NYIMBO 94
Tiyamikila Mau a Mulungu
Yopulinta
	- 1. Tikuyamikani Atate wathu, - Cifukwa mwatipatsa Mau anu. - Amatitsogolela atipatsa nzelu. - Coonadi cake catimasula. 
- 2. Mau anu M’lungu, ali na mphamvu. - Akhudza zolinga za mtima wathu. - Mfundo zanu, Yehova, zitipatsa nzelu. - Zititsogolela m’zocita zathu. 
- 3. Mau anu M’lungu, atithandiza. - Kuphunzila kwa aneneli anu. - Conde tithandizeni tikhale olimba. - Tikuyamikani Mulungu wathu. 
(Onaninso Sal. 19:9; 119:16, 162; 2 Tim. 3:16; Yak. 5:17; 2 Pet. 1:21.)