LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 September masa. 20-25
  • Anthu a “Maganizo Abwino” Adzalola Kuphunzira Nao

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anthu a “Maganizo Abwino” Adzalola Kuphunzira Nao
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUKAPEZA ANTHU ACIDWI
  • PHUNZIRO LA BAIBO LIKAYAMBIKA
  • ATSOPANO AKABWERA KU MISONKHANO
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Mmene Tingaonjezele Cimwemwe Cathu mu Ulaliki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Kuyandikila Abale ndi Alongo Athu n’Kwabwino Kwa Ife!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 September masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZIRA 39

NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”

Anthu a “Maganizo Abwino” Adzalola Kuphunzira Nao

“Anthu onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira.”​—MAC. 13:48.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Nthawi yoyenerera pomwe tiyenera kupempha munthu kuyamba kuphunzira naye Baibo komanso yomuitanira kumisonkhano.

1. Kodi anthu amasiyana motani mmene amalandilira uthenga wabwino? (Macitidwe 13:​47, 48; 16:​14, 15)

ANTHU ambiri m’zaka za zana loyamba anali kulandira coonadi nthawi yomweyo imene amva uthenga wabwino. (Werengani Macitidwe 13:​47, 48; 16:​14, 15.) Masiku anonso pali anthu ena amene amasangalala nao uthenga wabwino nthawi yoyamba imene aumva. Ngakhale aja amene poyamba sanaonetse cidwi pa uthenga wabwino, m’kupita kwa nthawi angatsegule mtima wao n’kulandira uthengawo. Tiyenera kutani tikapeza anthu a “maganizo abwino” mu ulaliki?

2. Kodi nchito yathu yopanga ophunzira ifanana motani ndi ya wolima dimba?

2 Nchito yathu yopanga ophunzira tingaiyerekezere ndi zimene munthu wolima dimba amacita. Zipatso zina zikayamba kupsya mu mtengo wina, mwini dimbayo amazithyola kwinaku akusamalira komanso kuthirira mitengo ina, ngakhale kubzala mitengo ina m’dimba lakelo. Mofananamo, tikapeza munthu amene afuna kumvetsera uthenga wathu, timafuna kum’thandiza kuti akhale wotsatira wa Khristu mwamsanga. Timacita zimenezi, kwinaku tikuthandiza ena amene akufunikirabe nthawi kuti aone kufunika kodziwa Mulungu komanso kuphunzira Baibo. (Yoh. 4:​35, 36) Kuzindikira kudzatithandiza kusankha njira yabwino koposa imene tingathandizire anthu. Tiyeni tione zimene tingacite pa kukambirana kwathu koyamba ndi anthu acidwi. Tionenso mmene tingawathandizire kuti apite patsogolo.

MUKAPEZA ANTHU ACIDWI

3. Kodi tiyenera kutani tikapeza anthu acidwi muutumiki? (1 Akorinto 9:26)

3 Tikapeza anthu acidwi muutumiki, tiwathandize nthawi yomweyo kuti ayambe kuyenda panjira yopita ku moyo. Zikatero, tisacedwe kuwapempha kuti tiziphunzira nao Baibo komanso kuwaitanira ku misonkhano yathu nthawi yomweyo.​—Werengani 1 Akorinto 9:26.

4. Fotokozani cocitika ca munthu amene anali wokonzeka kuyamba kuphunzira Baibo nthawi yomweyo.

4 Kuyambitsa phunziro. Anthu ena omwe timakamba nao amakhala okonzeka kuyamba kuphunzira Baibo nthawi yomweyo. Mwacitsanzo, tsiku lina pa Cinai, mtsikana wina ku Canada anafika pa kasitandi ka ulaliki wapoyera n’kutengapo bulosha yakuti Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya! Mlongo yemwe anali pakasitandipo anam’fotokozera kuti kabukuka timakagwiritsa nchito kuphunzirira Baibo kwaulere. Mtsikanayo anacita cidwi ndipo anapereka foni namba yake. Pambuyo pake tsiku lomwelo, mtsikanayo analembera mlongoyo meseji yomufunsa tsiku limene angayambe kuphunzira. Mlongoyo anati angabwere kumapeto kwa mlungu. Koma mtsikanayo anati: “Bwanji mawa? Ndine womasuka.” Moti anaphunziradi tsiku lotsatira. Mtsikanayo anapezeka pamsonkhano kumapeto kwa mlungu womwewo, ndipo anapita patsogolo mofulumira kwambiri.

5. Kodi tingaonetse bwanji kuzindikira tikamapempha anthu kuti tiyambe kuphunzira nao Baibo? (Onaninso zithunzi.)

5 Sitiyembekezera kuti anthu onse angakhale ndi cidwi cofanana ndi cimene mtsikana uja anali naco. Ena amafunika kuwalimbikitsa kuti akulitse cidwi cao. Poyamba, tingafunike kukambirana nao nkhani imene angacite nayo cidwi. Ngati tikhalabe ndi maganizo abwino pa anthuwo ndi kuwaonetsa cidwi, m’kanthawi kocepa tingayambe kuphunzira nao Baibo. Kodi tingawapemphe bwanji anthu kuti tiyambe kuphunzira nao? Abale ndi alongo angapo amene ali ndi luso loyambitsa maphunziro a Baibo anafunsidwa funso limeneli.

Zithunzi: 1. Abale awiri akulankhula ndi mwamuna wacikulire yemwe wakhala pa khonde. 2. Alongo awiri agawira bulosha yakuti “Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!” kwa mai pa khomo pake. Maiyo wanyamula mwana wake wamng’ono wamwamuna ndipo mwana wina waimirira pafupi naye.

Kodi tinganene ciani kuti anthu awa akopeke nako kuphunzira Baibo? (Onani ndime 5)a


6. Kodi tingacite ciani kuti tisiye khomo lili citsegukire kwa munthu amene waonetsa cidwi?

6 Ofalitsa ndi apainiya ena omwe anafunsidwa zokhudza kuyambitsa maphunziro ananena kuti m’maiko ena ndi bwino kupewa mau akuti “kuphunzira,” “kosi yophunzitsa Baibo,” kapena “kukuphunzitsani.” Ananena kuti ndi bwino kukamba mau akuti “kuceza,” “kukambirana,” ndi “kuidziwa Baibo.” Kuti musiye khomo la makambirano lili citsegukire, mungauze munthuyo kuti, “Ndikhulupirira mungakonde kudziwa kuti Baibo imayankha mafunso ofunika kwambiri paumoyo” kapena “Baibo si buku la cipembedzo cabe ayi, imaperekanso malangizo otithandiza paumoyo.” Mungaonjezerenso kuti: “Sizitenga nthawi yaitali. M’mphindi 10 kapena 15 mungaphunzire mfundo yothandiza kwambiri.” Tizipewa kukamba mau monga akuti, “tipangane” kapena “mlungu ndi mlungu.” Mau ngati amenewa angapangitse munthu kumva ngati tamuika mu pulogilamu inayake.

7. Kodi ndi liti pomwe ena amazindikira kuti apeza coonadi ca m’Baibo? (1 Akorinto 14:​23-25)

7 Aitanireni kumisonkhano. Zikuoneka kuti m’nthawi ya mtumwi Paulo ena anazindikira kuti apeza coonadi ca m’Baibo atapezeka pa msonkhano wacikhristu. (Werengani 1 Akorinto 14:​23-25.) Nthawi zambiri izi ndi zimene zimacitikanso masiku ano. Acatsopano ambiri, amapita patsogolo mwamsanga akayamba kupezeka pamisonkhano yathu. Kodi ndi liti pomwe muyenera kuwaitanira? M’mutu 10, m’buku la Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya! muli mbali yopempha munthu kuti akapezeke pa misonkhano. Koma musayembekezere mpaka mutafika pa mbali imeneyo. Pa makambirano anu oyamba omwewo, muitanireni ku msonkhano wa kumapeto kwa mlungu. Pomuitanira, mungam’chulireko mutu wa nkhani ya onse, kapena mfundo imene mudzaphunzira mu Nsanja ya Mlonda mlunguwo.

8. Kodi munthu amene tikumuitanira kumisonkhano tingam’fotokozere zotani? (Yesaya 54:13)

8 Poitanira munthu, mufotokozereni kusiyana komwe kulipo pakati pa misonkhano yathu ndi ya zipembedzo zina. Wophunzira Baibo wina atapezekapo koyamba pa phunziro la Nsanja ya Mlonda, anafunsa mphunzitsi wake kuti: “Kodi wotsogoza amadziwa dzina la aliyense?” Mphunzitsiyo anafotokoza kuti tonsefe timayesetsa kudziwa dzina la aliyense mumpingo monga mmene timadziwira maina a anthu am’banja mwathu. Wophunzirayu anati izi n’zosiyana kwambiri ndi kuchalichi kwao. Tingam’fotokozerenso colinga ca misonkhano yathu. (Werengani Yesaya 54:13.) Timasonkhana kuti tilambire Yehova, tiphunzire za iye, ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake. (Aheb. 2:12; 10:​24, 25) Zotsatira zake n’zakuti misonkhano yathu imakhala ya dongosolo komanso yophunzitsadi kanthu. Sipakhala miyambo. (1 Akor. 14:40) Nyumba zathu za Ufumu zinakonzedwa m’njira yakuti cizikhala cosabvuta kuphunziriramo. Sitikambirana nkhani za ndale cifukwa sitilowerera m’ndale. Timapewanso kukangana pa nkhani za munthu mwini kapena nkhani zina. Zimakhala zothandiza kuonetsa wophunzira wathu pasadakhale vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? Kutero kudzam’thandiza kudziwiratu zimene adzapeza.

9-10. Tikaitanira munthu kumisonkhano, kodi tingatani pofuna kum’tsimikizira kuti sitidzam’kakamiza kukhala wa Mboni kapena kutengako mbali? (Onaninso cithunzi.)

9 Ena amazengereza kupezeka pamisonkhano cifukwa amaopa kuti adzapemphedwa kukhala a Mboni. Mutsimikizireni munthu amene mwaitanira kuti timamva bwino kukhala ndi alendo. Muuzeninso kuti sitimakakamiza alendo kukhala a Mboni kapena kutengapo mbali pa misonkhano. Mabanja onse ndi olandiridwa, kuphatikizapo aja omwe ali ndi ana aang’ono. Pamisonkhano yathu, ana sitiwaphunzitsira paokha. M’malomwake, tonse timaphunzirira limodzi. Izi zimathandiza makolo kudziwa kuti ana ao ali ndi ndani komanso kuti akuphunzitsidwa ciyani. (Deut. 31:12) Muuzeninso kuti sitisonkhetsa ndalama kapena kupititsa mbale ya copereka. M’malomwake, timatsatira lamulo la Yesu lakuti: “Munalandira kwaulere, muzipereka kwaulere.” (Mat. 10:8) Mufotokozereninso kuti sayenera kucita kubvala zobvala zodula kuti apezekepo. Mulungu amayang’ana mumtima osati pa maonekedwe akunja.​—1 Sam. 16:7.

10 Munthu akapezeka pamisonkhano, m’pangitseni kumva kuti ndi wolandiridwa. Mudziwikitseni kwa akulu ndi kwa ofalitsa ena. Akamva kuti ndi wolandiridwa, mwacionekere adzafuna kudzabweranso. Misonkhano ili mkati, muzionera limodzi malemba m’Baibo yanu ngati iye alibe. M’thandizeni kutsatira mkambi ndi kuona mmene timaphunzirira.

Mai wa pa cithunzi capita ndi wosangalala cifukwa ca mmene abale ndi alongo amulandirira ku Nyumba ya Ufumu. Wanyamula mwana wake wamng’ono pomwe mwana wake wina akukambirana ndi wacicepere.

Munthu akayamba mwamsanga kupezeka pamisonkhano, amayambanso kupindula mwamsanga (Onani ndime 9-10)


PHUNZIRO LA BAIBO LIKAYAMBIKA

11. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumalemekeza nthawi ya wophunzira wanu?

11 Kodi tiyenera kukumbukira mfundo ziti tikayamba kuphunzira Baibo ndi munthu? Muzilemekeza nthawi ya mwininyumba. Mwacitsanzo, mukapangana naye nthawi, yesetsani kuisunga, mosasamala kanthu mmene anthu a kudera lanu amaonera nkhani yosunga nthawi. Kuonjezera apo, zingakhale bwino kwambiri kusatenga nthawi yaitali pa phunziro lanu loyamba. Ofalitsa ena aluso amakamba kuti ndi bwino kumaliza phunziro la Baibo mwamsanga ngakhale kuti wophunzira akali kufuna kumva zambiri. Ndipo pewani kulankhula zoculuka. Muzimulola wophunzira wanu kufotokozapo maganizo ake.​—Miy. 10:19.

12. Kodi tiyenera kukhala ndi colinga canji tikangoyamba kutsogoza phunziro la Baibo?

12 Kungoyambira paciyambi, colinga canu cizikhala kuthandiza wophunzira wanu kudziwa Yehova ndi Yesu komanso kuti ayambe kuwakonda. Kuti tikwaniritse colingaci, tiyenera kugwiritsa nchito Mau a Mulungu m’malo mofotokoza zimene timaganiza. (Mac. 10:​25, 26) Mtumwi Paulo anali kuphunzitsa kwambiri nkhani zokhudza Yesu Khristu, amene Yehova anam’tumiza kuti adzatithandize kum’dziwa bwino Yehovayo ndi kum’konda. (1 Akor. 2:​1, 2) Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino kufunika kothandiza ophunzira atsopano kuti akulitse makhalidwe abwino omwe tingawayerekezere ndi golide, siliva, ndi miyala ya mtengo wapatali. (1 Akor. 3:​11-15) Makhalidwewa aphatikizapo cikhulupiriro, nzeru, kuzindikira, ndi kuopa Yehova. (Sal. 19:​9, 10; Miy. 3:​13-15; 1 Pet. 1:7) Tengerani kaphunzitsidwe ka Paulo mwa kuthandiza wophunzira wanu kukhala ndi cikhulupiriro colimba, komanso kukhala pa ubale wolimba ndi Atate wake wacikondi wakumwamba.​—2 Akor. 1:24.

13. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife oleza mtima komanso omvetsa pamene tikuthandiza anthu acidwi? (2 Akorinto 10:​4, 5) (Onaninso cithunzi.)

13 Tengerani kaphunzitsidwe ka Yesu mwa kukhala woleza mtima ndi kukhala womvetsetsa. Pewani kufunsa wophunzira wanu mafunso amene anagam’pangitse kukhala womangika. Ngati pali mfundo imene sakuimvetsa, pitani pa mfundo ina. Mfundo imene sakuimvetsayo mungakaikambirane ulendo wina. M’malo momukakamiza kuti abvomereze ciphunzitso cinacake asanakonzeke, m’patseni nthawi kuti coonadi cizike mizu mumtima mwake. (Yoh. 16:12; Akol. 2:​6, 7) Baibo imati ziphunzitso zabodza zili ngati “zinthu zozikika molimba” zimene tiyenera ‘kugwetsa.’ (Werengani 2 Akorinto 10:​4, 5.) Mau amene anamasulidwa kuti “zinthu zozikika molimba,” anamasulidwa kucokera ku mau am’cinenero coyambirira otanthauza “nsanja yolimba.” M’malo mogwetsa nsanjayo wophunzira wanu ali mkati, muyenera coyamba kum’thandiza kupanga Yehova kukhala Nsanja yake, kapena kuti Pothawira pake. Tikatero, cidzakhala cosabvuta kwa iye kusiya ziphunzitso zimene anali kuzikhulupirira kwambiri.​—Sal. 91:9.

Abale awiri a m’cithunzi capita akuphunzira buku lakuti “Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!” ndi mwamuna wacikulire uja. Pa shelufu yapafupi pali zinthu zacisilikali.

M’patseni nthawi yokwana wophunzira wanu kuti coonadi cizike mizu mwa iye (Onani ndime 13)


ATSOPANO AKABWERA KU MISONKHANO

14. Kodi tiyenera kucita nao motani atsopano amene akabwera ku misonkhano yathu?

14 Yehova amafuna kuti atsopano tizicita nao mokoma mtima mosasamala kanthu za cikhalidwe cao, mmene zacuma zilili paumoyo wao, kapena kumene acokera. (Yak. 2:​1-4, 9) Ndiye kodi tingaonetse bwanji kuti timawakonda anthu amene abwera ku misonkhano yathu?

15-16. Kodi tingawathandize bwanji atsopano kumva kuti ndi olandiridwa ku misonkhano yathu?

15 Anthu ena amabwera kumisonkhano yathu pofuna kudzaona mmene imacitikira, kapena analimbikitsidwa ndi munthu wakudera lina kuti akapezekepo. Conco, musazengereze kukambirana nao anthu otero akafika pamisonkhano yathu. Alandireni mwansangala, koma osati mocita kunyanya, kuopera kuti angacite manyazi. Apempheni kuti mukhalire nao pamodzi. Apatseni Baibo ndi zofalitsa zophunzirira zao-zao. Apo ai, muzionera nao limodzi pa zofalitsa zanu. Kuonjezera apo, ganizirani mmene akumvera. Mwamuna wina amene anafika pamisonkhano anauza m’bale amene anam’landira kuti anali womangika cifukwa ca mmene anabvalira. M’baleyo anam’thandiza kukhala womasuka ndipo anam’fotokozera kuti Mboni za Yehova ndi anthu ngati iyeyo. Mwamunayo anapita patsogolo mpaka kubatizika, koma sanaiwale mmene m’bale uja anacitira naye zinthu. Komabe tizikumbukukira izi: Pokambirana ndi alendo, misonkhano isanayambe kapena ikatha, aonetseni cidwi popanda kulowerera nkhani zao za munthu mwini.​—1 Pet. 4:15.

16 Cinanso cimene tingacite kuti tithandize atsopano kumva kuti ndi olandiridwa ndico kukhala aulemu tikamaceza, tikamapereka ndemanga, komanso tikamakamba nkhani kupulatifomu zokhudza anthu amene si Mboni kapena zikhulupiriro zao. Pewani kukamba mau amene angawakhumudwitse kapena omwe angamveke ngati tikuwatukwana. (Tito 2:8; 3:2) Mwacitsanzo, sitimayetsa n’komwe kunyoza zikhulupiriro za anthu amene si Mboni. (2 Akor. 6:3) Pa nkhaniyi, abale amene amakamba nkhani za anthu onse, ayenera kusamala kwambiri. Ayeneranso kuonetsa kuti akuganizira anthu amene si Mboni mwa kufotokozera mau kapena mfundo zimene sangazimvetse.

17. Kodi tiyenera kutani tikapeza anthu a maganizo abwino muutumiki?

17 Tsiku lililonse, nchito yathu yopanga ophunzira imakhala yofulumira kuposa n’kale lonse. Ndipo tizipezabe anthu amene ‘ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Tikawapeza, tisazengereze kuwapempha kuti tiyambe kuphunzira nao Baibo, kapena kuwaitanira kumisonkhano yathu. Mwa kutero, tidzawathandiza kuti ayambe kuyenda pamseu wopita kumoyo wosatha.​—Mat. 7:14.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi tingawathandize bwanji anthu a “maganizo abwino” pa ulendo woyamba?

  • Kodi tizikumbukira kucita zotani tikangoyamba kuphunzira Baibo ndi munthu?

  • Kodi tiyenera kucita ciani kuti atsopano azimva kuti alandiridwa akafika pamisonkhano yathu?

NYIMBO 64 Timasangalala Kuthandizila pa Nchito Yokolola

a MAU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Abale awiri afikira msilikali wopuma panchito yemwe wakhala pakhonde; alongo awiri akulalikira mwacidule kwa mzimayi wotangwanika.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani