Rui Almeida Fotografia/Moment via Getty Images
KHALANI MASO!
Kodi Baibo Imatipo Ciani pa Ciwawa Cocitika Cifukwa ca Ndale?
Kuukila akulu-akulu a boma kwakhala kofala kwambili.
N’cifukwa ciani ciwawa cocitika cifukwa ca ndale cikuonjezeka? Kodi cidzatha? Nanga Baibo imakambapo ciani?
Baibo inakambilatu kuti anthu adzagawikana cifukwa ca ndale
Baibo inakambilatu kuti m’nthawi yathu ino, imene imati ndi “masiku otsiliza,” anthu ambili adzakhala ndi makhalidwe amene adzayambitsa ciwawa komanso kusagwilizana.
“Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Anthu adzakhala . . . osayamika, osakhulupilika, . . . osafuna kugwilizana ndi ena, . . . oopsa, . . . ocitila anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula cifukwa ca kunyada.”—2 Timoteyo 3:1-4.
Baibo inakambilatunso kuti zipolowe, monga anthu kuukila boma komanso mavuto a zandale, zidzaonjezeka m’nthawi yathu ino. (Luka 21:9, mawu a m’munsi) Ngakhale n’conco, ciwawa cocitika cifukwa ca ndale komanso kugawikana, sizidzakhalapo mpaka kalekale.
Kutha kwa ciwawa cocitika cifukwa ca ndale
Baibo imafotokoza kuti Mulungu adzacotsapo maboma onse a anthu ndipo adzakhazikitsa boma lake lakumwamba.
“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene . . . udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.
Ufumu wa Mulungu udzagwilizanitsa anthu ndipo udzabweletsa mtendele padziko lonse.
Wolamulila wake, Yesu Khristu, amachedwa “Kalonga Wamtendele,” ndipo iye adzaonetsetsa kuti “mtendele sudzatha.”—Yesaya 9:6, 7.
Ngakhale panopa, nzika za Ufumu umenewu zikuphunzila kukhala mwamtendele. Pa cifukwa cimeneci, Baibo imakamba kuti: “Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndipo mikondo yawo adzaisula kuti ikhale zida zosadzila mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunzilanso nkhondo.”—Yesaya 2:3, 4.
Kuti mudziwe zambili, welengani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?” ku Chichewa, ndiponso onelelani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?