NYIMBO 11
Cilengedwe Citamanda Mulungu
Yopulinta
(Salimo 19)
1. Cilengedwe canu M’lungu wathu,
Ni camphamvu, ni cosangalatsa.
Cilengeza ucifumu wanu,
Cimapatsa anthu onse nzelu.
Cilengeza ucifumu wanu,
Cimapatsa anthu onse nzelu.
2. Malamulo anu ni oona,
Nthawi zonse timawadalila.
Mau anu amatithandiza—
Nthawi zonse kukhala anzelu.
Mau anu amatithandiza—
Nthawi zonse kukhala anzelu.
3. Ni dalitso kulambila imwe,
Kuyeletsa dzina lanu M’lungu.
Tikamvela malamulo anu,
Tidzapeza moyo wamuyaya.
Tikamvela malamulo anu,
Tidzapeza moyo wamuyaya.
(Onaninso Sal. 12:6; 89:7; 144:3; Aroma 1:20)