panitan/stock.adobe.com
Yesu Adzathetsa Umphawi
Yesu ali pa dziko lapansi, anaonetsa cikondi cacikulu kwa anthu, maka-maka osauka komanso acisoni cacikulu. (Mateyu 9:36) Anafika popeleka moyo wake kuti athandize anthu ena. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Posacedwa, adzaonetsanso kuti amakonda anthu poseŵenzetsa ulamulilo wake na mphamvu zake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu pothetsa umphawi pa dziko lonse lapansi.
Posewenzetsa mawu andakatulo, Baibo imafotokoza zimene Yesu adzacita. Imati:
“Ateteze anthu onyozeka pakati pa anthu, Apulumutse ana a anthu osauka.”—Salimo 72:4.
Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene Yesu anaticitila komanso zimene adzaticitila m’tsogolo? Njila ndi mwakuphunzila zambili zokhuza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” umene Yesu anali kulalikila. (Luka 4:43) Welengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”