KHALANI MASO!
Kuwombela Anthu Mfuti M’masukulu—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?
Pa May 24, 2022, mu tauni yaing’ono ya Uvalde, mu mzinda wa Texas, ku America, munacitika tsoka losaneneka. Nyuzipepala ya New York Times, inakamba kuti “mnyamata wina anawombela mfuti na kupha ana 19 komanso aphunzitsi aŵili . . . pa sukulu ya ana yochedwa Robb Elementary School.”
N’zomvetsa cisoni kuti zinthu zoopsa ngati zimenezi zakhala zikucitika kaŵili-kaŵili. Nyuzipepala yochedwa USA Today inanena kuti caka catha ku America kokha, “zocitika zowombela anthu m’masukulu zinakwana 249. Ciŵelengelo cimeneci n’cokwela kwambili kuposa caka ciliconse ciyambile mu 1970.”
Kodi n’cifukwa ciyani zocitika zankhanza zotelezi zimacitika? N’ciyani cingatithandize kuzipilila nkhanza zoipitsitsa za mtundu umenewu? Kodi tingakhale na ciyembekezo cakuti zaciwawa zimenezi zidzatha? Mayankho a mafunso amenewa amapezeka m’Baibo.
N’cifukwa ciyani zaciwawa zikuwonjezekabe padziko?
Baibo imacha nthawi imene tikukhalamo kuti “masiku otsiliza.” Ndipo inati panthawi imeneyi anthu adzakhala “osakonda acibale awo,” “oopsa,” ndiponso ocita zinthu zankhanza komanso zaciwawa. Anthu amakhalidwe amenewa “adzaipilaipilabe.” (2 Timoteyo 3:1-5, 13) Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?”
Anthu ambili amadzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani Mulungu sacitapo kanthu kuti zinthu zoipa monga kuwombela anthu mfuti m’masukulu zisamacitike?’ Kuti mudziŵe yankho la m’Baibo pankhaniyi, ŵelengani nkhani yakuti “N’cifukwa Ciyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana ndi Mavuto?”
Kodi nkhanza zoipa zimenezi tingazipilile bwanji?
“Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa Malembawa . . . amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.
Mfundo za m’Baibo zingakuthandizeni kupilila zaciwawa za m’dzikoli. Kuti mudziŵe zambili, onani magazini ya Galamukani! ya mutu wakuti “Kodi Anthu Adzasiya Kuchitiranana Zachiwawa?”
Ana akamva malipoti a nkhani zoopsa panyuzi amacita mantha kwambili. Kodi makolo angawathandize bwanji? Onani nkhani yakuti “Kodi Mwana Wanu Amaopa Akamva za Zimene Zacitika?”
Kodi zaciwawa zidzatha?
“Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”—Salimo 72:14.
“Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzila mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunzilanso nkhondo.”—Mika 4:3.
Mulungu adzakwanitsa kucita zimene anthu alephela. Boma lake lakumwamba, kapena kuti Ufumu wake, lidzacotsapo zida zonse zankhondo na kuthetsa ciwawa. Kuti mudziŵe zambili zimene Ufumu wa Mulungu udzacita, ŵelengani nkhani yakuti “Mu Ufumu wa Mulungu, pa Dziko ‘Padzakhala Mtendele Woculuka.’”