, 7, BL) Mwacitsanzo, m’malo moyembekezera kuti abale ndi alongo a ku malo kumene tatumizidwa azicita zinthu mmene tifunira, tinayesetsa kuphunzira cifukwa cake anali kucita zinthu m’njira inayake. Tinali kufuna kumvetsa cikhalidwe cao ndi mmene amaganizira. Kutengera citsanzo ca Yesu kunali kutipangitsa kumva ngati tabzalidwa “m’mphepete mwa mitsinje ya madzi.” Zikatero, tinali kuphuka muutumiki ulionse umene tapatsidwa.​—Sal. 1:​2, 3.

Mats ndi Ann-Catrin anyamula katundu ndi zakudya.

Tili ku Zaire, tinali kukhala umoyo wosamuka-samuka

Ann-Catrin: Mtengo ukabzalidwanso, umafuna kuwala kwa dzuwa kuti upitirize kukula. Kwa ife, Yehova nthawi zonse wakhala “dzuwa.” (Sal. 84:11) Iye watipatsa abale ndi alongo amene amatikonda. Mwacitsanzo, tili ku Tehran, m’dziko la Iran, abale ndi alongo athu mumpingo wathu waung’ono anationetsa mzimu wocereza. Izi zinatikumbutsa mzimu wocereza wa anthu ochulidwa m’Baibo. Tikanakonda kukhalabe m’dzikoli. Koma mu July 1980, boma linatseka nchito ya Mboni za Yehova. Anatiuza kuti ticoke m’dzikolo pasanathe masiku awiri. Tinatumizidwa ku Africa, m’dziko la Zaire, limene masiku ano limachedwa Congo.

Nyumba yamalata m’dera la ku midzi ku Zaire.

Nthawi yosangalatsa pa utumiki wathu ku Zaire, mu 1982

N’tadziwa kuti atitumiza ku Africa, n’nagwetsa misozi. Zimene n’namva zokhudza njoka ndi matenda a ku Africa zinandipatsa mantha. Koma anzathu awiri amene anali atatumikira ku Africa kwa nthawi yaitali anatiuza kuti: “Musacite mantha. Simunapiteko ku Africa. Koma tikudziwa kuti mukapitako, mudzakondako.” Ndipo tinakondakodi! Abale ndi alongo kumeneko ndi acikondi komanso olimbikitsa. Titatumikira ku Zaire kwa zaka 6, tinafunikira kucoka cifukwa ca ciletso. N’namwetulira poona kuti n’nasinthiratu mmene n’nali kuonera Africa. Moti n’nali kupemphera kwa Yehova kuti, “Conde, lolani kuti tikhalebe mu Africa.”

Kodi ndi madalitso otani omwe mwapeza pa zaka zonsezi?

Ann-Catrin wakhala pa mpando wa ndatopa pa bwalo pa galimoto yao yochedwa Volkswagen Kombi.

Galimoto imenenso tinali kugonamo ku Tanzania, mu 1988

Mats: Utumikiwu watithandiza kukhala pa ubwenzi ndi amishonale ocokera ku maiko osiyana-siyana ndi zikhalidwe zosiyana-siyana. Cina, pocita mautumiki ena, aliyense wa ife anali kutsogoza maphunziro oculuka ngati 20! Ndipo izi zinali kutipangitsa kukhala acimwemwe kwambiri. Kuonjezera apo, sindidzaiwala cikondi ndi kucereza kwa abale ndi alongo a mu Africa. Poyendera mipingo ya ku Tanzania, tinali kugona m’galimoto. Ndipo abale a kumeneko anali kucita zilizonse “zimene akanatha” kuti aticereze ngakhale kuti anali osauka kwambiri. (2 Akor. 8:3) Cina cimene cinali kutisangalatsa kwambiri ndi ici: Pamapeto pa tsiku lililonse, ine ndi Ann-Catrin tinali kukhala phee! n’kumasimbirana zimene zacitika pa tsikulo, ndi kuyamika Yehova pokhala nafe.

Ann-Catrin: Kwa ine, cimene candisangalatsa ndi kudziwana ndi abale ndi alongo a m’maiko osiyana-siyana. Tinaphunzira zilankhulo zosiyana-siyana monga ci Farsi, Cifulenci, ci Luganda, ndi ci Swahili kwinaku tikuphunziranso zikhalidwe zosiyana-siyana zocititsa cidwi. Tinathandiza abale ndi alongo acatsopano kupita patsogolo, tinapanga mabwenzi abwino, ndipo tinali kusangalala kutumikira Yehova “mogwirizana.”​—Zef. 3:9.

Tinaonanso zinthu zosiyana-siyana zokongola zacilengedwe. Nthawi iliyonse tikalandira utumiki watsopano, zinali ngati tili pa ulendo wokaona malo ndipo Yehova ndiye anali wotionetsa malowo. Yehova watiphunzitsa zinthu zimene patokha sitikanaziphunzira.

Zithunzi: 1. Mats ndi Ann-Catrin akulalikira mai yemwe ali ndi ana. 2. Ann-Catrin akulalikira mnyamata wa ci Maasa.

Tikulalikira m’magao osiyana-siyana a ku Tanzania

Kodi mwakumanapo ndi mabvuto otani? Nanga munathana nao bwanji?

Mats: Tinadwalapo matenda osiyana-siyana, kuphatikizapo malungo. Ndipo Ann-Catrin anacitidwapo maopaleshoni osayembekezereka. Tinalinso kudera nkhawa makolo athu okalamba. Tiyamikira acibale athu amene anali kuwasamalira. Anagwira nchitoyo moleza mtima, mwacimwemwe, komanso mwacikondi. (1 Tim. 5:4) Ngakhale kuti tinali kuwatumizira thandizo, nthawi zina tinali kudziimbabe mlandu poganiza kuti zimene tinali kucita sizinali zokwanira.

Ann-Catrin: Mu 1983, apo n’kuti tikutumikira ku Zaire, ndinafooka kwambiri ndi nthenda ya kolera. Dokotala, pofuna kupulumutsa moyo wanga, anauza Mats kuti, “M’tulutse m’dziko lino lero lomwe!” Tsiku lotsatira tinapita ku Sweden pandeke yonyamula katundu. Ndekeyo ndiyo yokha inalipo.

Mats: Tinaganiza kuti uku ndiko kutha kwa utumiki wathu waumishonale. Conco, tinalira kwambiri. Koma mosiyana ndi zimene dokotala ananena kuti Ann-Catrin sadzacira, iye anakhala bwino. Ndipo patapita caka cimodzi, tinabwerera ku Zaire. Koma ulendo uno tinafikira ku Lubumbashi, mumpingo waung’ono wa ci Swahili.

Ann-Catrin: Tili ku Lubumbashi, ndinali ndi pakati koma mwana anapitirira. Ngakhale kuti tinalibe colinga cokhala ndi ana, kutaikiridwa mwana wathu kunandipweteka mosaneneka. Pa nthawi yacisoni imeneyo, Yehova anatipatsa mphatso imene sitinayembekezere. Mphatsoyo inali yakuti tinayambitsa maphunziro a Baibo ambiri kuposa n’kale lonse. Komanso, pasanathe caka cimodzi, ciwerengero ca ofalitsa mumpingo mwathu cinaonjezeka kucoka pa 35 kufika pa 70. Ndipo ciwerengero ca opezeka pamisonkhano cinaonjezeka kucoka pa 40 kufika pa 220. Tinali otanganidwa kwambiri ndi utumiki ndipo madalitso a Yehova ananditonthoza kwabasi. Ngakhale n’tero, kawiri-kawiri timaganizira ndi kukamba za mwana wathu wokondedwa. Ndipo tikuyembekezera mwacidwi nthawi pomwe Yehova adzaciritse mitima yathu kotheratu.

Mats: Pa nthawi ina, Ann-Catrin anayamba kumva kufooka komanso kutopa kotheratu mphamvu. Pa nthawi imodzi-modziyo anandipeza ndi khansa ndipo ndinafunika kucitidwa opaleshoni yaikulu. Koma pano ndili bwino, ndipo Ann-Catrin akucita zonse zimene angathe potumikira Yehova.

Tafika pozindikira kuti sindife tokha amene tikulimbana ndi mabvuto. Nkhondo yapaciweniweni ya ku Rwanda ya mu 1994 itatha, tinapita kukaonana ndi abale ndi alongo ambiri ku misasa ya anthu othawa kwao. Kuona cikhulupiriro cao, kupirira kwao, ndi mzimu wao wocereza kunatiphunzitsa kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kuthandiza anthu ake pabvuto lina lililonse.​—Sal. 55:22.

Ann-Catrin: Tinakumana ndi bvuto pamene tinapezeka pa mwambo wopatulira ofesi ya nthambi ya ku Uganda mu 2007. Pulogalamuyi itatha, tinanyamuka ndi gulu la amishonale ndi atumiki a pa Beteli, onse pamodzi 25. Tinali kupita ku Nairobi, m’dziko la Kenya. Tisanafike paboda ndi dziko la Kenya, galimoto ina imene inali kubwera kutsogolo kwathu mwadzidzidzi inalowa kumbali yathu n’kugundana ndi galimoto yathu. Dalaivala ndi anzathu ena asanu anafera pomwepo. Koma mlongo wina anakafera kucipatala. Tikuyembekezera mwacidwi kudzaonananso ndi mabwenzi athu amenewo.​—Yobu 14:​13-15.

Ine n’navulala pangoziyo. Koma m’kupita kwa nthawi, n’nakhala bwino. Komabe, ine ndi mwamuna wanga Mats komanso ena amene tinali nao pangoziyo, kwa kanthawi ndithu, tinali kubvutika kwambiri maganizo pokumbukira zimene zinacitikazo. Kumbali yanga, nkhawa inali kukula kwambiri usiku moti ndinali kudzidzimuka n’kumva ngati ndadwala matenda a kumtima. Izi zinali kundicititsa mantha kwambiri. Koma cimene cinatithandiza kupirira ndi kupemphera kwa Yehova kucokera pansi pamtima ndi kuwerenga malemba athu apamtima. Tinapitanso kwa madokotala odziwa za matenda a maganizo ndipo anatithandiza kwambiri. Palipano, bvuto lathu linacepako ndipo timapempha Yehova kuti atithandize kutonthoza anthu ena amene akukumana ndi bvuto ngati limeneli.

Pofotokoza zimene zinakuthandizani kuti mupirire mabvuto, munanena kuti Yehova anakunyamulani “ngati mazira osaphika.” Kodi munatanthauza ciani?

Mats: Mauwa acokera ku mwambi wa ci Swahili wakuti “Tumebebwa kama mayai mabichi,” kutanthauza kuti “Tinanyamulidwa ngati mazira osaphika.” Munthu amanyamula mazira osaphika mosamala kwambiri kuti asaphwanyike. N’cimodzi-modzi ndi Yehova. Anatisamalira bwino m’mautumiki athu onse. Sitinasowepo zinthu zofunikira paumoyo, ndipo nthawi zina tinali kukhala ndi zambiri kuposa zimene tinali kufunikira. Njira imodzi imene tinaonera cikondi ca Yehova ndi thandizo lake ndi kudzera m’Bungwe Lolamulira limene linaticitira cifundo.

Ann-Catrin: Lekani n’kufotokozeren’koni citsanzo cimodzi ca mmene Yehova anatithandizira mwacikondi. Ndinalandira foni yondidziwitsa kuti atate ku Sweden akudwala mwakaya-kaya. Apa n’kuti mwamuna wanga Mats wangocira kumene matenda a malungo ndipo tinalibe ndalama zokwanira zogulira matikiti a ndeke kuti tibwerere kwathu. Conco, tinaganiza zogulitsa galimoto yathu. Kenako tinalandira foni kucokera ku banja lina lomwe linamva za bvuto lathu ndipo anatiuza kuti adzatigulira tikiti imodzi. Tinalandiranso foni ina yocokera kwa mlongo wina wacikulire amene anali atasungako ndalama m’bokosi lomwe analembapo kuti “Za ofunikira thandizo.” M’mphindi zocepa cabe, Yehova anatithandiza kuti tipeze matikiti amene tinali kufunikira.​—Aheb. 13:6.

Mukayang’ana kumbuyo pa zaka 50 zimene mwakhala mukucita utumiki wa nthawi zonse, kodi mwaphunzira ciani?

Mats ndi Ann-Catrin aimirira moyandikana ndipo ndi osangalala.

Tili mu utumiki wathu watsopano ku Myanmar

Ann-Catrin: Ndaphunzira kuti ‘timakhala amphamvu tikakhala odekha komanso tikamasonyeza kuti timadalira’ Mulungu. Tikam’khulupirira Yehova, amatimenyera nkhondo. (Yes. 30:15; 2 Mbiri 20:​15, 17) Cifukwa cakuti tacita zonse zotheka pa mautumiki athu onse, talandira madalitso omwe sitikanalandira kwina kulikonse.

Mats: Cacikulu cimene ndaphunzira n’cakuti kaya zinthu zibvute bwanji, ndiyenera kudalira Yehova n’kuyembekezera kuti adzandithandiza. (Sal. 37:5) Iye sanalepherepo ngakhale kamodzi kutithandiza. Ndipo ife timaonabe kuti akutithandiza pa utumiki wathu wa pa Beteli umene tikucita palipano ku Myanmar.

Tikukhulupirira kuti acinyamata amene akufuna kuonjezera utumiki wao, Yehova adzawaonetsa cikondi cake cokhulupirika ngati mmene wacitira kwa ife. Tikukhulupiriradi kuti Yehova adzawaonetsa cikondi cake cokhulupirika ngati angamulole kuwathandiza kuphuka, kulikonse kumene angabzalidwe.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani