Kodi a Mboni za Yehova Amacita Nao Bwanji Anthu Amene Kale Anali m’Cipembedzo Cao?
Timayesetsa kuonetsa cikondi, kukoma mtima, komanso ulemu kwa anthu onse. Ngati wa Mboni za Yehova wafooka kapena wasiya kulambila nafe, timayesetsa kukambilana naye, timamutsimikizila kuti timamukonda, ndi kuyesetsa kumuthandiza kukhalanso paubwenzi ndi Mulungu.—Luka 15:4-7.
Nthawi zina, munthu angacite zinthu zimene zingamupangitse kuti acotsedwe mumpingo. (1 Akorinto 5:13) Komabe, popeza timawakonda kwambili okhulupilila anzathu, timayesetsa kumuthandiza munthuyo kuti asinthe n’colinga coti asacotsedwe mumpingo. Ndipo ngakhale atacotsedwa, timamuonetsabe cikondi ndi ulemu, potsatila zimene Baibo imatilimbikitsa kucita.—Maliko 12:31; 1 Petulo 2:17.
N’ciani cimacititsa kuti munthu acotsedwe mumpingo?
Baibo imakamba momveka bwino kuti ngati Mkhristu wacita chimo lalikulu ndipo safuna kusintha, ayenela kucotsedwa mumpingo. (1 Akorinto 5:11-13) Baibo imafotokoza momveka bwino macimo akulu-akulu amene angacititse kuti munthu acotsedwe mumpingo. Mwacitsanzo, imakamba za macimo monga cigololo, kuledzela, kupha munthu, kucitila nkhanza a m’banja lathu, komanso kuba.—1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21; 1 Timoteyo 1:9, 10.
Koma sikuti timangofikila kucotsa mumpingo munthu yemwe wacita chimo lalikulu. Coyamba, akulu mumpingoa amayesetsa kumuthandiza munthuyo kuti asinthe khalidwe lake. (Aroma 2:4) Akulu amakhala odekha, ofatsa komanso okoma mtima akamayesetsa kuti amufike pamtima munthu yemwe wacita chimoyo. (Agalatiya 6:1) Kucita zinthu mwanjila imeneyi kumathandiza wolakwayo kuzindikila colakwa cake ndipo amalimbikitsidwa kusintha. (2 Timoteyo 2:24-26) Koma ngati apitiliza kucita zimene Baibo imakamba kuti n’zolakwika ndipo safuna kulapa ngakhale kuti akulu ayesetsa mobweleza-bweleza kumuthandiza, munthuyo amacotsedwa mumpingo. Akulu amapeleka cilengezo cacidule kudziwitsa mpingo kuti munthuyo salinso wa Mboni za Yehova.
Akulu amakhala odekha, ofatsa komanso okoma mtima akamayesetsa kuti amufike pamtima munthu yemwe wacita chimoyo
Kodi kucotsa munthu amene safuna kusiya kucita zoipa kuli ndi mapindu otani? Mpingo umapindula cifukwa umatsatila mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino, ndipo zimathandiza kuti ena asatengele zocita zoipa za munthuyo. (1 Akorinto 5:6; 15:33; 1 Petulo 1:16) Phindu lina n’lakuti munthu wocimwayo akacotsedwa, zingamuthandize kusiya khalidwe lake loipa.—Aheberi 12:11.
Kodi a Mboni za Yehova amacita nao bwanji anthu amene acotsedwa mumpingo?
Pokamba za munthu amene wacotsedwa mumpingo, Baibo imalimbikitsa Akhristu kuti “musiye kugwilizana” naye munthuyo. Imapitiliza kunena kuti “ngakhale kudya naye munthu woteleyu ayi.” (1 Akorinto 5:11) Conco siticeza naye munthu amene anacotsedwa mumpingo. Ngakhale n’conco, sikuti timamupewelatu munthuyo. Iye ndi womasuka kupezeka pamisonkhano yathu, ndipo a Mboni za Yehova amene ali pamsonkhanowo angamupatse moni.b Timamuonetsa ulemu munthuyo. Iye angapemphenso thandizo kwa akulu kuti amuthandize kubwelela mumpingo.
Anthu amene acotsedwa mumpingo ndi omasuka kupezeka pamisonkhano yathu
Kodi zimakhala bwanji ngati munthu wacotsedwa mumpingo koma mnzake wa muukwati komanso ana ake akali Mboni za Yehova? Amapitiliza kucitila limodzi zinthu zimene amacita monga banja masiku onse, koma sapitiliza kucita naye zinthu zokhudza kulambila. Popeza akhala m’nyumba imodzi, amapitiliza kuonetsana cikondi monga banja cifukwa kucotsedwa mumpingo sikuthetsa cibale.
Munthu amene anacotsedwa mumpingo angapemphe akulu kuti akamucezele. Pamene akumucezela, akuluwo angapeleke uphungu wacikondi wa m’Malemba. Angamulimbikitse kuti alape ndi kubwelela mumpingo. (Zekariya 1:3) Ngati waleka kucita zoipa ndipo waonetsa m’zocita zake kuti akufunadi kutsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino, munthuyo amabwezeletsedwa mumpingo. Anthu mumpingo ‘amamukhululukila ndi mtima wonse ndiponso kumutonthoza,” monga mmene Akhrsitu a ku Korinto anacitila pamene munthu wocimwa anasintha n’kusiya makhalidwe ake oipa.—2 Akorinto 2:6-8.
Kod anthu amene anacotsedwa mumpingo amamva bwanji pambuyo pobwezeletsedwa?
Onani zimene Mboni za Yehova zina zinakamba pambuyo pobwezeletsedwa mumpingo.
“N’taganiza zobwelela mumpingo, n’nali kuona monga akulu adzafuna kudziwa zonse zimene ndinali kucita panthawi yonse imene ndinali wocotsedwa. M’malomwake, io anangondiuza kuti, ‘Tikufuna kuti uziganizila zimene ungacite kuti upite patsogolo.’ Mtima wanga unakhala pansi n’tangomva mau amenewo.”—Maria, wa ku America.
“Anthu mumpingo anamva bwino pamene ndinabwezeletsedwa. N’nadzimva kuti ndine wofunika. Abale ndi alongo anandithandiza kudziwa kuti io komanso Yehova anandikhululukila. Izi zinandithandiza kuleka kudziimba mlandu pa zocita zanga zakale. Akulu anali okonzeka kundithandiza kulimbitsanso ubwenzi wanga ndi Yehova. Anandilimbikitsa komanso kundithandiza kuona kuti Yehova akali kundikonda.”—Malcom, wa ku Sierra Leone.
“Zimandikondweletsa kudziwa kuti Yehova amawakonda kwambili anthu ake ndipo amafuna kuti gulu lake lizikhala loyela nthawi zonse. Ngakhale kuti anthu ena anganene kuti kucita izi ndi nkhanza, koma kucotsa munthu mumpingo n’kofunika ndipo kumaonetsa kuti timamukondadi munthuyo. Ndimayamikila kwambili kudziwa kuti Atate wathu wakumwamba ndi Mulungu wacikondi ndipo amakhululuka.”—Sandi, wa ku America.
a Akulu ndi amuna olimba mwauzimu omwe amaphunzitsa Malemba ndi kusamalila anthu a Yehova powathandiza ndi kuwalimbikitsa. Iwo salandila malipilo akamagwila ntchito yawoyi.—1 Petulo 5:1-3.
b M’zocitika zina zoipa kwambili, munthu angadzilekanitse ndi mumpingo komanso angamacite zinthu zoyesa kuuononga ndi kulefula awo amene ali mumpingo, kapena angayese kukopa ena kuti nawonso azicita zoipazo. Zimenezi zikacitika, timatsatila lamulo la m’Baibo lakuti ’tisapeleke moni’ kwa munthu woteloyo.—2 Yohane 9-11.