LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 October masa. 24-29
  • Musamaiwale Kupemphelela Anthu Ena

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Musamaiwale Kupemphelela Anthu Ena
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUPEMPHELELA ANTHU ENA?
  • AMENE AMAFUNIKILA MAPEMPHELO ATHU
  • TIKAMAPEMPHELELA ALIYENSE PAYEKHA-PAYEKHA
  • TIZIWAONA MOYENELA MAPEMPHELO ATHU
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Mungatani Kuti Muzipemphela Mocokela Pansi pa Mtima?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 October masa. 24-29

NKHANI YOPHUNZILA 43

NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde

Musamaiwale Kupemphelela Anthu Ena

“ [Muzipemphelelana] . . . Pembedzelo la munthu wolungama limagwila nchito mwamphamvu kwambili.”​—YAK. 5:16.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tikambilane cifukwa cake kupemphelela ena n’kofunika komanso mmene tingacitile zimenezi.

1. Kodi tidziwa bwanji kuti Yehova amaona mapemphelo athu kukhala ofunika?

PEMPHELO ndi mphatso yapadela kwambili. Ganizilani izi: Yehova anagawilako angelo maudindo ena. (Sal. 91:11) Anapatsanso Mwana wake maudindo ena ofunika kwambili. (Mat. 28:18) Nanga bwanji udindo womvetsela mapemphelo? Uwu ndi udindo umene Yehova sanapatse aliyense. Yehova, “Wakumva pemphelo,” iyemwini amamvetsela mapemphelo athu.​—Sal. 65:2.

2. Kodi mtumwi Paulo anatipatsa citsanzo cotani pa nkhani yopemphelela anthu ena?

2 Timauza Yehova momasuka nkhawa zathu. Koma tifunikanso kupemphelela ena. N’zimene mtumwi Paulo anali kucita. Mwacitsanzo, anauza mpingo wa ku Efeso kuti: “Ndikupitilizabe kukupemphelelani.” (Aef. 1:16) Iye anali kupemphelelanso munthu payekha-payekha. Mwacitsanzo, anali kupemphelela Timoteyo. Pa nthawi ina, anamuuza kuti, “Ndikuthokoza Mulungu, . . . ndipo sindiiwala kukuchula m’mapemphelo anga opembedzela usana ndi usiku.” (2 Tim. 1:3) Nayenso Paulo anali ndi nkhawa zake zimene anafunika kupemphelelapo. (2 Akor. 11:23; 12:​7, 8) Komabe, anali kupatulanso nthawi yopemphelela ena.

3. N’ciani cingatipangitse kuiwala kupemphelela anthu ena?

3 Nthawi zina, tingaiwale kupemphelela ena. Cifukwa ciani? Mlongo wina dzina lake Sabrinaa anafotokozako cifukwa cimodzi. Anati: “Masiku ano timakhala otanganidwa kwambili moti tingamangoganizila za mabvuto athu, n’kumapemphelela zofuna zathu zokha.” Kodi izi zimakucitikilani nthawi zina? Ngati n’telo, nkhani ino ikuthandizani. (1) Ifotokoza cifukwa cake kupemphelela ena n’kofunika. (2) Ipelekanso malingalilo othandiza a mmene tingacitile zimenezi.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUPEMPHELELA ANTHU ENA?

4-5. Kodi ndi motani mmene kupemphelela ena ‘kumagwilila nchito mwamphamvu kwambili’? (Yakobo 5:16)

4 Kupemphelela ena ‘kumagwila nchito mwamphamvu kwambili.’ (Welengani Yakobo 5:16.) Kodi kupemphelela anthu ena kungasinthedi zinthu mu umoyo wao? Inde. Yesu atadziwa kuti mtumwi Petulo posacedwa adzam’kana, anati: “Ine ndakupemphelela kuti cikhulupililo cako cisathe.” (Luka 22:32) Nayenso Paulo anali kudziwa kuti pemphelo lingasinthe zinthu. Pamene anamangidwa pamlandu wabodza ku Roma, analembela Filimoni kuti: “Ndikhulupilila kuti cifukwa ca mapemphelo anu, ndimasulidwa kuti ndidzakutumikileni.” (Filim. 22) N’zimene zinacitikadi. Posapita nthawi, Paulo anamasulidwa ndipo anayambilanso kulalikila.

5 Koma izi sizitanthauza kuti tikapemphela timakakamiza Yehova kuti acitepo kanthu. Iye amaona mmene atumiki ake amakhudzidwila ndi mabvuto a ena, ndipo nthawi zina angasankhe kucitapo kanthu mogwilizana ndi mapemphelo ao. Kudziwa zimenezi kuyenela kutilimbikitsa kupemphela mocokela pansi pa mtima n’kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova.​—Sal. 37:5; 2 Akor. 1:11.

6. Kodi kupemphelela anthu ena kumatithandiza kukhala ndi khalidwe liti? (1 Petulo 3:8)

6 Kupemphela ena kumatithandiza kukhala ndi “cifundo cacikulu.” (Welengani 1 Petulo 3:8.) Munthu wacifundo amadziwa mabvuto amene wina akukumana nao ndipo amafuna kum’thandiza. (Maliko 1:​40, 41) Mkulu wina, dzina lake Michael, anati: “Ndikamapemphelela ena, ndimayamba kumvetsa mabvuto amene akukumana nao. Izi zimapangitsa cikondi canga pa iwo kukula kwambili. Ndimamva kuti ndayandikilana nao kwambili ngakhale kuti nthawi zina iwo sangadziwe zimenezi.” Mkulu winanso, dzina lake Richard, anafotokoza ubwino wina wopemphelela ena. Anati: “Tikamapemphelela munthu wina, timalimbikitsidwa kuti tim’thandize.” Anatinso: “Tikamathandiza munthu amene tinali kum’pemphelela, zimakhala ngati tikuthandiza kuti mapemphelo athu okhudza munthuyo ayankhidwe.”

7. Kodi kupemphelela ena kungatithandize bwanji kuti tiziona mabvuto athu moyenela? (Afilipi 2:​3, 4) (Onaninso zithunzi.)

7 Kupemphelela anthu ena kumatithandiza kuona mabvuto athu moyenela. (Welengani Afilipi 2:​3, 4.) Tonsefe timakumana ndi mabvuto pokhala kuti tili m’dziko lolamulidwa ndi Mdyelekezi. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:12) Tikakhala ndi cizolowezi copemphelela anthu ena, timakumbukila kuti “abale [athu] padziko lonse akukumananso ndi mabvuto ngati omwewo.” (1 Pet. 5:9) Mpainiya wina, dzina lake Katherine, anakamba kuti: “Kupemphelela ena kumandikumbutsa kuti enanso akukumana ndi mabvuto. Mfundoyi imandithandiza kuti ndisamangokhalila kuganizila mabvuto anga.”

Zithunzi: Abale ndi alongo amene akukumana ndi mabvuto akupemphelela ena. 1. Kamtsikana kakupemphela katakhala pabedi. Kacithunzi kam’kati kaonetsa banja lina m’bwato limene likucoka kunyumba kwao cifukwa ca kusefukila kwa madzi. 2. Banja la pacithunzi capita likupemphela pamodzi. Kacithunzi kam’kati kaonetsa m’bale yemwe ali m’ndende. 3. M’bale wa pacithunzi capita yemwe ali m’ndende akupemphela. Kacithunzi kam’kati kaonetsa mlongo wacikulile ali cigonele pabedi ku cipatala. 4. Mlongo wa pacithunzi capita akupemphela. Kacithunzi kam’kati kaonetsa kamtsikana komwe kali pacithunzi coyambilila. Kamtsikanaka kakhala pakokha pomwe ana ena m’kalasi mwao akukondwelela tsiku la kubadwa.

Kupemphelela anthu ena kumatithandiza kuti tiziona mavuto athu moyenela (Onani ndime 7)d


AMENE AMAFUNIKILA MAPEMPHELO ATHU

8. Pelekani zitsanzo za anthu amene tingachule m’mapemphelo athu.

8 Kodi ndani amene tingachule m’mapemphelo athu? Pali anthu ambili amene tingapemphelele. Mwacitsanzo, tingapemphelele anthu amene akudwala, acicepele amene amasekedwa ndi kukakamizidwa ndi anzao a kusukulu kuti acite zosayenela, kapena okalamba. Tingapemphelelenso okhulupilila anzathu amene akutsutsidwa ndi a m’banja mwao kapena ndi boma. (Mat. 10:​18, 36; Mac. 12:5) Abale athu ena athawa kwao cifukwa ca zaciwawa zimene zikucitika m’dela lao. Ndipo ena akubvutika cifukwa ca matsoka a zacilengedwe. Ena mwa abale ndi alongo athu amenewa sitingawadziwe. Koma tikamawapemphelela timaonetsa kuti tikutsatila lamulo la Yesu lakuti “muzikondana.”​—Yoh. 13:34.

9. N’cifukwa ciani tiyenela kupemphelela abale amene akutsogolela m’gulu la Yehova komanso akazi ao?

9 Tingapemphelelenso abale amene akutsogolela m’gulu la Yehova. Abalewa aphatikizapo a m’Bungwe Lolamulila ndi amene amawathandiza, a m’Komiti ya Nthambi, abale oyang’anila madipatimenti pa maofesi a nthambi, oyang’anila madela, akulu pampingo, ndi atumiki othandiza. Ambili mwa abalewa ali ndi mabvuto ao, koma amadzipeleka ndi mtima wonse kuti atithandize. (2 Akor. 12:15) Mwacitsanzo, wadela wina, dzina lake Mark, anati: “Limodzi mwa mabvuto aakulu kwambili amene ndikukumana nao ndi kukhala kutali ndi makolo anga okalamba. Onse ali ndi thanzi lofooka. Ngakhale kuti mlongo wanga ndi mwamuna wake akuwasamalila, cimandiwawabe kuona kuti sindikucita zambili powathandiza.” Kaya tikudziwa mabvuto amene abale odzipeleka amenewa akukumana nao kapena ayi, tiyenela kumawachula m’mapemphelo athu. (1 Ates. 5:​12, 13) Tiyenelanso kupemphelela akazi ao, cifukwa thandizo lao limapangitsa amuna ao kupitilizabe kutumikila.

10-11. Kodi Yehova amamva mapemphelo athu amene timapeleka popanda kuchula dzina la m’bale kapena mlongo? Fotokozani.

10 Monga taonela, nthawi zambili timapemphelela magulu osiyana-siyana a abale ndi alongo athu. Mwacitsanzo, popanda kuganizila munthu wina wake, tingapemphe Yehova kuti athandize amene ali m’ndende, kapena kuti atonthoze amene anafeledwa. Mkulu wina, dzina lake Donald, anati, “Abale ndi alongo omwe akubvutika ndi oculuka kwambili moti nthawi zina timangopeleka pemphelo limodzi lolowetsamo onse.”

11 Kodi Yehova amasangalala nawo mapemphelo aconci? N’zosacita kufunsa! Popeza sitidziwa zonse zimene okhulupilila anzathu akufunikila, m’pake kupemphelela magulu a abale ndi alongo. (Yoh. 17:20; Aef. 6:18) Mapemphelo otelo amaonetsa kuti ‘timakonda gulu lonse la abale.’​—1 Pet. 2:17.

TIKAMAPEMPHELELA ALIYENSE PAYEKHA-PAYEKHA

12. Kodi kukhala wachelu kungatithandize bwanji kuti popemphela tizichula mwacindunji zimene ena akumana nazo muumoyo wao?

12 Muzikhala chelu. Kuonjezela pa kupemphelela magulu a abale ndi alongo, tiyenelanso kupemphelela munthu payekha mwa kum’chula dzina. Kodi pali aliyense mumpingo mwanu amene akudwala matenda osathelapo? Kodi mumpingo mwanu muli wacinyamata amene amakhala wosasangalala cifukwa cakuti anzake kusukulu amam’kakamiza kucita zosayenela? Kodi mulinso kholo limene likulela lokha mwana, ndipo likubvutika kumulela ‘m’malangizo a Yehova komanso kum’phunzitsa mogwilizana ndi zimene Yehova amanena?’ (Aef. 6:4) Mukamakhala chelu kuti muone mabvuto amene ena akukumana nao, mudzakulitsa cikondi canu pa iwo. Zimenezi zidzakuthandizani kuti muziwachula m’mapemphelo anu.b​—Aroma 12:15.

13. Tingatani kuti anthu amene sitinawaonepo tiziwachula m’mapemphelo athu?

13 Muziwachula maina powapemphelela. Tingacite zimenezi ngakhale kuti anthuwo sitinawaonepo. Mwacitsanzo, ganizilani abale ndi alongo athu amene ali m’ndende ku Crimea, Eritrea, Russia ndi Singapore. Ndipo pa jw.org mungapezepo maina a abale ndi alongo amene ali m’ndende.c Woyang’anila dela wina, dzina lake Brian, ananena kuti: “Kulemba dzina la m’bale kapena mlongo amene ali m’ndende ndi kuliwelenga mokweza, kumandithandiza kukumbukila munthuyo n’kumamuchula ndikamapemphela.”

14-15. Tingatani kuti m’mapemphelo athu tizichula mwacindunji zimene ena akukumana nazo?

14 Muzichula mwacindunji zimene akufunikila. Michael, amene tam’chula kuciyambi, anati: “Ndikawelenga nkhani zokhudza abale amene ali m’ndende ndimayesa kuganizila mmene ndikanamvela ndikanakhala kuti ndikukumana ndi zimene iwo akukumana nazo. Ndingamadele nkhawa mkazi wanga ndipo ndingamafune kuti azisamalidwa. Izi zimandithandiza kudziwa zimene ndingachule ndikamapemphelela abale okwatila amene ali m’ndende.”​—Aheb. 13:​3, mau a m’munsi.

15 Kuganizila umoyo wa tsiku ndi tsiku wa abale ndi alongo athu omwe ali m’ndende kudzatithandiza kudziwa zinthu zimene tingachule powapemphelela. Mwacitsanzo, tingapemphele kuti woyang’anila ndende aziwacitila zinthu mokoma mtima, komanso kuti akulu-akulu a boma alole abale athu kukhalanso ndi ufulu wolambila. (1 Tim. 2:​1, 2) Tingapemphelelenso abale ndi alongo amene ali mumpingo umodzi ndi m’bale womangidwayo kuti alimbikitsidwe ndi citsanzo cake. (1 Pet. 2:12) Enanso amene tingapemphelele ndi anthu amene si Mboni kuti aone makhalidwe abwino a m’bale kapena mlongo womangidwayo ndi kumvetsela uthenga wathu. Mfundo zimenezi zigwilanso nchito popemphelela abale ndi alongo amene akukumana ndi mayeso ena. Tikamakhala chelu, komanso tikamapemphelela ena mwa kuchula maina ao ndi kufotokoza mwacindunji zimene akufunikila, tidzaonetsa kuti ‘timakondana kwambili’.​—1 Ates. 3:12.

TIZIWAONA MOYENELA MAPEMPHELO ATHU

16. Kodi tingatani kuti tiziona mapemphelo athu moyenela? (Mateyu 6:8)

16 Monga taonela, mapemphelo athu angathandize kuti zinthu zisinthe pa umoyo wa anthu ena. Komabe, tiyenela kuona mapemphelo athu moyenela. Pamene tikupemphela, tizikumbukila kuti zimene tikupempha, Yehova azidziwa kale. Komanso, tizikumbukila kuti iye safunikila malangizo athu kuti athetse bvuto linalake. Yehova amadziwa zimene atumiki ake akufunikila ngakhale pamene iwo, kapena ife, tisanam’pemphe n’komwe. (Welengani Mateyu 6:8.) Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kupemphelela anthu ena? Kuonjezela pa zimene takambilana kale m’nkhani ino, kupemphelela anthu ena kumaonetsa kuti timasamala za iwo. Cikondi n’cimene cimatisonkhezela kupemphelelana. Ndipo Yehova amasangalala akaona atumiki ake akutengela citsanzo cake mwa kuonetsana cikondi.

17-18. Kodi kupemphelela okhulupilila anzathu tingakuyelekezele ndi ciani?

17 Mapemphelo athu amaonetsa kuti timawakonda Akhristu anzathu. Ndipo Yehova amayamikila zimenezo ngakhale kuti nthawi zina tingaone kuti mapemphelo athu sakuyankhidwa mmene tinali kuyembekezela. Kuti timvetse mfundoyi, tiyelekezele kuti pali banja limene lili ndi ana awili, wamwamuna ndi wamkazi. Ndipo mwana wamwamuna wadwala. Ndiye mwana wamkazi akucondelela atate ake kuti: “M’thandizeni mlongo wanga. Wadwala kwambili!” Tateyo akudziwa za kudwala kwa mwana wake, komanso amam’konda. Ndipo wayamba kale kucitapo kanthu. Koma pempho la mwana wake wamkazi likum’sangalatsa cifukwa lionetsa kuti amam’dela nkhawa mlongo wake.

18 Mofananamo, Yehova amatilimbikitsa kuti tizidelana nkhawa ndi kupemphelelana. Tikatelo, mapemphelo athu adzaonetsa kuti timawakondadi abale ndi alongo athu ndipo Yehova amaona zimenezi. (2 Ates. 1:3; Aheb. 6:10) Komanso monga mmene taphunzilila, nthawi zina mapemphelo athu angapangitse kuti zinthu zisinthe mu umoyo wa anthu ena. Conco, mulimonse mmene zingakhalile, musaiwale kupemphelela ena.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi mapemphelo athu ‘amagwila nchito mwamphamvu kwambili’ m’lingalilo lotani?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kupemphelela magulu a abale ndi alongo athu?

  • Kodi tingatani kuti pamene tipemphelela munthu aliyense payekha-payekha tizichula mwacindunji zimene akukumana nazo?

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

a Maina ena asinthidwa.

b Tambani vidiyo pa jw.org yakuti Takeshi Shimizu: Yehova Ni “Wakumva Pemphelo.”

c Kuti mupeze maina a okhulupilila anzathu amene ali m’ndende, pitani pa jw.org ku Chichewa n’kufufuza mau akuti “Mayiko Amene a Mboni za Yehova Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira.”

d MAU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Abale ndi alongo amene akukumana ndi mabvuto akupemphelela ena.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani