LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 October masa. 18-23
  • Kodi Mungatani Kuti Muzipemphela Mocokela Pansi pa Mtima?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mungatani Kuti Muzipemphela Mocokela Pansi pa Mtima?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIPEMPHELA KWA YEHOVA MOMASUKA
  • ZIMENE MUNGACITE KUTI MUZIPEMPHELA MOCOKELA PANSI PA MTIMA
  • MUZIGANIZILA MAPEMPHELO OCOKELA PANSI PA MTIMA OLEMBEDWA M’BAIBO
  • PITILIZANI KULIMBITSA UBWENZI NDI YEHOVA KUPITILA M’PEMPHELO
  • Musamaiwale Kupemphelela Anthu Ena
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Yehova “Amacilitsa Anthu Osweka Mtima”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 October masa. 18-23

NKHANI YOPHUNZILA 42

NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika

Kodi Mungatani Kuti Muzipemphela Mocokela Pansi pa Mtima?

“ Ndaitana ndi mtima wanga wonse. Ndiyankheni inu Yehova.”​—SAL. 119:145.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kuganizila mapemphelo olembedwa m’Baibo kungatithandize kuti tizipemphela mocokela pansi pa mtima.

1-2. (a) Kodi n’ciani cingatilepheletse kupemphela momasuka kwa Yehova? (b) Kodi tidziwa bwanji kuti Yehova amawamvetsela mwachelu mapemphelo athu?

KODI nthawi zina mapemphelo anu amakhala obweleza-bweleza, osacokela pansi pa mtima, kapena amwambo cabe? Ngati n’conco, dziwani kuti sindinu nokha. Popeza timakhala ndi zocita zambili, tingamapemphele mothamanga. Nthawi zina tingamapemphele momangika cifukwa codziona osayenelela kupemphela kwa iye.

2 Baibo imatitsimikizila kuti cofunika kwambili kwa Yehova sikulankhula mau ogometsa popemphela, koma kupemphela mocokela pansi pa mtima. Iye amamva “pempho la anthu ofatsa”. (Sal. 10:17) Popeza amasamala za ife, amakhala chelu kumvetsela mau alionse amene timakamba m’pemphelo.​—Sal. 139:​1-3.

3. Kodi tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?

3 Ndiye tingafunse kuti: N’cifukwa ciani tiyenela kumasuka popemphela kwa Yehova? Tingatani kuti tizipemphela mocokela pansi pa mtima? Kodi kuganizila mapemphelo ocokela pansi pa mtima a m’Baibo kungatithandize bwanji kuti tizipeleka mapemphelo okonzedwa bwino? Nanga tingatani ngati tili ndi nkhawa kwambili moti popemphela tikulephela kufotokoza mmene tikumvela? Tiyeni tipeze mayankho pa mafunso amenewa.

MUZIPEMPHELA KWA YEHOVA MOMASUKA

4. N’ciani cingatithandize kuti tisamakhale omangika popemphela kwa Yehova? (Salimo 119:145)

4 Kuzindikila kuti Yehova ndi bwenzi lathu lokhulupilika limene limafuna kuti zinthu zizitiyendela bwino kudzatithandiza kumapemphela momasuka. Umu ndi mmene wolemba Salimo 119 anali kuonela Yehova popemphela. Koma sikuti analibe mabvuto. Mwacitsanzo, anthu ena anali kumunenela mabodza. (Sal. 119:​23, 69, 78) Komanso nthawi zina, zolakwa zake zinali kumulefula. (Sal. 119:5) Ngakhale n’telo, sanali kukhala womangika popemphela.​—Welengani Salimo 119:145.

5. N’cifukwa ciani sitiyenela kulola manyazi kutilepheletsa kupemphela kwa Yehova? Fotokozani fanizo.

5 Yehova amafuna kuti ngakhale anthu amene acita chimo lalikulu azipemphela kwa iye. (Yes. 55:​6, 7) Conco, tikacita chimo tisalole manyazi kutilepheletsa kupemphela. Tiyelekezele motele: Woyendetsa ndeke amadziwa kuti afunika kufunsila malangizo kwa oyang’anila mayendedwe a ndeke akafunikila thandizo. Ndiye tinene kuti wasocela kapena wasokoneza zinazake. Kodi angalephele kupempha thandizo poopa kucita manyazi? Kutali-tali! Mofananamo, tiyenela kupemphela momasuka kwa Yehova ngakhale pamene tacimwa kapena pamene tikubvutika kupanga cisankho.​—Sal. 119:​25, 176.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUZIPEMPHELA MOCOKELA PANSI PA MTIMA

6-7. Kodi kuganizila makhalidwe a Yehova kungatithandize bwanji kuti tizipemphela mocokela pansi pa mtima? Fotokozani citsanzo. (Onaninso mau a m’munsi.)

6 Tikamamasuka kwa Yehova, mwa kumuuza za kukhosi kwathu m’pemphelo, timam’yandikila kwambili. Ndiye tingatani kuti tizipemphela momasuka?

7 Muziganizila makhalidwe a Yehova.a Tikamaganizila kwambili makhalidwe ake, cidzakhala cosabvuta kupemphela kwa iye momasuka. (Sal. 145:​8, 9, 18) Ganizilani citsanzo ca Mlongo Kristine, amene atate ake anali aciwawa. Iye anati: “Kulankhula kwa Yehova monga Atate wanga kunali kobvuta kwa ine. N’nali kuganiza kuti Yehova adzaleka kundikonda cifukwa ca zophophonya zanga.” Kodi ndi khalidwe liti la Yehova lomwe linam’thandiza? Iye anati: “Kuganizila cikondi cokhulupilika ca Yehova kumandithandiza kumva kuti ndine wotetezeka. Ndikudziwa kuti iye sadzandisiya. Ndipo ngakhale n’talakwitsa zinazake, iye adzapitiliza kundithandiza mwacikondi. Izi zimandithandiza kukhala womasuka pom’fotokozela zinthu zimene zimandikondweletsa komanso zimene zimandidetsa nkhawa.”

8-9. Kuyamba taganizilapo pa zimene tichule m’pemphelo kuli ndi ubwino wanji? Fotokozani citsanzo.

8 Muziganizila zoti munene. Musanapemphele, zingakhale bwino kudzifunsa mafunso ngati awa: ‘Ndi mabvuto ati omwe ndikulimbana nao panopa? Kodi pali munthu amene ndifunika kum’khululukila? Ndi cothetsa nzelu catsopano citi cimene ndingafune kuti Yehova andithandize kuthetsa?’ (2 Maf. 19:​15-19) Tingatengelenso pemphelo la citsanzo la Yesu mwa kuganizila zimene tingapemphe kwa Yehova zokhudza dzina Lake, Ufumu Wake ndi cifunilo Cake.​—Mat. 6:​9, 10.

9 Mlongo wina, dzina lake Aliska, atadziwa kuti mwamuna wake wapezeka ndi khansa ya kuubongo, zinali zobvuta kwa iye kupemphela. Pokumbukila za nthawiyo, iye anati: “N’nasokonezeka maganizo kwambili moti sindikanatha kupemphela zomveka.” Kodi n’ciani cam’thandiza? Anakamba kuti: “Ndisanapemphele ndimayamba ndaganizila bwino zimene ndifuna kunena. Kucita zimenezi kwandithandiza kuti ndisamapemphe zokhudza ine ndekha. Izi zimandikhazika mtima pansi ndipo ndimatha kupemphelela nkhani zosiyanasiyana.”

10. N’cifukwa ciani ndi bwino kucedwamo m’pemphelo? (Onaninso zithunzi.)

10 Musamapemphele mothamanga. N’zoona kuti mapemphelo aafupi angakhale othandiza. Koma mapemphelo otalikilapo moyenelela ndiwo angatithandize kwambili kufotokoza bwino za kukhosi kwathu.b Elijah, mwamuna wa Aliska, anakamba kuti: “Ndimapemphela mobweleza-bweleza patsiku. Ndipo cifukwa cakuti ndimapemphela kwa nthawi yaitali, ndamuyandikila kwambili Yehova. Ndimapemphela modekha podziwa kuti Yehova sakundifulumizitsa ngati kuti ndikumucedwetsa zinazake.” Kuti muzipemphela mosathamanga, yesani izi: Sankhani nthawi ndi malo kumene mungamapemphelele popanda zosokoneza, ndipo khalani ndi cizolowezi copemphela mosathamanga ngakhalenso motulutsa mau.

Zithunzi: 1. Dzuwa lisanatuluke, m’bale akusinkhasinkha. Pa thebulo pake pali Baibo yotsegula ndi kapu ya khofi. 2. Dzuwa latuluka, ndipo akali malo omwe aja. Akupemphela kwa nthawi yaitali.

Sankhani nthawi ndi malo kumene mungamapemphelele modekha popanda cosokoneza (Onani ndime 10)


MUZIGANIZILA MAPEMPHELO OCOKELA PANSI PA MTIMA OLEMBEDWA M’BAIBO

11. Kodi kusinkhasinkha mapemphelo ocokela pansi pa mtima a m’Baibo kungakuthandizeni bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “Kodi Mumamva Mmene Iwo Anali Kumvela?”)

11 Kuganizila mapemphelo ocokela pansi pa mtima komanso masalimo, kapena kuti nyimbo zopatulika zolembedwa m’Baibo, kungakuthandizeni kwambili. Mukaona mmene atumiki a Mulungu anali kukhuthulila za mumtima mwao kwa iye, inunso mudzalimbikitsidwa kupemphela momasuka. Pamene mukucita zimenezi, mungapezenso mau ena otamanda Mulungu amene mungagwilitse nchito popemphela. Ndipo mwacionekele, mudzapeza mapemphelo omwe muli mau ogwilizana kwambili ndi zimene mukukumana nazo.

Kodi Mumamva Mmene Iwo Anali Kumvela?

Atumiki okhulupilika a Yehova anapemphela kwa iye mocokela pansi pa mtima m’mikhalidwe yosiyana-siyana. Kodi munamvapo ngati iwo?

  • Pamene Yakobo anali kulimbana ndi nkhawa, m’pemphelo lake anaonetsa kuti anali woyamikila komanso anali ndi cikhulupililo.​—Gen. 32:​9-12.

  • Mfumu Solomo ali wacicepele, anaona ngati udindo umene Yehova anam’patsa wam’kulila. Conco, anapempha Yehova kuti am’thandize.​—1 Maf. 3:​7-9.

  • Davide atacita cigololo ndi Batiseba, anacondelela Yehova kuti alenge “mtima wolungama” mkati mwake.​—Sal. 51:​9-12.

  • Mariya atalandila utumiki watsopano, anatamanda Yehova.​—Luka 1:​46-49.

Zimene mungacite pa kuwelenga kwanu: Santhulani mau opezeka m’pemphelo la munthu wochulidwa m’Baibo. Kenako onani mmene Yehova anayankhila pemphelo la mtumiki wakeyo. Gwilitsani nchito mfundo zimene mwaphunzila.

12. Kodi ndi mafunso ati amene tingadzifunse tikamawelenga mapemphelo a m’Baibo?

12 Pamene mukuganizila mapemphelo a m’Baibo, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndani ananena mauwa, nanga panali pa cocitika canji? Kodi mau a m’pempheloli akugwilizana ndi zimene ndikupitamo? Kodi pempheloli likundiphunzitsa ciani?’ Kuti mupeze mayankho pa mafunsowa mungafunike kufufuza mozamilapo, ndipo m’pake kutelo.Tiyeni tioneko zitsanzo za mapemphelo otelo.

13. Ndi phunzilo lanji limene titengapo pa pemphelo la Hana? (1 Samueli 1:​10, 11) (Onaninso cithunzi )

13 Welengani 1 Samueli 1:​10, 11. Hana anapeleka pempheloli pa nthawi imene anali kukumana ndi mabvuto awili akulu-akulu. Bvuto loyamba n’lakuti sanali kubeleka. Laciwili, mkazi mnzake anali kumusautsa kwambili. (1 Sam. 1:​4-7) Ngati mukukumana ndi bvuto losathelapo, kodi pemphelo la Hana lingakuphunzitseni ciani? Hana anapeza mpumulo mwa kupemphela kwa nthawi yaitali ndi kukhuthulila Mulungu za mu mtima mwake. (1 Sam. 1:​12, 18) Ifenso tingapeze mpumulo ‘tikam’tulila Yehova nkhawa zathu’ mwa kum’fotokozela mmene tikumvela cifukwa ca mabvuto amene tikukumana nao.​—Sal. 55:22.

Zithunzi: 1. Hana akuyang’ana kumbali mwacisoni pomwe Elikana akusewela ndi ana ake awili. 2. Penina akumwetulila pomwe wafukatila mwana wake wakhanda. 3. Hana akupemphela mocondelela uku akulila. 4. Mkulu wa Ansembe Eli wakhala pa kampando atapinda manja. Akuyang’ana Hana ndi diso lankhudzule.

Hana anali kubvutika ndi nkhawa cifukwa cokhala wosabeleka komanso cifukwa cosautsika ndi mkazi mnzake. Pa nthawiyi, anakhuthulila Yehova za mumtima mwake (Onani ndime 13)


14. (a) N’cianinso cina cimene tingaphunzilepo pa citsanzo ca Hana? (b) Kodi kuganizila mapemphelo a m’Baibo kungatithandize bwanji kukonza bwino mapemphelo athu? (Onani mau a m’munsi.)

14 Patapita zaka zocepa Hana atabeleka mwana, dzina lake Samueli, anam’peleka kwa mkulu wa ansembe Eli. (1 Sam. 1:​24-28) M’pemphelo locokela pansi pa mtima limene Hana anapeleka, anaonetsa kuti Yehova amateteza atumiki ake okhulupilika ndi kuwasamalila.c (1 Sam. 2:​1, 8, 9) Sikuti mabvuto a Hana anali atathelatu. Kungoti iye anayamba kuganizila kwambili mmene Yehova anam’dalitsila m’malo moganizila kwambili za mabvuto ake. Kodi tiphunzilapo ciani? Tikamaganizila kwambili mmene Yehova wakhala akutithandizila tidzatha kupilila mabvuto osathelapo.

15. Tikamakumana ndi zopanda cilungamo, tingaphunzilepo ciani pa pemphelo la mneneli Yeremiya? (Yeremiya 12:1)

15 Welengani Yeremiya 12:1. Pa nthawi ina, mneneli Yeremiya anabvutikapo maganizo poona anthu oipa zinthu zikuwayendela bwino. Kuonjezela apo, anali kukhumudwa ndi zimene Aisiraeli anzake anali kum’cita. (Yer. 20:​7, 8) Tingamvetse mmene iye anamvela tikaona anthu oipa zinthu zikuwayendela bwino, kapena anthu akamatinyoza. Ngakhale kuti Yeremiya anafotokoza nkhawa zake, sanakambe kuti Mulungu ndi wopanda cilungamo. Cikhulupililo cake cakuti Yehova ndi Mulungu wacilungamo ciyenela kuti cinalimbilako ataona kuti Yehova akupeleka cilango kwa anthu ake opanduka. (Yer. 32:19) Ifenso tiyenela kufotokoza nkhawa zathu momasuka m’pemphelo tili ndi cikhulupililo cakuti Yehova pa nthawi yake adzathetsa zopanda cilungamo zonse zimene tikukumana nazo.

16. Kodi tingaphunzile ciani kwa Mlevi wina ngati sititha kucita zambili cifukwa ca zobvuta zina? (Salimo 42:​1-4) (Onaninso zithunzi.)

16 Welengani Salimo 42:​1-4. Nyimbo imeneyi inalembedwa ndi Mlevi amene analibe mwai wolambila ndi Aisiraeli anzake pakacisi. Salimo lake lionetsa mmene anali kumvela. Ifenso tingamvetse mmene anali kumvela ngati sititha kucoka panyumba, mwina cifukwa codwala kapena ngati takhomeledwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cathu. Nthawi zina tingakhale osangalala pomwe nthawi zina tingakhale ndi cisoni. Mulimonsemo, tiyenela kumuuza Yehova mmene tikumvela. Kucita izi kungatithandize kudziwa cimene cikutipangitsa kumva conco. Kungatithandizenso kuyamba kuona mabvuto athu moyenela. Mwacitsanzo, Mleviyu anazindikila kuti adzakhalanso ndi mwai wotamanda Yehova. (Sal. 42:5) Anaganizilanso mmene Yehova anali kum’samalila. (Sal. 42:8) Kupemphela kwa Mulungu mocokela pansi pa mtima kungatithandize kumvetsa cifukwa cake tikumva mwa njila inayake, kungatithandize kuona zinthu moyenela, komanso kungatithandize kupeza mphamvu zotithandiza kupilila.

Zithunzi: 1. Mlevi akupemphela mocondelela ali m’cipululu. 2. M’bale akupemphela ali khale pabedi m’cipatala. Pa miyendo pake pali Baibo yotsegula.

Mlevi amene analemba Salimo 42 anakhuthula za mumtima mwake kwa Mulungu. Tikamakhuthula za mumtima mwathu kwa Yehova m’pemphelo, tingayambe kuona zinthu moyenela (Onani ndime 16)


17. . (a) Kodi tingaphunzilepo ciani pa pemphelo la Yona? (Yona 2:​1, 2) (b) Kodi mau a m’buku la Masalimo angatithandize bwanji tikakumana ndi mabvuto? (Onani mau a m’munsi.)

17 Welengani Yona 2:​1, 2. Mneneli Yona anapeleka pempheloli ali m’mimba mwa cinsomba cacikulu. Ngakhale kuti Yona sanamvele Yehova, anali ndi cidalilo cakuti Mulungu adzamvetsela pemphelo lake. Popemphela, Yona anachula mau ambili a m’Masalimo.d Mwacionekele, anali kuwadziwa bwino Masalimowo. Kuganizila Masalimowo kunam’thandiza kukhala wotsimikiza kuti Yehova adzam’thandiza. Mofananamo, tikaloweza mavesi ena a m’Baibo, tidzatha kuwakumbukila pamene tikupemphela kwa Yehova m’nthawi zobvuta, ndipo adzatilimbikitsa.

PITILIZANI KULIMBITSA UBWENZI NDI YEHOVA KUPITILA M’PEMPHELO

18-19. Ngati nthawi zina timalephela kufotokoza mmene tikumvela popemphela, kodi mfundo ya pa Aroma 8:​26, 27 ingatilimbikitse bwanji? Fotokozani citsanzo.

18 Welengani Aroma 8:​26, 27. Nthawi zina tingalemedwe kwambili ndi nkhawa moti n’kulephela kufotokoza mmene tikumvela. Koma sikuti tilibe thandizo. Pa nthawi za conco, mzimu woyela “umacondelela” kwa Yehova m’malo mwa ife. Motani? Yehova anagwilitsa nchito mzimu woyela kuti alembe mapemphelo ambili m’Mau ake. Tikalephela kufotokoza maganizo athu momveka bwino, Yehova angatenge mau opezeka m’mapemphelo a m’Baibo ngati kuti acokela kwa ife ndipo angawayankhe.

19 Mfundoyi inathandiza mlongo wina wa ku Russia, dzina lake Yelena. Anaponyedwa m’ndende cifukwa copemphela ndi kuwelenga Baibo. Yelena anapanikizika maganizo kwambili moti kupemphela kunali kum’bvuta. Iye anakamba kuti: “Kenako n’nakumbukila mfundo yakuti ndikathedwa nzelu moti n’kulephela kudziwa zonena m’pemphelo, Yehova amatenga mapemphelo a atumiki ake akale . . . ngati mapemphelo ocokela kwa ine. . . . Izi zinandithandiza kwambili pa nthawi yobvuta zedi imeneyi.”

20. Tikakhala ndi nkhawa, kodi tingadzikonzekeletse bwanji kuti tipemphele?

20 Tikakhala ndi nkhawa, maganizo athu angamayendeyende pomwe tikupemphela. Kuti tikonzekeletse maganizo athu tingamvetsele kuwelengedwa kwa buku la Masalimo pa cipangizo. Tingacitenso bwino kulemba mmene tikumvela monga anacitila Mfumu Davide. (Sal. 18, 34, 142; tumau twapamwamba.) Komabe, palibe lamulo loikika la mmene tingadzikonzekeletsele popemphela. (Sal. 141:2) Mungagwilitse nchito njila imene ingakukomeleni.

21. N’cifukwa ciani tiyenela kupemphela ndi mtima wonse?

21 N’zolimbikitsa kwambili kudziwa kuti Yehova amamvetsa mmene tikumvela ngakhale tisananene ciliconse. (Sal. 139:4) Komabe, amasangalala akamva mapemphelo athu oonetsa kuti timam’dalila. Conco, musazengeleze kupemphela kwa Atate wanu wakumwamba. Gwilitsani nchito mau opezeka m’mapemphelo a m’Baibo. Pemphelani ndi mtima wonse. Muuzeni zimene zikukusangalatsani ndi zimene zikukudetsani nkhawa. Ndipo pokhala bwenzi lanu lenileni, Yehova sadzakusiyani.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’ciani cingakuthandizeni kuti muzipemphela kwa Yehova momasuka?

  • Kodi n’zinthu ziti zimene mungacite kuti mapemphelo anu azikuthandizani kumuyandikila kwambili Yehova?

  • Kodi kusinkhasinkha mapemphelo ocokela pansi pa mtima olembedwa m’Baibo kungakuthandizeni bwanji?

NYIMBO 45 Kusinkha-sinkha kwa Mtima Wanga

a Onan’koni ena mwa “Makhalidwe akuluakulu a Yehova” ochulidwa m’buku lakuti Malemba Othandiza pa Umoyo Wathu Wacikhristu pansi pa mutu wakuti “Yehova.”

b Mapemphelo oimilako mpingo nthawi zambili amakhala acidule.

c Hana popemphela anachula mau ofanana ndi amene Mose analemba. Mwacionekele, anali kupeza nthawi yosinkhasinkha Malemba. (Deut. 4:35; 8:18; 32:​4, 39; 1 Sam. 2:​2, 6, 7) Pambuyo pa zaka mahandiledi, Mariya, mai a Yesu, anakamba mau otamanda Mulungu ofanana kwambili ndi amene Hana anakamba.​—Luka 1:​46-55.

d Kuti muone zitsanzo, yelekezelani Yona 2:​3-9 ndi Salimo 69:1; 16:10; 30:3; 142:​2, 3; 143:​4, 5; 18:6; komanso 3:8. Apa mavesiwa aikidwa potsatila mmene Yona ananenela mfundo zake m’pemphelo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani