NYIMBO 129
Tidzapilila Mosalekeza
Yopulinta
	- 1. Yesu anati, - ‘Pililani mayeselo.’ - Anapeleka - citsanzo ca kupilila. - Anali kudziŵa - lonjezo la M’lungu. - (KOLASI) - Tiyeni tipilile. - Tikhale olimba. - Mwa mphamvu ya Yehova, - Ise tipilile mosaleka. 
- 2. Tingakumane - Na mavuto nthawi zina. - Koma tidziŵa - M’lungu adzatidalitsa, - Na moyo wosatha - m’dziko la mtendele. - (KOLASI) - Tiyeni tipilile. - Tikhale olimba. - Mwa mphamvu ya Yehova, - Ise tipilile mosaleka. 
- 3. Sitidzafo’ka - Kapena kucita mantha. - Tidzapilila - potumikila Yehova. - Mavuto adzatha - m’dziko latsopano. - (KOLASI) - Tiyeni tipilile. - Tikhale olimba. - Mwa mphamvu ya Yehova, - Ise tipilile mosaleka. 
(Onaninso Mac 20:19, 20; Yak 1:12; 1 Pet 4:12-14.)