hadynyah/E+ via Getty Images
KHALANI MASO!
Njala Padziko Lonse Yawonjezeka Cifukwa ca Nkhondo Komanso Kusintha kwa Nyengo—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Nkhondo ya ku Ukraine komanso kusintha kwa nyengo, zapangitsa kuti pakhale kusoŵa kwa cakudya pa dziko lonse. Anthu ambili m’maiko osauka amavutika kuti apeze cakudya cokwanila.
“Kupanga cakudya komanso kupeza cakudya cokwanila kwakhala kovuta cifukwa ca nkhondo, kusintha kwa nyengo, kukwela mtengo kwa magetsi na mafuta komanso zinthu zina.”—Anatelo António Guterres, kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations, pa July 17, 2023.
“Popeza dziko la Russia linasiya kutumiza cakudya ku maiko ena kucoka ku Ukraine, akatswili anena kuti izi zingapangitse kuti vuto la cakudya liwonjezeke m’maiko osauka. Mitengo ya cakudya idzakwela kwambili, makamaka m’maiko a ku Kumpoto kwa Africa na ku Middle East.”—Inatelo lipoti ya pa Atalayar.com, pa July 23, 2023.
Onani zimene Baibo imakambapo pa vuto la cakudya komanso tsogolo lathu.
Baibo inakambilatu za vuto la cakudya
Yesu analosela kuti: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala.”—Mateyu 24:7.
Buku la Chivumbulutso limakamba za amuna anayi okwela pa mahosi. Mmodzi wa amuna okwela pa mahosiwo akuimila nkhondo. Wina amene akubwela pambuyo pake akuimila njala yadzaoneni panthawi imene cakudya cidzakhala cosoŵa kwambili, komanso ca mtengo woboola m’thumba. “Ndinaona hachi yakuda. Wokwelapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake. Kenako ndinamva mawu . . . akuti: ‘Kilogalamu imodzi ya tiligu, mtengo wake ukhala dinari imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balele, mtengo wake ukhala dinari imodzi.’”—Chivumbulutso 6:5, 6.a
Maulosi a m’Baibo onena za njala amenewa akukwanilitsidwa m’nthawi yathu ino, imene Baibo imaicha “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1) Kuti mudziŵe zambili za “masiku otsiliza,” komanso za okwela pamahachi ochulidwa m’buku la Chivumbulutso, tambani vidiyo yakuti Dziko Linasintha Kuyambila mu 1914 komanso ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Amuna Anayi Okwela pa Mahosi N’ndani?”
Mmene Baibo Ingatithandizile
Baibo ili na ulangizi wanzelu umene ungatithandize kudziŵa mocitila na zovuta zimene timakumana nazo, kuphatikizapo kukwela kwa mitengo ya cakudya, ngakhalenso kusoŵa kumene kwa cakudyaco. Onani zitsanzo m’nkhani yakuti “Zimene Mungachite Ngati Mukupeza Ndalama Zochepa.”
Baibo imatipatsanso ciyembekezo cakuti zinthu zidzakhala bwino. Imatiuza kuti nthawi izafika pamene “padziko lapansi padzakhala tiligu wambili,” moti munthu aliyense adzakhala na cakudya ca mwana alilenji. (Salimo 72:16) Ngati mufuna kudziŵa zambili za tsogolo limene Baibo ikulonjeza, komanso cifukwa cake muyenela kuikhulupilila, ŵelengani nkhani yakuti “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”
a “Dinari imodzi” inali malipilo a nchito ya tsiku lonse.