LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Zinacitikadi?
    Nsanja ya Mlonda (Yogawila)—2016 | No. 2
    • Thupi la Yesu licotsedwa pa mtengo wozunzikilapo pamene ophunzila ake akuyang’ana capatali

      NKHANI YA PACIKUTO | N’CIFUKWA CIANI YESU ANAVUTIKA NDI KUTIFELA?

      Kodi Zinacitikadi?

      Mu 33 C.E., Yesu wa ku Nazareti anaphedwa. Iye anapatsidwa mlandu wabodza woukila boma, anamenyedwa mwankhanza, ndipo anakhomeledwa pamtengo. Iye anafa imfa yoŵaŵa. Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, ndipo patapita masiku 40 Yesu anabwelela kumwamba.

      Zocitika zapadela zimenezi zinalembedwa m’mabuku anai a Uthenga Wabwino a m’Malemba Acigiliki Acikristu, amene amadziŵika kuti Cipangano Catsopano. Kodi zimene zinalembedwa m’mauthenga amenewo zinacitikadi? Funso limeneli n’lofunika kwambili. Ngati zinthu zimenezo sizinacitike, ndiye kuti cikhulupililo ca Akristu n’copanda nchito, ndipo ciyembekezo cokhala ndi moyo m’Paladaiso ndi loto cabe. (1 Akorinto 15:14) Komabe, ngati zinthuzo zinacitikadi, ndiye kuti anthu ali ndi tsogolo labwino kwambili, limene inu mungauzeko ena. Koma kodi nkhani za m’Mauthenga Abwino zinacitika kapena sizinacitike?

      ZIMENE MAUMBONI AKUONETSA

      Mosiyana ndi nthano zabodza, nkhani za m’Mauthenga Abwino zinafufuzidwa mosamala ndi kulembedwa molondola. Mwacitsanzo, zimachula maina a malo enieni, ndipo ambili mwa malo amenewa anthu angapite kukawaona masiku ano. Cina, zimafotokoza anthu enieni, ndipo akatswili olemba mbili yakale amacitila umboni kuti anthuwo analikodi.—Luka 3:1, 2, 23.

      Olemba ena a m’nthawi ya atumwi komanso a m’zaka za m’ma 100 C.E., anachulapo za Yesu.a Njila imene Yesu anaphedwela yofotokozedwa m’Mauthenga Abwino ndi yofanana ndi njila zimene Aroma anali kugwilitsila nchito pakupha munthu. Kuonjezela apo, zocitika zimene analemba ndi zofanana m’njila yakuti zinalembedwa molondola ndiponso mosapita m’mbali. Iwo analembanso ngakhale zolakwa za ophunzila ena a Yesu. (Mateyu 26:56; Luka 22:24-26; Yohane 18:10, 11) Maumboni onsewa akuonetsa kuti olemba Mauthenga Abwino anali oona mtima, ndipo analemba zinthu zokhudza Yesu molondola kwambili.

      NANGA BWANJI ZA KUUKITSIDWA KWA YESU?

      Ngakhale kuti ambili amakhulupilila kuti Yesu anabweladi padziko lapansi kenako anaphedwa, ena amakaikila zakuti iye anaukitsidwa. Atumwi ake naonso sanakhulupilile pamene anamva lipoti lakuti iye waukitsidwa. (Luka 24:11) Komabe, pamene io ndi ophunzila ena anamuona Yesu woukitsidwayo panthawi zosiyanasiyana, m’pamene anakhulupilila. Ndipo panthawi ina, Yesu anaonekela kwa anthu oposa 500.—1 Akorinto 15:6.

      Molimba mtima, ophunzila a Yesu analengeza za kuukitsidwa kwake kwa anthu ambili kuphatikizapo amene anamupha, ngakhale kuti kucita zimenezo kunaika moyo wao pangozi. (Machitidwe 4:1-3, 10, 19, 20; 5:27-32) Kodi ophunzila ambili akanalimba mtima conco zikanakhala kuti sanali otsimikiza mtima kuti Yesu anaukitsidwadi? Kukamba zoona, mfundo yakuti Yesu anaukitsidwadi ndi imene inacititsa kuti Cikristu cifalikile kwambili m’nthawi zakale ngakhale masiku ano.

      Nkhani zokhudza imfa ya Yesu ndi kuukitsidwa kwake zolembedwa m’Mauthenga Abwino, ndi umboni wakuti nkhani zonse zofotokoza mbili yakale n’zoona. Kuŵelenga nkhani zimenezi bwinobwino, kudzakuthandizani kukhulupilila kuti zinacitikadi. Ndipo cikhulupililo canu cidzalimbanso mukamvetsetsa cifukwa cake zinthuzo zinacitika. Nkhani yotsatila ifotokoza zimenezi.

      a Ena mwa anthu amenewa ndi Tacitus, amene anabadwa mu 55 C.E. Iye analemba kuti Akristu anatengela dzinali kwa “Kristu” amene Pontiyo Pilato, mmodzi mwa olamulila athu, anamulamula kuti azunzidwe ndi kuphedwa mu ulamulilo wa mfumu Tiberiyo.” Enanso amene analemba za Yesu anali Suetonius, (wa m’nthawi ya atumwi), wolemba mbili yakale waciyuda Josephus (wa m’nthawi ya atumwi), ndi Pliny Wamng’ono amene anali bwanamkubwa wa ku Bituniya (wa kumayambililo kwa zaka za m’ma 100 C.E).

      N’cifukwa Ciani Pali Maumboni Ocepa Osakhala a m’Baibulo?

      Ponena za mmene zocita za Yesu zinakhudzila anthu padziko lapansi, kodi tingayembekezele kupeza maumboni ena a m’nthawi ya atumwi kuposa a m’Baibulo, amene akuonetsa kuti Yesu anali munthu weniweni ndi kuti anaukitsidwa? Osati kwenikweni. Coyamba, Mauthenga Abwino analembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Ndipo zolemba zina za m’nthawi imeneyo zikalipo. (1 Petulo 1:24, 25) Ndiyeno, anthu ambili amene anali kutsutsa Yesu sakanalemba zinthu zimene zikanapangitsa anthu kukhulupilila Yesu.

      Pankhani ya kuukitsidwa kwa Yesu, Petulo, amene anali mmodzi wa atumwi ake, anafotokoza kuti: “Ameneyu Mulungu anamuukitsa tsiku lacitatu ndi kumulola kuonekela, osati kwa anthu onse, koma kwa mboni zoikidwilatu ndi Mulungu, zomwe ndi ife amene tinadya ndi kumwa naye limodzi atauka kwa akufa.” (Machitidwe 10:40, 41) N’cifukwa ciani sanaonekele kwa anthu onse? Uthenga Wabwino wa Mateyu umatiuza kuti pamene atsogoleli acipembedzo amene anali adani a Yesu anamva kuti iye waukitsidwa, io anapeza njila yothetsela kufalitsidwa kwa nkhani yakuti Yesu wauka.—Mateyu 28:11-15.

      Kodi izi zitanthauza kuti Yesu anali kufuna kuti nkhani yakuti iye anaukitsidwa isafalikile? Iyai. Petulo anapitiliza kufotokoza kuti: “Anatilamula kuti tilalikile kwa anthu ndi kupeleka umboni wokwanila wakuti iyeyu ndi amene Mulungu anamuika kukhala woweluza anthu amoyo ndi akufa.” Akristu oona akhala akucita zimenezi kuyambila kale.—Machitidwe 10:42.

  • N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kutifela?
    Nsanja ya Mlonda (Yogawila)—2016 | No. 2
    • Anthu amitundu yosiyanasiyana akusangalala ndi umoyo m’Paladaiso

      NKHANI YA PACIKUTO

      N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kutifela?

      ‘Ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzela mwa ucimo.’—Aroma 5:12

      Adamu ndi Hava akuyang’ana cipatso coletsedwa; Adamu ndi Hava atakalamba; bokosi likukaikidwa kumanda

      Mungayankhe bwanji mutafunsidwa kuti, “Kodi mungakonde kukhala ndi moyo kwamuyaya?” Anthu ambili angakambe kuti inde, koma amaona kuti zimenezo sizingacitike. Iwo amakamba kuti anthufe tinalengedwa kuti tizifa.

      Koma bwanji ngati akufunsani kuti, “Kodi mwakonzekela kufa?” Anthu ambili angakambe kuti iyai. Izi zionetsa kuti mwacibadwa anthufe timafuna kukhalabe ndi moyo, ngakhale kuti timakumana ndi mavuto ambili. Baibulo limakamba kuti Mulungu analenga anthu ndi cifuno cokhala ndi moyo kwamuyaya. Limakamba kuti “[iye] anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Mlaliki 3:11.

      Koma zoona zake n’zakuti anthu sakhala ndi moyo kwamuyaya. Nanga n’ciani cinalakwika? Kodi Mulungu anacitapo ciliconse kuti akonze zinthu? Mayankho a m’Baibulo ndi okhazika mtima pansi, ndipo amaonetsa cifukwa cake Yesu anavutika ndi kufa.

      N’CIANI CINALAKWIKA?

      Macaputala atatu oyambilila a buku la Genesis m’Baibulo, amatiuza kuti Mulungu anapatsa anthu oyambilila Adamu ndi Hava mwai wakuti akhale ndi moyo kwamuyaya. Iye anawauza zimene anayenela kucita kuti akhale kwamuyaya. Macaputala amenewa afotokoza kuti iwo sanamvele Mulungu ndipo anataya mwai umenewo. Anthu ambili amaona kuti nkhani imeneyo ndi nthano cabe. Koma mofanana ndi mabuku a Uthenga Wabwino, zimene zinalembedwa m’buku la Genesis ponena za mbili yakale n’zoona.a

      Kodi n’ciani cinacitika pambuyo pakuti Adamu sanamvele Mulungu? Baibulo limayankha kuti: “Monga mmene ucimo unaloŵela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu] ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.” (Aroma 5:12) Mwakusamvela Mulungu, Adamu anacimwa. Zimenezi zinacititsa kuti ataye mwai wokhala ndi moyo kwamuyaya. Patapita nthawi, iye anafa. Popeza ndife mbadwa zake, tinatengela ucimo kwa iye. Ndiye cifukwa cake timadwala, timakalamba, ndi kufa. Izi n’zofanana ndi mmene mwana amatengela zocita za makolo ake. Kodi Mulungu anacitapo ciliconse kuti akonze zinthu?

      ZIMENE MULUNGU ANACITA

      Mulungu anapanga makonzedwe akuti abwezeletse mwai wokhala ndi moyo kwamuyaya umene Adamu anataya kwa mbadwa zake. Kodi Mulungu anacita bwanji zimenezo?

      M’Baibulo, pa Aroma 6:23 pamati: “Malipilo a ucimo ndi imfa.” Zimenezi zitanthauza kuti ucimo umabweletsa imfa. Adamu anacimwa, ndiye cifukwa cake anafa. Mofananamo, ifenso ndife ocimwa ndipo timalandila malipilo a ucimo amene ndi imfa. Conco, timabadwa ndi ucimo ngakhale kuti si mwakufuna kwathu. Mwacikondi, Mulungu anatuma Mwana wake, Yesu, kudzatilipilila “malipilo a ucimo.” Kodi zimenezi zinatheka bwanji?

      Anthu amitundu yosiyanasiyana akusangalala ndi umoyo m’Paladaiso

      Imfa ya Yesu inatsegula njila yodzakhala ndi moyo wacimwemwe komanso wamuyaya

      Popeza munthu mmodzi wangwilo, Adamu, anabweletsa ucimo ndi imfa mwa kusamvela Mulungu, panafunikanso munthu wangwilo womvela mpaka imfa n’colinga cakuti atimasule ku ucimo. Baibulo limafotokoza kuti: “Monga mwa kusamvela kwa munthu mmodziyo, ambili anakhala ocimwa, momwemonso kudzela mwa kumvela kwa munthu mmodziyu, ambili adzakhala olungama.” (Aroma 5:19) “Munthu mmodziyu,” ndi Yesu. Iye anacoka kumwamba, ndi kukhala munthu wangwilob, kenako anatifela. Pa cifukwa cimeneci, zinakhala zotheka kwa ife kuyesedwa olungama ndi kuima pamaso pa Mulungu, komanso kukhala ndi mwai wodzakhala ndi moyo kwamuyaya.

      CIFUKWA CAKE YESU ANAVUTIKA NDI KUFA

      Nanga n’cifukwa ciani Yesu anafunika kufa? Kodi Mulungu Wamphamvuyonse sakanangopeleka lamulo lakuti mbadwa za Adamu zikhale kwamuyaya? Iye anali ndi mphamvu yocita zimenezo. Koma kucita zimenezo kukanakhala kunyalanyaza lamulo lake lakuti malipilo a ucimo ndi imfa. Limenelo si lamulo wamba limene lingacotsedwe kapena kusinthidwa pofuna kusangalatsa ena. Lamulo limenelo limagwilizana kwambili ndi cilungamo cake.—Salimo 37:28.

      Ngati kuti Mulungu sanaonetse cilungamo pankhaniyi, anthu akanaganiza kuti Mulungu sangacite zinthu mwacilungamo pankhani zinanso. Mwacitsanzo, kodi cikanakhala cilungamo ngati akanasankha mbadwa zina za Adamu kuti zikhale kwamuyaya? Kodi anthu akanam’khulupilila kuti amasunga malonjezo ake? Cilungamo cimene Mulungu anatsatila kuti atipulumutse, cimatitsimikizila kuti iye amacita zinthu mwacilungamo nthawi zonse.

      Cifukwa ca nsembe ya Yesu, Mulungu anatsegula mwai wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi. Pa Yohane 3:16 Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” Imfa ya Yesu simangoonetsa cilungamo ca Mulungu, koma imaonetsanso cikondi cacikulu cimene Mulungu ali naco pa anthu.

      Nanga n’cifukwa ciani Yesu anavutika ndi kufa imfa yoŵaŵa monga mmene zinalembedwela m’Mauthenga Abwino? Mwa kukhalabe wokhulupilika pokumana ndi mavuto aakulu, Yesu anaonetselatu kuti zimene Mdyelekezi anakamba zakuti anthu sangakhale okhulupilika kwa Mulungu akakumana ndi, n’zabodza. (Yobu 2:4, 5) Zimene Satana anakamba zinaoneka monga n’zoona cifukwa poyamba anacititsa Adamu munthu wangwilo kucimwa. Koma Yesu, amene anali wangwilo monga Adamu, anakhalabe womvela ngakhale kuti anavutika kwambili. (1 Akorinto 15:45) Motelo, iye anaonetsa kuti zinali zotheka kwa Adamu kusankha kumvela Mulungu. Mwa kupilila pamene anali kuvutitsidwa, Yesu anatisiila citsanzo cakuti titsatile.(1 Petulo 2:21) Mulungu anadalitsa Mwana wake cifukwa ca kumvela mwa kumuukitsila kumoyo wosafa, kumwamba.

      MMENE MUNGAPINDULILE NDI IMFA YA YESU

      Imfa ya Yesu inacitikadi, ndipo inatsegula njila yodzakhala ndi moyo kwamuyaya. Kodi mukufuna kudzakhala ndi moyo wosatha? Yesu anafotokoza zimene tifunika kucita pamene anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

      Amene amafalitsa magazini ino akukupemphani kuti muphunzile zambili za Yehova, Mulungu woona, ndi za Mwana wake Yesu Kristu. A Mboni za Yehova amene ali m’dela lanu ndi okonzeka kukuthandizani. Mudzaphunzilanso zambili mukapita pa webusaiti yathu ya www.jw.org.

      a Onani nkhani yakuti “The Historical Character of Genesis,” m’buku lacingelezi la Insight on the Scriptures, pa tsamba 922, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

      b Mulungu anasamutsa moyo wa mwana wake ndi kuuika m’mimba mwa Mariya, ndipo iye anakhala ndi pakati. Mzimu woyela wa Mulungu unateteza Yesu kuti asatengele kupanda ungwilo kwa Mariya.—Luka 1:31, 35.

      Mkate wopanda cofufumitsa ukupelekedwa kwa anthu pa Cikumbutso

      “Muzicita Zimenezi”

      Usiku wakuti aphedwa maŵa, Yesu anasonkhana pamodzi ndi atumwi ake okhulupilika, kenako anayambitsa Cikumbutso ca imfa yake. Iye anawauza kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (Luka 22:19) Pomvela lamulo limeneli, Mboni za Yehova padziko lonse zimasonkhana kamodzi pa caka kuti zikumbukile imfa ya Yesu. Caka catha, anthu 19,862,783 anapezeka pa cocitika cimeneci.

      Caka cino, Cikumbutso ca imfa ya Yesu cidzakhalako pa Citatu, March 23, dzuŵa litaloŵa. Tikuitanilani inuyo, a m’banja lanu, ndiponso anzanu, kuti mudzapezekepo ndi kumvetsela nkhani ya m’Baibulo. Nkhaniyo idzafotokoza cifukwa cake imfa ya Yesu ndi yofunika ndi mmene ingakupindulitsileni inuyo panokha. Simudzalipila ndalama iliyonse, ndipo sipadzayendetsedwa mbale ya ndalama. Funsani a Mboni za Yehova a m’dela lanu kuti akuuzeni nthawi ndi malo kumene kudzakhalila cocitikaco. Kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.jw.org.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani