alfa27/stock.adobe.com
Yesu Adzacotsapo Anthu Osamvela Malamulo
Yesu adziŵa mmene cimamvekela munthu akamavutika cifukwa ca kusamvela malamulo na kupanda cilungamo kwa anthu ena. Iye anaimbidwapo mlandu wabodza, kumenyedwa, kuweluzidwa mopanda cilungamo, komanso kufa imfa yowawa. Ngakhale kuti anali wosalakwa, iye anali wokonzeka kupeleka “moyo wake dipo kuti awombole anthu ambili.” (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Tsopano pokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, iye adzabweletsa cilungamo padziko lonse lapansi, ndipo adzathetselatu zopanda cilungamo zonse.—Yesaya 42:3.
Baibo imafotokoza mmene dziko lapansi lidzakhalila Yesu akadzacitapo kanthu. Imati:
“Oipa sadzakhalaponso. Udzayangʼana pamene ankakhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:10, 11.
Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene Yesu anaticitila komanso zimene adzaticitila m’tsogolo? Njila imodzi ndi mwakuphunzila zambili zokhuza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” umene Yesu anali kulalikila. (Luka 4:43) Welengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?”