Mafunso Ocokera kwa Owerenga
Kodi mlembi wa Miyambo 30:18, 19 anatanthauza ciani pomwe anati “njira ya mwamuna ndi mtsikana” ndi yosamvetsetseka?
Anthu ambiri, kuphatikizapo akatswiri ena a Baibo, samvetsa tanthauzo la mauwa. Mu Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano, Miyambo 30:18, 19 anaimasulira kuti: “Pali zinthu zitatu zimene nʼzodabwitsa kwambiri kwa ine, ndiponso zinthu 4 zimene sindizimvetsa. Zinthu zake ndi izi: Njira ya ciwombankhanga mumlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya sitima pakati-kati pa nyanja, ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.”
Kumbuyoku, mau akuti “njira ya mwamuna ndi mtsikana” tinali kuwamva kuti akunena za zinthu zoipa. N’cifukwa ciani tinali kuwaona conco? Mavesi ozungulira nkhaniyi amakamba zinthu zoipa zimene sizinena kuti “ndakhuta.” (Miy. 30:15, 16) Ndipo vesi 20 ikukamba za “mkazi wacigololo” amene akukamba kuti sanacite colakwa ciliconse. Conco, tinali kufotokoza kuti monga mmene zilili ndi njira ya ciwombankhanga mumlengalenga, njira ya njoka pamwala, kapena njira ya sitima yamakedzana pakati-kati pa nyanja, nayenso mwamuna angacite zinazake popanda anthu kudziwa. Pa cifukwa cimeneci, mau akuti “njira ya mwamuna ndi mtsikana” tinali kuwamva kuti akunena za mnyamata amene mwamacenjera anganyengerere mtsikana kuti agone naye.
Komabe, pali zifukwa zomveka zimene tingakambire kuti mavesi amenewa amakamba za zinthu zabwino. Mlembiyu anali kungofotokoza zinthu zimene zinali kum’cititsa cidwi.
Mau a Ciheberi coyambirira amacirikiza kaonedwe kakuti mavesiwa amakamba za zinthu zabwino. Mogwirizana ndi buku lakuti Theological Lexicon of the Old Testament, mau aciheberi omasuliridwa kuti “sindizimvetsa” pa Miyambo 30:18 “amafotokoza zinthu zimene munthu . . . waona kuti ndi zacilendo, zosatheka, kapena zodabwitsa kwambiri.”
Pulofesa wina dzina lake Crawford H. Toy wa pa yunivesite ya Harvard ku America, anakambanso kuti mavesiwa safotokoza zinthu zoipa. Iye anati: “Mfundo yake imakamba za kudabwitsa kwa zinthu zimene zafotokozedwa.”
Conco m’pomveka kunena kuti mau a pa Miyambo 30:18, 19 amafotokoza zinthu zabwino zodabwitsa kwambiri, zimene mwina sitingathe kuzimvetsa. Mofanana ndi mlembi wa Baibo ameneyu, nafenso timagoma ndi mmene ciwombankhanga cimaulukira m’mwamba kwambiri, mmene njoka imathamangira pamwala ngakhale kuti ilibe miyendo, mmene sitima yolemera imadutsira panyanja, ndi mmenenso mwamuna ndi mkazi amagwera m’cikondi n’kukhala umoyo wosangalala.