Pemphani Zimene Mufuna
Kwa zaka zambili, mwina munali kulalikila ndi kuphunzitsa coonadi ca m’Mau a Mulungu mwa kugwilitsila nchito zofalitsa m’cinenelo cimene anthu ambili amakamba cimene si cinenelo canu kapena cinenelo ca anthu acidwi amene mumakumana nao. Tidziŵa kuti timagwila zinthu msanga ndipo timazimvetsa pamene tiphunzila m’cinenelo cathu. Ndiye cifukwa cake, timayesetsa kutembenuza ndi kusindikiza zofalitsa n’colinga cakuti zofalitsa zimenezi zipezeke m’zinenelo zambili kuposa kale lonse. Kodi mumazengeleza kufunsila mabuku oonjezeka maka-maka amene anatuluka pa msonkhano posacedwapa m’cinenelo canu? Kodi mukupempha zimene mufuna kuti muzilalikila mogwila mtima m’gawo lanu? Pansipa pali zofalitsa zimene zipezeka m’Cinyanja ndi m’Cisoli zimene zatuluka posacedwapa:
◻ Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu!
◻ Ndani Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?
◻ Mvetselani kwa Mulungu
◻ Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
Nthawi Imene Mungasunge Zofalitsa: Anthu a m’gawo lanu mwina amadziŵa zinenelo zambili koma amakamba cinenelo cimodzi masiku onse. Mukamalalikila, mungakumane ndi anthu, mabanja amene pocita zinthu zao za tsiku ndi tsiku amagwilitsila nchito cinenelo cosiyana ndi canu kapena cinenelo codziŵika kumaloko. Kodi munafufuza kuti mudziŵe ngati zofalitsa zathu zipezeka m’cinenelo cimeneco? Mpingo ungasungeko zofalitsa zocepa zimene timagwilitsila nchito mu utumiki zimene zipezeka m’cinenelo cimeneco, monga tumapepala twa uthenga, tumabuku tumene tunatulutsidwa posacedwapa, ndi buku la Baibo Imaphunzitsa. Ofalitsa angagaŵile zofalitsa zimenezi kulikonse kumene akumana ndi anthu amene amaŵelenga cinenelo cimeneco.
Mmene Mungaodele Zofalitsa Zimenezi: Ngati mpingo sumakhala ndi zofalitsa m’cinenelo cimene munthu wacidwi amaŵelenga, kodi mungaode bwanji zofalitsa m’cinenelo cimeneco? Ofalitsa ayenela kufunsa mtumiki wa mabuku kuti adziŵe zofalitsa zimene zili m’cinenelo cimeneco, kotelo kuti aode zofalitsazi pa oda yotsatila ya mpingo.
Tiyeni tipitilizebe kugwilitsila nchito bwino zofalitsa zathu kuti tithandize anthu “kaya akhale a mtundu wotani,” a cinenelo cotani, kuti “apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.”—1 Tim. 2:3, 4.