LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w16 June masa. 3-8
  • Yehova Amatiumba

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amatiumba
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • YEHOVA AMASANKHA ANTHU AMENE AFUNA KUWAUMBA
  • N’CIFUKWA CIANI YEHOVA AMATIUMBA?
  • MMENE YEHOVA AMATIUMBILA
  • Kodi Mumalola Kuti Woumba Wamkulu Akuumbeni?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Lolani Kuti Yehova Aumbe Maganizo na Khalidwe Lanu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
w16 June masa. 3-8
Woumba watenga dothi ndipo akuumba mphika

Yehova Amatiumba

“Inu Yehova, , . . . inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife nchito ya manja anu.”—YESAYA. 64:8.

NYIMBO: 89, 26

TIMAPINDULA BWANJI TIKAMVETSETSA . . .

  • mmene Yehova amasankhila anthu amene afuna kuwaumba?

  • cifukwa cake Yehova amaumba anthu ake?

  • mmene Mulungu amaumbila anthu amene amamumvela?

1. Kodi Yehova ni Woumba wamkulu m’njila ya bwanji?

MU November 2010, mbiya inayake yakale kwambili ya m’dziko la China, anali kuitsatsa pa mtengo wa madola pafupifupi 70 miliyoni, ku England. N’zocititsa cidwi kuona kuti woumba, angaumbe cinthu cokongola ndiponso codula kwambili kucokela kudothi. Yehova, amene amatiumba, ni wamkulu kuposa woumba wina aliyense. Baibulo imakamba kuti Yehova anapanga munthu wangwilo kucokela “kufumbi lapansi,” kapena kuti kudothi. (Genesis 2:7) Munthu ameneyo ni Adamu. Iye anali “mwana wa Mulungu” ndipo analengedwa m’njila yakuti azikwanitsa kutengela makhalidwe a Mulungu.—Luka 3:38.

2, 3. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Aisiraeli olapa?

2 Adamu atapandukila Mlengi wake, sanakhalenso mwana wa Mulungu. Komabe, mbadwa zambili za Adamu zasankha Yehova kukhala Wolamulila wawo. (Aheberi 12:1) Mwa kumvela Mlengi wawo, iwo amaonetsa kuti asankha Mulungu kukhala Atate wawo ndiponso wowaumba osati Satana. (Yohane 8:44) Kukhulupilika kwawo kwa Mulungu kumatikumbutsa Aisraeli olapa amene anati: “Inu Yehova, inu ndinu Atate wathu. Ife ndife dongo ndipo inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife nchito ya manja anu.”—Yesaya 64:8.

3 Masiku ano, olambila oona a Yehova amayesetsa kukhala odzicepetsa ndi omvela. Iwo amaona kuti ni mwai kucha Yehova kuti Atate wawo, ndipo afuna kuti iye aziwaumba. Kodi timayesetsa kukhala monga dothi lofewa limene Yehova angaumbile cinthu camtengo wapatali? Kodi timaona abale ndi alongo athu kuti akali kuumbidwa ndi Mulungu? Pofuna kutithandiza kuti tiziwaona moyenelela, tikambilana mmene Yehova amasankhila anthu amene afuna kuwaumba, cifukwa cake amawaumba, ndi mmene amawaumbila.

YEHOVA AMASANKHA ANTHU AMENE AFUNA KUWAUMBA

4. Kodi Yehova amasankha bwanji anthu amene amawakokela kwa iye? Pelekani zitsanzo.

4 Yehova saona anthu mmene ife timawaonela. M’malomwake, amaona mumtima ndipo amaona mmene aliyense wa ife alili. (Ŵelengani 1 Samueli 16:7b.) Yehova anacita zimenezi pamene anali kukhazikitsa mpingo wacikhiristu. Mulungu anakokela kwa iye ndi kwa Mwana wake anthu ambili amene anali kuonedwa otsika. (Yohane 6:44) Mwacitsanzo, mmodzi wa anthu amenewo anali Mfarisi wina dzina lake Saulo, amene anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe.” (1 Timoteyo 1:13) Koma Yehova anayesa mtima wa Saulo ndipo sanamuone monga dothi lacabecabe. (Miyambo 17:3) M’malomwake, Yehova anaona kuti Saulo angaumbidwe ndi kukhala ‘ciwiya cocita kusankhidwa’ kuti akalalikile “kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” (Machitidwe 9:15) Yehova anasankhanso anthu ena ndi kuwaumba kuti akhale ‘ziwiya zolemekezeka.’ Pa anthu amenewo panali ena amene kale anali kuledzela, kucita ciwelewele, ndi kuba. (Aroma 9:21; 1 Akorinto 6:9-11) Pamene anali kuphunzila Malemba, analimbitsa cikhulupililo cawo mwa Yehova ndipo anamulola kuti awaumbe.

Si udindo wathu kuweluza anthu a m’gawo lathu kapena a mumpingo

5, 6. Kodi kudziŵa kuti Yehova ni amene amatiumba, kuyenela kukhudza bwanji mmene timaonela (a) anthu a m’gawo lathu? (b) abale ndi alongo athu?

5 Timadziŵa kuti Yehova amasankha ndi kukoka anthu oyenelela. Ndiye cifukwa cake sitiyenela kuweluza anthu a m’gawo lathu kapena a mumpingo mwathu. Mwacitsanzo, mvelani zimene munthu wina dzina lake Michael anali kucita akaona Mboni za Yehova. Iye anati: “N’nali kuwanyalanyaza ndi kuwapewa. N’nali kucita zinthu mopanda ulemu. Patapita nthawi, n’nakumana ndi banja lina limene n’nakonda cifukwa ca makhalidwe awo abwino. Tsiku lina n’nadabwa kwambili n’tadziŵa kuti iwo anali a Mboni za Yehova. Khalidwe lawo labwino linan’cititsa kuzindikila kuti n’nali kuzonda a Mboni za Yehova cifukwa cosawadziŵa bwino ndiponso cifukwa ca zinthu zabodza zimene ena anali kuniuza zokhudza iwo.” Michael anali kufuna kuphunzila zambili ndipo anavomela phunzilo la Baibulo. Patapita nthawi, anabatizidwa ndi kukhala mtumiki wa nthawi zonse.

6 Tikamaona Yehova monga Wotiumba wathu, timayamba kuona abale ndi alongo athu moyenela. Tidzadziŵa kuti aliyense wa iwo akali kuumbidwa. Umu ndi mmene Yehova amawaonela. Iye amaona mmene mtima wao ulili ndipo adziŵa kuti kupanda ungwilo kudzatha posacedwapa. Adziŵanso kuti aliyense wa iwo angakhale munthu wabwino. (Salimo 130:3) Tingatengele Yehova mwa kuona abale athu mmene iye amawaonela. Tingagwile nchito pamodzi ndi Wotiumba wathu mwa kuthandiza abale ndi alongo kukula kuuzimu. (1 Atesalonika 5:14, 15) Akulu mumpingo ayenela kukhala citsanzo cabwino pankhani imeneyi.—Aefeso 4:8, 11-13.

N’CIFUKWA CIANI YEHOVA AMATIUMBA?

7. N’cifukwa ciani tiyenela kuyamikila cilango ca Yehova?

7 Mwina munamvelapo anthu ena akukamba kuti: ‘Sin’nali kuyamikila cilango cimene makolo anga anali kunipatsa mpaka pamene n’nakhala ndi ana angaanga.’ Pamene tikula, tingayambe kuyamikila cilango pozindikila kuti timalangizidwa cifukwa ca cikondi. (Ŵelengani Aheberi 12:5, 6, 11.) Kukamba zoona, Yehova amatikonda monga ana ake, ndiye cifukwa cake amatipatsa cilango ndi kutiumba mwacikondi. Iye afuna kuti tikhale anzelu, okondwela, ndi kuti tizimukonda monga Atate wathu. (Miyambo 23:15) Iye sakondwela ngati tivutika, ndipo safuna kuti tife monga “ana oyenela kulandila mkwiyo wa Mulungu,” kutanthauza anthu osalapa.—Aefeso 2:2, 3.

Yehova amatikonda monga ana ake, ndiye cifukwa cake amatipatsa cilango ndi kutiumba mwacikondi

8, 9. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji masiku ano? Nanga maphunzilo amenewa adzapitiliza bwanji mtsogolo?

8 Tikalibe kudziŵa Yehova, mwina tinali ndi makhalidwe ambili oipa. Koma Yehova anatiumba ndi kutithandiza kusintha, ndiye cifukwa cake tili ndi makhalidwe abwino. (Yesaya 11:6-8; Akolose 3:9, 10) Tsopano tili m’Paradaiso wauzimu. Awa ni malo abwino amene Yehova watipatsa masiku ano otithandiza kuti tiumbike. M’Paradaiso ameneyu timakhala otetezeka ngakhale kuti tili m’dziko loipa. Anthu amene anakulila m’banja lopanda cikondi, amasangalala kukhala m’paradaiso wauzimu cifukwa abale ndi alongo amawakonda. (Yohane 13:35) Ndipo taphunzila kukonda anthu ena. Koma koposa zonse, tadziŵa Yehova Mulungu amene amatikonda monga atate wathu.—Yakobo 4:8.

9 M’dziko latsopano, tidzapindula mokwanila ndi paradaiso wauzimu. Tidzasangalala ndi moyo m’paradaiso weniweni pamene Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila dziko lonse. Panthawi imeneyo, Yehova adzapitiliza kutiumba ndi kutiphunzitsa m’njila imene sitinaganizilepo. (Yesaya 11:9) Yehova adzacititsa kuti maganizo ndi matupi athu akhale angwilo. Izi zidzacititsa kuti cikhale cosavuta kumvetsetsa malangizo ake ndi kuwatsatila. Conco, tiyeni tipitilize kulola Yehova kutiumba, ndipo tizionetsa kuti timayamikila cilango cake cimene amatipatsa cifukwa cotikonda.—Miyambo 3:11, 12.

MMENE YEHOVA AMATIUMBILA

10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji luso ndi kuleza mtima kwa Woumba Wamkulu?

10 Woumba waluso amadziŵa bwino dothi limene akuseŵenzetsa poumba. Nayenso Yehova amatidziŵa bwino kwambili. Amadziŵa zofooka zathu, zimene tingakwanitse kucita, ndi mmene tapitila patsogolo, ndipo amaganizila zimenezi akamatiumba. (Ŵelengani Salimo 103:10-14.) Tingadziŵe mmene Yehova amationela mwa kuganizila zimene Yesu anacita atumwi ake atalakwitsa zinazake. Nthawi zina, atumwi anali kukangana pankhani ya amene anali wamkulu pakati pao. Mukanakhalako panthawiyo, kodi sembe munamvela bwanji ndi zocita za atumwiwo? Mwina mukanaganiza kuti iwo ali monga dothi lolimba. Komabe, Yesu anadziŵa kuti iwo angasinthe ngati amvetsela malangizo ake amene anawapatsa mokoma mtima ndiponso ngati akhala odzicepetsa monga iye. (Maliko 9:33-37; 10:37, 41-45; Luka 22:24-27) Pamene Yesu anaukitsidwa, atumwiwo analandila mzimu wa Mulungu ndipo analeka kukangana za amene anali wamkulu pakati pawo. M’malomwake, anaika maganizo awo pa nchito imene Yesu anawapatsa.—Machitidwe 5:42.

11. Kodi Davide anaonetsa bwanji kuti anali monga dothi lofewa? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

11 Masiku ano, Yehova amaseŵenzetsa Baibulo, mzimu wake woyela, ndi mpingo kuti atiumbe. Kodi tifunika kucita ciani kuti Baibulo itiumbe? Tifunika kuiŵelenga, kuganizila mozama pa zimene taŵelenga, ndi kupempha Yehova kuti atithandize kugwilitsila nchito zimene taphunzila. Mfumu Davide anati: “Ndikakumbukila inu ndili pabedi langa, pa nthawi za ulonda wa usiku ndimasinkhasinkha za inu.” (Salimo 63:6) Iye anakambanso kuti: “Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolela.” (Salimo 16:7) Davide anasinkhasinkha malangizo a Yehova ndi kuwamvela ndipo anasintha maganizo ake ngakhale kuti sicinali copepuka kutelo. (2 Samueli 12:1-13) Davide anatipatsa citsanzo cabwino pankhani yodzicepetsa ndi kumvela. Conco, dzifunseni kuti: ‘Nikamaŵelenga Baibulo, kodi nimasinkhasinkha ndi kulola malangizo a Mulungu kusintha maganizo ndi mtima wanga? Kodi niyenela kuwonjezela nthawi imene nimacita zimenezi?’—Salimo 1:2, 3.

12, 13. Kodi Yehova amatiumba bwanji pogwilitsila nchito mzimu woyela ndi mpingo wacikhiristu?

12 Mzimu woyela ungatiumbe m’njila zosiyanasiyana. Mwacitsanzo, ungatithandize kutengela makhalidwe a Yesu ndi kuonetsa makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa. (Agalatiya 5:22, 23) Limodzi mwa makhalidwe amenewa ni cikondi. Timakonda Mulungu ndipo timafuna kumumvela ndi kumulola kutiumba cifukwa tidziŵa kuti malamulo ake amatipindulitsa. Kuonjezela apo, mzimu woyela ungatipatse mphamvu kuti tipewe kuumbidwa ndi dziko loipali. (Aefeso 2:2) Pamene mtumwi Paulo anali mwana, anali kutsatila zocita za atsogoleli acipembedzo ca Ciyuda. Koma mzimu woyela unamuthandiza kusintha. Patapita nthawi, iye analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Ifenso tiyenela kupempha mzimu woyela tili ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzayankha mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima.—Salimo 10:17.

Akulu aŵili akukonzekela, kenako akukambilana mfundo za m’Malemba ndi m’bale. Pambuyo pake m’baleyo akucita phunzilo laumwini

Yehova amaseŵenzetsa akulu acikhiristu kuti atiumbe, ndipo tifunika kumvela malangizo awo (Onani ndime 12,13)

13 Yehova amaseŵenzetsa mpingo ndi akulu kuti aumbe aliyense wa ife. Mwacitsanzo, akulu akadziŵa kuti tili ndi cifooko cinacake, amayesetsa kutithandiza. Komabe, sapeleka malangizo a m’mutu mwao. (Agalatiya 6:1) M’malomwake, iwo amapempha Yehova kuti awapatse nzelu ndi luso lomvetsa zinthu. Ndiyeno, amafufuza m’Baibulo ndi m’zofalitsa zathu kuti apeze mfundo zimene zingatithandize. Ngati akulu abwela kwa inu ndi kukuthandizani mwacikondi ndiponso mokoma mtima, mwina pankhani ya mmene mumavalila, muzikumbukila kuti malangizo awo ndi umboni wakuti Mulungu amakukondani. Mukaseŵenzetsa malangizo awo, mudzakhala monga dothi lofewa limene Yehova angaumbe mosavuta ndipo mudzapindula kwambili.

14. Ngakhale kuti Yehova amatiumba, kodi amalemekeza bwanji ufulu wathu wosankha?

14 Kumvetsetsa mmene Yehova amatiumbila, kungatithandize kukhala paubwenzi wabwino ndi abale ndi alongo. Cina, tidzayamba kuona anthu a m’gawo lathu ndi maphunzilo athu a Baibulo moyenelela. M’nthawi zakale, woumba mbiya anali kucotsa miyala ndi zinthu zina zosafunika mu dothi asanayambe kuumba. Woumba Wamkulu, Yehova, amathandiza anthu amene afuna kuumbidwa. Iye sawakakamiza kusintha, koma amawaphunzitsa miyezo yake yolungama. Ndiyeno, iwo afunika kusankha okha, kusintha kapena ai.

15, 16. Kodi ophunzila Baibulo amaonetsa bwanji kuti afuna kuumbidwa ndi Yehova? Pelekani citsanzo.

15 Mvelani zimene zinacitikila mlongo wina dzina lake Tessie, amene amakhala ku Australia. Iye anali ndi mwayi wophunzila Baibulo. Komabe, sanapite patsogolo, ndipo sanali kupita kumisonkhano. Mlongo amene anali kuphunzila naye, anapemphela kwa Yehova ndipo anaganiza zoleka kuphunzila naye. Ndiyeno, cinthu cina cosangalatsa cinacitika. Pamene anali kuphunzila, Tessie anafotokozela mlongo amene anali kumuphunzitsa cifukwa cake sanali kupita patsogolo kuuzimu. Iye anakamba kuti anali kudziona monga wacinyengo cifukwa anali kukonda kuchova njuga. Koma panthawiyo anali ataleka.

16 Pasanapite nthawi, Tessie anayamba kufika pamisonkhano ndipo anayamba kuonetsa makhalidwe acikhiristu ngakhale kuti mabwenzi ake akale anali kumuseka. Pambuyo pake, Tessie anabatizika ndi kukhala mpainiya wa nthawi zonse ngakhale kuti anali ndi ana aang’ono. N’zoonekelatu kuti ngati ophunzila Baibulo asintha kuti akondweletse Mulungu, Iye adzawayandikila ndi kuwaumba kuti akhale ziwiya zolemekezeka.

17. (a) Mumamvela bwanji mukaganizila kuti Yehova amakuumbani? (b) Tidzaphunzila ciani m’nkhani yotsatila?

17 Ngakhale masiku ano, anthu ena amaumba zinthu zokongola kwambili ndi manja awo. N’zimenenso Yehova amacita. Iye amatiumba moleza mtima mwa kutipatsa malangizo, ndipo amatiyang’anila kuti aone ngati tikuwatsatila kapena ai. (Ŵelengani Salimo 32:8.) Kodi mwaona kuti ndinu ofunika kwa Yehova? Kodi mwaona kuti Iye amakuumbani mosamala? Ngati n’conco, ni makhalidwe ati amene adzakuthandizani kukhala monga dothi lofewa limene Yehova angaumbe? Ni makhalidwe ati amene mufunika kupewa kuti musakhale dothi louma limene silingaumbike? Nanga makolo angacite ciani kuti aseŵenzele pamodzi ndi Yehova pophunzitsa ana awo? Nkhani yotsatila iyankha mafunso amenewa.

KUFOTOKOZA MAU ENA

  • Yehova amatiumba mwa kuseŵenzetsa Baibulo, mzimu wake woyela, ndi mpingo. Iye amatithandiza kusintha kuti tikhale anthu abwino

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani