LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Betsileo
  • Lelo

Cisanu, October 10

Kuopa Yehova ndi ciyambi ca nzelu.​—Miy. 9:10.

Pokhala Akhristu, kodi tiyenela kucita ciyani zithunzi zamalisece zikaonekela pa cipangizo cathu? Tisaziyang’ane ngakhale pang’ono! Cingatithandize kutelo ni kukumbukila kuti ubale wathu na Yehova ni wamtengo wapatali. Ndipo ngakhale zithunzi zimene si zamalisece kwenikweni zingadzutse cilakolako ca kugonana. N’cifukwa ciyani nazonso tiyenela kuzipewa? Cifukwa sitifuna ngakhale pang’ono kuganizila zocita zaciwelewele. (Mat. 5:28, 29) Mkulu wina ku Thailand dzina lake David anati: “Nimadzifunsa kuti: ‘Olo kuti zithunzi zimenezi si zamalisece kwenikweni, kodi Yehova angakondwele nikapitiliza kuziyang’ana?’ Funso ngati limeneli limanithandiza kucita mwanzelu.” Mantha oyenela oopa kukhumudwitsa Yehova, amatithandiza kucita mwanzelu. Mantha aumulungu otelo ndiwo “ciyambi ca nzelu.” w23.06 23 ¶12-13

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, October 11

Inu anthu anga, pitani mukalowe mʼzipinda zanu zamkati.​—Yes. 26:20.

“Zipinda zamkati” zingaimile mipingo yathu. Pa cisautso cacikulu, Yehova adzatiteteza tikapitilizabe kum’lambila pamodzi na Akhristu anzathu. Cotelo, tiyenela kuyesetsa pali pano kukulitsa cikondi pa abale na alongo athu. Cipulumutso cathu cingadzadalile cikondi cathu pa iwo. “Tsiku lalikulu la Yehova” lidzakhala nthawi yovuta kwa anthu. (Zef. 1:14, 15) Nawonso atumiki a Yehova adzakumana na mavuto. Koma tikakonzekela pali pano, tidzakhalabe odekha na kuthandiza anthu ena. Tidzatha kupilila mavuto alionse amene tingadzakumane nawo. Okhulupilila anzathu akadzakumana na mavuto, tidzawaonetsa cifundo popeleka thandizo lofunikila kwa iwo. Ndipo tikaphunzila kuonetsa cikondi abale na alongo athu pali pano, cidzakhala capafupi kudzagwilizana nawo kwambili pa nthawi zovuta m’tsogolomu. Pamapeto pake, Yehova adzatifupa potipatsa moyo wosatha m’dziko limene matsoka na masautso adzakhala mbili yakale.​—Yes. 65:17. w23.07 7 ¶16-17

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Sondo, October 12

[Yehova] adzakupatsani mphamvu, adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupilika komanso adzakulimbitsani.​—1 Pet. 5:10.

Nthawi zambili Mawu a Mulungu amachula anthu okhulupilika kuti ni amphamvu. Koma ngakhale aja amene anali amphamvu kwambili si nthawi zonse pamene anali kudzimva telo. Nthawi zina Mfumu Davide anali kudzimva “wamphamvu ngati phili,” koma nthawi zina anali kudzimva wofooka ndipo anali “kucita mantha.” (Sal. 30:7) Ngakhale kuti Samisoni anali na mphamvu zapadela pamene mzimu wa Mulungu unali kugwila nchito pa iye, iye anazindikila kuti popanda mphamvu zocokela kwa Mulungu ‘angafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.’ (Ower. 14:5, 6; 16:17) Amuna okhulupilika amenewa anali olimba cifukwa Yehova ndiye anawapatsa mphamvu. Mtumwi Paulo anadziŵa kuti nayenso anafunikila mphamvu zocokela kwa Yehova. (2 Akor. 12:9, 10) Monga ambili a ife, mtumwi Paulo nayenso anali kulimbana na mavuto a thanzi. (Agal. 4:13, 14) Nthawi zina, zinalinso zovuta kuti acite coyenela. (Aroma 7:18, 19) Analinso kukhala na nkhawa pa zimene zidzamucitikila. (2 Akor. 1:8, 9) Komabe, pamene anali wofooka, m’pamene anali kukhala wamphamvu. Motani? Cifukwa Yehova anam’patsa mphamvu zimene anali kufunikila kuti apilile mavuto ake. w23.10 12 ¶1-2

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani