AspctStyle/stock.adobe.com
Yesu Adzathetsa Nkhondo
Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaonetsa cikondi cacikulu pa anthu moti anapeleka moyo wake monga nsembe cifukwa ca iwo. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Posacedwa, iye adzaonetsanso cikondi cake pa anthu poseŵenzetsa mphamvu zake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kuti athetse “nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—Salimo 46:9.
Onani zimene Yesu adzacita malinga n’zimene Baibo imakamba:
“Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawapulumutsa kuti asapondelezedwe komanso kucitilidwa zaciwawa.”—Salimo 72:12-14.
Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene Yesu anaticitila komanso zimene adzaticitila m’tsogolo? Njila imodzi ndi mwakuphunzila zambili zokhuza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu,” umene Yesu anali kulalikila. (Luka 4:43) Welengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”