KHALANI MASO!
N’cifukwa Ninji Zandale Zikugaŵanitsa Anthu Conco?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Kusagwilizana pa zandale kwavutitsa anthu m’maiko ambili padziko lonse. Mwacitsanzo, kafukufuku amene bungwe lochedwa Pew Research Center linacita m’caka ca 2022 anaonetsa kuti “65% ya anthu acikulile a m’maiko 19 amene anatengako mbali pa kafukufukuyo anati m’maiko awo muli kusagwilizana kwakukulu pakati pa anthu a zipani zosiyana-siyana.”
Kodi nanunso mwaona kuti kumene m’makhala kusagwilizana kwa anthu pa zandale kukulila-kulila? Koma n’cifukwa ninji? Kodi thandizo lingacokele kuti? Onani zimene Baibo imakamba.
Maganizo ogaŵanitsa anthu
Baibo inakambilatu kuti m’nthawi yathu ino, yochedwa “masiku otsiliza,” anthu ambili adzakhala na maganizo amene amacititsa kukhala kovuta kuwazigwilizanitsa na anzawo.
“Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, . . . osafuna kugwilizana ndi anzawo.”—2 Timoteyo 3:1-3.
Ngakhale kuti alipo anthu ambili oyesa kucita zinthu mwacilungamo, maboma akulephelabe kuyendetsa bwino zinthu. Anthu a zipani zosiyana-siyana amalephela kuseŵenzela pamodzi kuti athetse mavuto. Zotulukapo zake n’zimene Baibo inanenelatu kalekale.
“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.”—Mlaliki 8:9.
Komabe, Baibo imaonetsa kuti yankho lothetsa vutoli lilipo. Yankho limenelo ni boma limene wolamulila wake akhoza kucotsapo mavuto onse amene anthu amakunana nawo masiku ano.
Mtsogoleli woyenelela komanso wacikondi
Baibo imatiuza kuti pali mtsogoleli mmodzi yekhayo amene angathe kucotsapo mavuto onsewa. Mtsogoleliyo ni Yesu Khristu. Yesu ali na mphamvu komanso ulamulilo, ndiponso ni wofunitsitsa kubweletsa mgwilizano na mtendele kwa anthu onse.
“M’masiku ake wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendele woculuka”—Salimo 72:7.
“Mitundu yonse ya anthu idzamutumikila.”—Salimo 72:11.
Yesu ndiye mtsogoleli woyenelela cifukwa amakonda anthu, ndiponso ni wofunitsitsa kuwathandiza, maka aja amene amacitidwa zopanda cilungamo.
“Adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzaombola miyoyo yawo ku cipsinjo ndi ciwawa.”—Salimo 72:12-14.
Dziŵani zambili zokhudza Ufumu wa Mulungu umene ni boma lakumwamba lotsogoleledwa na Yesu. Dziŵaninso mmene mungapindulile nawo ulamulilo wa bomalo, na mmene mungaucilikizile.
Tambani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciyani?
Ŵelengani nkhani yakuti “Ufumu wa Mulungu ni Boma Lopanda Ziphuphu.”