Manuel Reino Berengui/DeFodi Images via Getty Images
KHALANI MASO!
Kodi Mpikisano wa Cikho ca Padziko Lonse Ungagwilizanitsedi Anthu?—Baibo Ikutipo Ciyani?
Anthu pafupifupi 5 biliyoni akhala akuonelela mpikisano wa Cikho ca Padziko Lonse, umene unayamba pa November 20 ndipo udzatha pa December 18, 2022. Ambili amaganiza kuti maseŵela ampikisano ngati amenewa angathandize kwambili, osati cabe kugwilizanitsa anthu openyelela.
“Maseŵela ali na mphamvu yosintha dziko. Ali na mphamvu yosonkhezela. Ali na mphamvu yogwilizanitsa anthu m’njila yapadela.”—Anatelo Nelson Mandela, pulezidenti wakale wa dziko la South Africa.
“Mpila wa miyendo . . . umagwilizanitsa anthu pa ciyembekezo, umawagwilizanitsa pa cimwemwe, umawagwilizanitsa pa cikondi, komanso umagwilizanitsa anthu a mitundu yosiyana-siyana.”—Anatelo Gianni Infantino, pulezidenti wa FIFA.a
Kodi mpikisano wa mpila wolimbilana Cikho ca Padziko Lonse kapena maseŵela ena aliwonse angagwilizanitsedi anthu? Kodi pali ciyembekezo cakuti padzikoli padzakhala mtendele na mgwilizano?
Kodi maseŵelawa amagwilizanitsadi anthu?
Pa mpikisano wa caka cino wa Cikho ca Padziko Lonse pacitika zambili osati maseŵela a mpila cabe. Maseŵelawa apangitsa anthu kuyamba kutsutsana pankhani zacikhalidwe komanso zandale monga zokhudza ufulu wa anthu, zacikhalidwe, komanso za kusiyana pa zacuma.
Ngakhale n’conco, anthu ambili amasangalala kuonelela maseŵela a padziko lonse ngati amenewa. Komabe, maseŵela amenewa sangabweletse mgwilizano wokhalitsa. M’malomwake, pa maseŵelawa pamaonekela kwambili makhalidwe ogaŵanitsa, amene Baibo inakambilatu kuti adzakhala cizindikilo ca ‘masiku otsiliza.’—2 Timoteyo 3:1-5.
Ciyembekezo codalilika ca mgwilizano wa padziko lonse
Baibo imapeleka ciyembekezo codalilika ca mgwilizano wa padziko lonse. Imalonjeza kuti anthu onse padzikoli adzakhala ogwilizana pansi pa ulamulilo wa boma lakumwamba lochedwa “Ufumu wa Mulungu.”—Luka 4:43; Mateyu 6:10.
Mfumu ya Ufumuwo, amene ni Yesu Khristu, adzaonetsetsa kuti padziko lonse pali mtendele. Baibo imati:
“Olungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendele nthawi zonse.”—Salimo 72:7.
“Adzalanditsa osauka amene akufuula popempha thandizo . . . Adzawombola miyoyo yawo ku cipsinjo ndi ciwawa.”—Salimo 72:12, 14.
Ngakhale masiku ano, ziphunzitso za Yesu zagwilizanitsa kale anthu mamiliyoni m’maiko 239. Iwo agonjetsa cidani. Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani za mutu wakuti “N’zotheka Kugonjetsa Cidani.”
a Mawu akuti FIFA atanthauza Fédération Internationale de Football Association, bungwe la padziko lonse loyang’anila maseŵela a mpila wa miyendo.