LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 October masa. 12-17
  • Cikondi ca Mulungu Cokhulupilika Cidzakhalapo Mpaka Kale-kale

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cikondi ca Mulungu Cokhulupilika Cidzakhalapo Mpaka Kale-kale
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIKUMBUKILA KUTI MFUNDO YAKUTI YEHOVA AMATIKONDA NDI CIPHUNZITSO COYAMBILILA CA M’BAIBO
  • MUZIGANIZILA CIKONDI CIMENE YEHOVA “ALI NACO PA INU”
  • DZIWANI ZIMENE ZIMAKUPANGITSANI KUKAIKILA
  • SANKHANI KUKHALABE WOKHULUPILIKA
  • Yehova Amakukonda Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Muzikhulupirira Kuti Yehova Amakukondani
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mmene Tingathetsele Zikaiko Zathu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Cikondi Cosasintha ca Yehova N’ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 October masa. 12-17

NKHANI YOPHUNZILA 41

NYIMBO 108 Cikondi Cokhulupilika ca Mulungu

Cikondi ca Mulungu Cokhulupilika Cidzakhalapo Mpaka Kale-kale

“ Yamikani Yehova, cifukwa iye ndi wabwino. Cikondi cake cokhulupilika cidzakhalapo mpaka kalekale.”​—SAL. 136:1.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tikambilana mmene tiyenela kuonela cikondi ca Yehova mogwilizana ndi mmene Malemba amacifotokozela, komanso mmene kucita zimenezo kungatithandizile kuti tisafooke tikakumana ndi mayeso.

1-2. Ndi bvuto liti limene Akhristu ambili amakumana nalo?

YELEKEZANI kuti bwato lili panyanja, ndipo panyanjapo pali cimphepo camphamvu camkuntho. Mafunde amphamvu akulikankhila uku ndi uku. Popanda kugwilitsa nchito nangula, mafundewo angalikankhile kulikonse bwatolo. Nangulayo angathandize kuti bwatolo lisatengeke pomwe cimphepoco cikuomba.

2 Pamene mukukumana ndi mayeso aakulu, mungakhale ngati bwato lotelo. Maganizo anu angamasinthe-sinthe. Tsiku lina mungakhale ndi cikhulupililo colimba cakuti Yehova amakukondani komanso amakuthandizani. Koma tsiku lotsatila, mungayambe kukaikila ngati Yehova amaona n’komwe zimene mukupitamo. (Sal. 10:1; 13:1) Mwina mnzanu angakuuzeni mau olimbikitsa ndipo kwa kanthawi mungamveko bwino. (Miy. 17:17; 25:11) Koma posakhalitsa, mungayambenso kukaikila zakuti Yehova akukuthandizani. Mungafike ngakhale poganiza kuti Yehova amakuonani kuti ndimwe wacabe-cabe kapena sakukondani. Kodi mungacite ciani kuti mukhale ndi maganizo okhazikika, ngati bwato lokhala ndi nangula pamene mukukumana ndi mayeso? M’mau ena tingati, mungacite ciani kuti mukhalebe otsimikiza kuti Yehova amakukondani komanso amakuthandizani?

3. Malinga ndi Salimo 31:7 komanso 136:​1, kodi “cikondi cokhulupilika” cimatanthauza ciani? Ndipo n’cifukwa ciani tinganene kuti Yehova ndi citsanzo cabwino koposa pankhani yoonetsa cikondi cokhulupilika? (Onaninso cithunzi.)

3 Cimodzi cimene cingatithandize kukhala osasunthika tikakumana ndi mayeso ndi kukumbukila cikondi cokhulupilika ca Yehova. (Welengani Salimo 31:7; 136:1.) Mau akuti “cikondi cokhulupilika” angatanthauze cikondi cacikulu komanso cosasintha cimene munthu ali naco pa munthu wina. Yehova ndi citsanzo cabwino koposa pa nkhani yoonetsa “cikondi cokhulupilika.” Baibo imam’fotokoza kuti ndi “wacikondi cokhulupilika coculuka.” (Eks. 34:​6, 7) Kunena za Yehova, Baibo imakambanso kuti: “Mumasonyeza cikondi cokhulupilika coculuka kwa onse amene amaitana inu.” (Sal. 86:5) Zimenezi zitanthauza kuti Yehova sasiya atumiki ake okhulupilika. Kukumbukila kuti Yehova ndi wokhulupilika kungakuthandizeni kukhala wolimba pamene mukukumana ndi mayeso aakulu.​—Sal. 23:4.

Nangula amene alumikizidwa kubwato akuthandiza kuti bwatolo lisatengeke pomwe kuli cimphempo camkuntho.

Monga mmene nangula amathandizila kuti bwato lisatengeke pa nyanja pakakhala cimphepo camphamvu, kukhulupilila kuti Yehova amatikonda kudzatithandiza kukhala olimba tikakumana ndi mayeso (Onani ndime 3)


MUZIKUMBUKILA KUTI MFUNDO YAKUTI YEHOVA AMATIKONDA NDI CIPHUNZITSO COYAMBILILA CA M’BAIBO

4. Chulani zitsanzo za ziphunzitso za m’Baibo zoyambilila ndipo fotokozani cifukwa cake timazikhulupilila.

4 Cina cimene cingakuthandizeni kukhala olimba pa mayeso ndi kuona cikondi ca Yehova monga ciphunzitso coyambilila ca m’Baibo. Kodi mumaganizila ciani mukamva mau akuti “ciphunzitso coyambilila ca m’Baibo”? Mwina mumaganizila mfundo za coonadi zimene munaphunzila m’Mau a Mulungu. Mwacitsanzo, munaphunzila kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, ndipo Yesu ndi mwana wobadwa yekha wa Mulungu, komanso kuti akufa sadziwa ciliconse. Munaphunzilanso kuti dzikoli lidzakhala Paradaiso mmene anthu adzakhala kwamuyaya. (Sal. 83:18; Mlal. 9:5; Yoh. 3:16; Chiv. 21:​3, 4) Munakhulupilila kwambili ziphunzitsozi moti simukanalola kuti wina akupangitseni kuyamba kuzikaikila. Cifukwa ciani? Cifukwa munadziwa kuti ziphunzitsozi ndi zozikika mumfundo zosatsutsika za coonadi. Tiyeni tione mmene kuona cikondi ca Yehova monga ciphunzitso coyambilila ca m’Baibo kungakuthandizileni kuthetsa maganizo akuti Yehova saona kapena kusamala za mayeso amene mukukumana nao.

5. Fotokozani mmene munthu amalekela kukhulupilila ziphunzitso zabodza.

5 Pamene munayamba kuphunzila Baibo, n’ciani cinakuthandizani kukana ziphunzitso zabodza? Mosakaikila, cimene cinakuthandizani ndi kuyelekezela zimene munaphunzitsidwa ku cipembedzo canu ndi zimene Malemba amaphunzitsa. Mwacitsanzo, tinene kuti poyamba munali kukhulupilila kuti Yesu ndi Mulungu wamphamvuzonse. Koma pamene munali kuphunzila Baibo, munadzifunsa kuti, ‘Kodi ciphunzitso ici n’coona?’ Pambuyo posanthula maumboni a m’Malemba, munapeza kuti zimenezo si zoona. Kenako munaleka kukhulupilila ciphunzitso cabodza cimeneco ndi kuyamba kukhulupilila coonadi ca m’Baibo ici cakuti: Yesu ndi “woyamba kubadwa wacilengedwe conse,” “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.” (Akol. 1:15; Yoh. 3:18) N’zoona kuti ziphunzitso zabodza zingakhale “zozikika molimba” ndipo cingakhale cobvuta kuleka kuzikhulupilila. (2 Akor. 10:​4, 5) Koma mutaphunzila coonadi, simunabwelele ku ziphunzitso zimene munali kukhulupilila poyamba.​—Afil. 3:13.

6. N’cifukwa ciani ndinu wotsimikiza kuti “cikondi ca Yehova cokhulupilika cidzakhalapo mpaka kalekale”?

6 Mungacitenso cimodzi-modzi ndi zimene munaphunzila m’Baibo zokhudza cikondi ca Yehova. Mukakumana ndi mayeso, ndiyeno mwayamba kukaikila cikondi ca Yehova, mungadzifunse kuti, ‘Kodi maganizo amenewa ndi oyenela?’ Yelekezelani zikaikilo zanu ponena za cikondi ca Yehova ndi mau a pa Salimo 136:​1, limene ndi lemba la mutu wa nkhani ino. N’cifukwa ciani Yehova amakamba kuti cikondi cake “n’cokhulupilika”? N’cifukwa ciani mau akuti “cikondi cake cokhulupilika cidzakhalapo mpaka kalekale” anabwelezedwa maulendo 26 mu Salimo 136? Monga taonela, mfundo yakuti Yehova ali ndi cikondi cokhulupilika pa anthu ake ndi ciphunzitso cacikulu ca m’Baibo mofanana ndi ziphunzitso zina za m’Mau a Mulungu zimene munazikhulupilila mosabvuta. Maganizo akuti Yehova amakuonani kuti ndinu wacabe-cabe kapena sakukondani ndi abodza. Kanani bodza limenelo mmene mungakanile mwamphamvu ciphunzitso ciliconse cabodza!

7. Chulan’koni malemba ena amene amatitsimikizila kuti Yehova amatikonda.

7 M’Baibo muli maumboni ambili otsimikizila kuti Yehova amatikonda. Mwacitsanzo, Yesu anauza otsatila ake kuti: “Ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zambili.” (Mat. 10:31) Yehova iyemwini anauza anthu ake kuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.” (Yes. 41:10) Onani kuti mauwa sananenedwe mokaikila. Yesu sananene kuti ‘Mungakhale ofunika kwambili,’ ndipo Yehova sananene kuti ‘Ndingakuthandize.’ M’malomwake, Yesu anati: “Ndinu ofunika kwambili” ndipo Yehova anati “Ndikuthandiza.” Ngati mwayamba kukaikila zakuti Yehova amakukondani pamene mukukumana ndi mayeso, malemba ngati amenewa angakuthandizeni kuti mumveko bwino. Koma kuposa pamenepo, angakutsimikizileni kuti iye amakukondani. Malembawa akufotokoza mfundo zosatsutsika. Mukasinkhasinkha malembawa ndi kupemphela kwa Yehova, inunso mudzatha kunena mau a pa 1 Yohane 4:16 akuti: “Ife tikudziwa komanso tikukhulupilila kuti Mulungu amatikonda.”a

8. Mungacite ciani ngati nthawi zina mumakaikila zakuti Yehova amakukondani?

8 Nanga bwanji ngati nthawi zina mumakaikilabe zakuti Yehova amakukondani? Yelekezelani mmene mukumvela ndi zimene mukudziwa. Tingasinthe mmene tikumvela koma cikondi ca Yehova monga mmene Malemba amaphunzitsila sicisintha-sintha. Kuganiza kuti Yehova satikonda kuli ngati kunena kuti mau a m’Baibo akuti “Mulungu ndi cikondi,” ndi abodza.​—1 Yoh. 4:8.

MUZIGANIZILA CIKONDI CIMENE YEHOVA “ALI NACO PA INU”

9-10. Kodi Yesu anali kukamba nkhani yanji pamene ananena mau akuti “Atatewo amakukondani,” malinga ndi Yohane 16:​26, 27? (Onaninso cithunzi.)

9 Tingadziwe zambili za cikondi ca Yehova mwa kuganizila mau amene Yesu anauza otsatila ake akuti: “Atatewo amakukondani.” (Welengani Yohane 16:​26, 27.) Yesu sananene mau amenewa kuti angosangalatsa ophunzila ake. Ndipo nkhani yonse ionetsa kuti Yesu sanali kukamba za mmene ophunzila ake anali kumvela pa nthawiyo. Koma anali kukamba za nkhani ina, nkhani ya pemphelo.

10 Yesu anali atangouza ophunzila ake kuti azipemphela kudzela mwa iye koma osati kwa iye. (Yoh. 16:​23, 24) Kunali kofunika kuti iwo adziwe zimenezi. Zioneka kuti Yesu ataukitsidwa, ophunzila ake anayamba kufuna kupemphela kwa iye. Ndipo iwo anali kuona Yesu monga bwenzi lao. Mwina anaganiza kuti cifukwa Yesu anali kuwakonda, iye anali kufuna kuti azimva zopempha zao kenako n’kuzipeleka kwa Atate ake. Koma Yesu anawauza kuti iwo sanafunike kuganiza motelo. Cifukwa ciani? Cifukwa iye anawauza kuti: “Atatewo amakukondani.” Mfundo imeneyi ndi mbali imodzi ya ciphunzitso coyambilila ca m’Baibo cokhudza pemphelo. Ganizilani mmene mfundoyi ikukukhudzilani: Mwa kuphunzila Baibo, mwafika pom’dziwa Yesu ndi kum’konda. (Yoh. 14:21) Koma mofanana ndi ophunzila a m’nthawi ya atumwi, inunso mungapemphele kwa Mulungu mwacidalilo podziwa kuti “amakukondani.” Nthawi zonse mukamapemphela kwa Yehova mumaonetsa kuti mumakhulupilila kuti iye amakukondani.​—1 Yoh. 5:14.

Zithunzi: Mwacidalilo, m’bale yemwe wakhala panja pabenci, akupemphelela zinthu zitatu zofunika. 1. Akupeleka cakudya kwa mkazi wake wodwala yemwe ali cigonele pabedi. 2. Mwana wake wamkazi akusangalala pomwe akuphunzila naye Baibo 3. Akuwelenga malisiti ambili.

Mungapemphele kwa Yehova ndi cidalilo podziwa kuti iyemwini “amakukondani” (Onani ndime 9-10)b


DZIWANI ZIMENE ZIMAKUPANGITSANI KUKAIKILA

11. N’cifukwa ciani Satana angakondwele kwambili tikamakaikila zakuti Yehova amatikonda?

11 N’ciani cimatipangitsa kukaikila zakuti Yehova amatikonda? Mwina mungayankhe kuti ndi Satana, ndipo mwa njila ina zimenezo n’zoona. Mdyelekezi “akufuna kutimeza,” ndipo ngati tikaikila zakuti Yehova amatikonda, iye amakondwela kwambili. (1 Pet. 5:8) Pajatu cikondi cake Yehova, n’cimene cinam’limbikitsa kuti apeleke dipo. Koma Satana amafuna kuti tiziona kuti ndife osayenelela dipolo. (Aheb. 2:9) Komanso kodi ndani amene amapindula tikamakaikila kuti Yehova amatikonda? Ndi Satana. Nanga ndi colinga ca ndani cimakwanilitsika tikaleka kutumikila Yehova cifukwa ca mayeso? Ndi ca Satana. Satana amafuna kuti tiziganiza kuti Yehova satikonda. Koma zoona zake n’zakuti iye ndiye sakondedwa ndi Yehova. Yehova analeka kum’konda Satana. Koma mwa zocita zake “zacinyengo kwambili,” amayesa kutipangitsa kuona ngati Yehova satikonda ife ndipo anatikana. (Aef. 6:11) Tikadziwa zolinga za mdani wathuyu, tidzakhala otsimikiza mtima “kumutsutsa Mdyelekezi.”​—Yak. 4:7.

12-13. Kodi ucimo umene tinatengela ungatipangitse bwanji kukaikila zakuti Yehova amatikonda?

12 Koma palinso cina cimene cingatipangitse kukaikila ngati Yehova amatikonda. N’ciani cimeneco? Ucimo wobadwa nao. (Sal. 51:5; Aroma 5:12) Ucimo wapangitsa kuti tikhale otalikilana ndi Mlengi wathu. Waononganso maganizo, mtima ndi thupi lathu.

13 Ucimo umatipangitsa kudziimba mlandu, kukhala ndi nkhawa, kudzimva osatetezeka komanso kucita manyazi. Tingamve mwa njila imeneyi tikacita chimo. Koma tingamvenso mwa njilayi cifukwa cokumbukila nthawi zonse kuti ndife opanda ungwilo, zimene n’zosiyana ndi mmene Mulungu anatilengela. (Aroma 8:​20, 21) Ife anthu opanda ungwilo tili ngati galimoto imene ili ndi theyala yoponca. Galimoto yotelo imalephela kuyenda bwino-bwino. Ifenso timalephela kucita zinthu bwino-bwino mmene Mulungu anatilengela. Conco, n’zosadabwitsa kuti nthawi zina zimatibvuta kukhulupilila kuti Yehova amatikonda. Zikakhala conco, tizikumbukila kuti Yehova ndi ‘Mulungu wamkulu komanso wocititsa mantha. . . [Amene] amasonyeza cikondi cokhulupilika kwa anthu amene amam’konda ndi kusunga malamulo ake.’​—Neh. 1:5.

14. Kodi kuganizila za dipo kungatithandize bwanji kuthetsa maganizo akuti Yehova sangatikonde? (Aroma 5:8) (Onaninso bokosi lakuti “Dzitetezeni ku ‘Cinyengo Camphamvu ca Ucimo.’”)

14 N’zoona kuti nthawi zina tingamadzione ngati ndife osayenelela cikondi ca Yehova. Ndipo kukamba zoona ndifedi osayenelela cikondi cake. Izi n’zimene zikupangitsa cikondi cake kukhala capadela kwambili. Palibe ciliconse comwe tingacite cotipangitsa kukhala oyenelela cikondi ca Yehova. Ngakhale n’telo, Yehova anapeleka dipo limene limaphimba macimo athu. Anacita zimenezi cifukwa cotikonda. (1 Yoh. 4:10) Kumbukilaninso kuti Yesu anabwela kudzapulumutsa ocimwa osati anthu angwilo. (Welengani Aroma 5:8.) Palibe munthu amene angacite zinthu mwangwilo, ndipo Yehova satiyembekezela kucita zimenezo. Tikadziwa kuti ucimo wathu ndi umene umatipangitsa kukaikila zakuti Yehova amatikonda, tidzayesetsa kukaniza maganizo akuti iye satikonda.​—Aroma 7:​24, 25.

Dzitetezeni ku “Cinyengo Camphamvu ca Ucimo”

Baibo imakamba za “cinyengo camphamvu ca ucimo.” (Aheb. 3:13) Kuonjezela pa kutikopa kuti ticite zoipa, ucimo ungatipangitse kuti nthawi zambili tizikaikila kuti Yehova amatikonda. Ndithudi, ucimo uli ndi “cinyengo camphamvu.”

Tingaganize kuti ife sitinganyengedwe. Mwacitsanzo, tingaganize kuti munthu sangatibele ndalama mwacinyengo. Komabe, ngati sitisamala ndalama zathu zonse zingabedwe.

Mofananamo tiyenela kukhala osamala ngati ucimo umene tinatengela wayamba “kutinyenga” kuti tiyambe kukhulupilila kuti Yehova satikonda. Ucimo ungapangitse kuti tizingoganizila zofooka ndi zolakwa zathu. Koma cimeneco ndi “cinyengo ca mphamvu” ca ucimo ndipo tiyenela kucikana.

SANKHANI KUKHALABE WOKHULUPILIKA

15-16. Tikakhalabe okhulupilika kwa Yehova tingakhale otsimikiza za ciani? Ndipo cifukwa ciani? (2 Samueli 22:26)

15 Yehova akufuna kuti tipange cisankho coyenela mwa “kukhala wokhulupilika kwa iye.” (Deut. 30:​19, 20) Tikatelo, nayenso adzakhala wokhulupilika kwa ife. (Welengani 2 Samueli 22:26.) Tikakhalabe okhulupilika kwa Yehova, sitiyenela kukaikila kuti adzatithandiza pa mabvuto alionse amene tingakumane nao pa umoyo wathu.

16 Monga taphunzilila m’nkhani ino, tili ndi zifukwa zabwino zokhalilabe olimba pamene tikukumana ndi mayeso. Tidziwa kuti Yehova amatikonda ndipo adzatithandiza. N’zimene Baibo imaphunzitsa. Tikayamba kukaikila ngati iye amatikonda, tiziganizila mfundo za coonadi zimene tidziwa pankhaniyi, m’malo moganizila kwambili mmene tikumvela panthawiyo. Tiyeni tipitilize kukhulupilila ndi mtima wonse mfundo ya coonadi yakuti cikondi ca Yehova cokhulupilika cidzakhalapo mpaka kalekale.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi tingapindule bwanji tikamakumbukila kuti mfundo yoti Yehova amatikonda ndi ciphunzitso coyambilila ca m’Baibo?

  • Kodi ucimo umene tinatengela ungatipangitse bwanji kukaikila zakuti Yehova amatikonda?

  • N’ciani cingatithandize kuleka kukaikila zakuti Yehova amatikonda?

NYIMBO 159 M’patseni Ulemelelo Yehova

a Malemba ena ndi Deuteronomo 31:​8, Salimo 94:​14, ndi Yesaya 49:15.

b MAU OFOTOKOZELA CITHUNZI: M’bale akupemphela kwa Yehova kuti am’thandize kusamalila mkazi wake wodwala, kuti agwilitse nchito bwino ndalama zake, komanso kuti aphunzitse mwana wake kukonda Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani