NYIMBO 112
Yehova, Mulungu wa Mtendele
Yopulinta
(Afilipi 4:9)
1. M’lungu mwalonjeza,
Kutipatsa mtendele.
Tipempha mutithandize,
Tikulitse mtendele.
Cikhulupililo
Cathu mwa Yesu Khristu,
Catithandiza kukhala
Pamtendele na imwe.
2. Titsogoleleni,
Ndipo mutiteteze
Na Mau na mzimu wanu,
Mu dziko lamdimali.
Tipemphela kuti
Imwe mutithandize
Kuti tisunge mtendele
Pakati pa abale.
3. Mwatisonkhanitsa,
Kumwamba na padziko,
Mwa mzimu tagwilizana,
Polengeza Ufumu.
Mu Ufumu wanu,
Simudzakhala nkhondo,
Olungama adzakhala
Pa mtendele kosatha.
(Onaninso Sal. 4:8; Afil. 4:6, 7; 1 Ates. 5:23.)