NYIMBO 68
Fesani Mbewu za Ufumu
Yopulinta
1. Bwelani kwa Ambuye Yesu,
Kuti museŵenze naye.
Iye adzakuthandizani,
Adzakutsogolelani.
Mbewu za co’nadi zimakula
M’mitima ya omvetsela.
Modzipeleka citani mwakhama
Nchito imene mwapatsidwa.
2. Kuti nchito iyende bwino
Pafunika khama lanu.
Muthandizenso omvetsela
Kuti akonde co’nadi.
Athandizeni kudziŵa kuti
Angapilile mavuto.
Ngati mwaona mbewu za co’nadi
Zikula mudzasangalala.
(Onaninso Mat. 13:19-23; 22:37.)