NYIMBO 113
Mtendele Wathu
Yopulinta
1. Yehova, ‘Tate wathu,
Ni wamtendele.
Adzathetsadi nkhondo,
Zonse pa dziko.
Kalonga wa Mtendele,
Ni Mwana wake.
Iye adzabweletsa,
Mtendele konse.
2. Mikangano, ukali,
Zonse tasiya.
Ise sitinyamula,
Zida za nkhondo.
Timakhululukila,
Otilakwila.
Monga nkhosa za Yesu,
Ndise ofatsa.
3. Anthu onse aone;
Mtendele wathu.
Ndipo adzatamanda,
Mulungu wathu.
Tisamale za ena,
M’zocita zathu.
Tidzaonetsa kuti
Ndise a M’lungu.
(Onaninso Sal. 46:9; Yes. 2:4; Yak. 3:17, 18.)