Photo by Zhai Yujia/China News Service/VCG via Getty Images
KHALANI MASO!
Kusefukila kwa Madzi Kowononga—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Anthu padziko lonse akuvutika cifukwa ca kusefukila kwa madzi kowononga. Tamvelani malipoti aya:
“M’masiku ocepa apitawa, ku likulu la dziko la China kunagwa cimvula cimene sicinagwepo m’zaka pafupifupi 140 zapitazo. . . . Kucokela pa Ciŵelu kufika pa Citatu, mu mzindawo munagwa cimvula cadzaoneni (mamilimita 744.8).”—Inatelo AP News, August 2, 2023.
“Lelo pa Cinayi, ni tsiku laciŵili namondwe Khanun akubweletsa cimvula camkuntho kum’mwela kwa Japan, ndipo anthu aŵili afa kale. . . . Akuti cimphepoci cidzabweletsa mvula yaikulu (mamilimita 600) m’dela la mapili pakati pa dziko la Taiwan.”—Inatelo Deutsche Welle, August 3, 2023.
“Kusefukila kwa madzi kumapeto kwa mlungu [ku Nova Scotia] kunacitika cifukwa ca mvula yaikulu imene siinagwepo kumadela a kumbali kwa Nyanja ya Atlantic, ku Canada, m’zaka 50 zapitazo.”—Inatelo BBC News, July 24, 2023.
Kodi Baibo imatipo ciyani pa zocitika ngati izi?
Cizindikilo ca “masiku otsiliza”
Baibo imanena kuti tikukhala m’nthawi yochedwa “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1) Yesu analosela kuti m’nthawi yathu, “kudzaoneka zoopsa,” kapena zinthu zocititsa mantha. (Luka 21:11) Kusintha kwa nyengo kwapangitsa kuti matsoka a zacilengedwe oopsa azicitika kaŵili-kaŵili komanso mosayembekezeleka.
Cifukwa cokhalila na ciyembekezo
Baibo imati zocititsa mantha zimene zikucitika masiku ano zimatipatsa cifukwa cokhalila na ciyembekezo. Motani? Yesu anati: “Mukadzaona zimenezi zikucitika, mudzadziwe kuti Ufumu wa Mulungu wayandikila.”—Luka 21:31; Mateyu 24:3.
Zocitika pa dzikoli zionetsa kuti posacedwa Ufumu wa Mulungu udzakonza zinthu zacilengedwe, kuphatikizapo zungulile-zungulile wa madzi.—Yobu 36:27, 28; Salimo 107:29.
Kuti mudziŵe zambili za mmene Ufumu wa Mulungu udzakonzela zinthu pa dziko, onani nkhani yakuti “Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?”