CUMA COCOKELA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 38-42
Yehova Amapeleka Mphamvu kwa Munthu Wotopa
40:29-31
Nkhwazi imakwanitsa kulenjekeka m’mlenga-lenga kwa maola ambili. Imacita bwanji zimenezi? Imati ikapeza mphepo yotentha imene ikukwela m’mwamba, nkhwaziyo imangozungulila m’mphepomo imene imaikwezela-kwezela m’mwamba. Ndiyeno ikapeza mphepo inanso yokwelelapo imaulukilamo ndi kupitiliza kumakwelela-kwelela m’mwamba
Mmene mphepo imathandizila nkhwazi kuuluka mosavuta cosakupiza mapiko, ni mmenenso Mulungu amatipatsila mphamvu zotithandiza kupitiliza kumulambila mokhulupilika