LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 11/13 tsa. 1
  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Hoseya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Hoseya
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 11/13 tsa. 1

Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Hoseya

1. Kodi ndi funso lotani limene mungadzifunse?

1 ‘Kodi ndine wofunitsitsa kudzimana ciani kuti nditumikile Yehova?’ Mwina munadzifunsapo funso limeneli posinkha-sinkha ubwino woculuka wa Mulungu ndi cifundo cake. (Sal. 103:2-4; 116:12) Hoseya anali wofunitsitsa kucita zimene Yehova anamuuza, ngakhale kuti zimenezo zinafuna kuti adzimane zinthu zina. Kodi tingam’tsanzile bwanji Hoseya?

2. Kodi tingatsatile bwanji citsanzo cabwino ca Hoseya pankhani yopitilizabe kulalikila?

2 Lalikilani M’nthawi Zovuta: Uthenga wa Hoseya unali kupita maka-maka kwa ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli, umene unatsala pang’ono kusiya kulambila koona. Mfumu Yerobowamu waciŵili anacita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo analimbikitsa kulambila fano la mwana wa ng’ombe kumene Yerobowamu woyamba anayambitsa. (2 Maf. 14:23, 24) Mafumu amene anabwela m’mbuyo anapitilizabe kucititsa kuti ufumu wa mafuko 10 uzilale mwa kuuzimu mpaka pamene unaonongedwa mu 740 B.C.E. Komabe, mosasamala kanthu kuti kulambila konama kunali kofala, Hoseya anatumikila mokhulupilika monga mneneli kwa zaka zosacepela 59. Kodi nafenso tili okonzeka kupitilizabe kulalikila caka ndi caka, ngakhale titakumana ndi citsutso ndi cizunzo?—2 Tim. 4:2.

3. Kodi zimene Hoseya anacita zimaonetsa bwanji cifundo ca Yehova?

3 Muziganizila Cifundo ca Yehova: Yehova anauza Hoseya kukwatila ‘mkazi wa dama.’ (Hos. 1:2) Ngakhale kuti mkazi wake, Gomeri, anabelekela Hoseya mwana wa mwamuna, iye pambuyo pake anabelekanso ana aŵili apathengo. Kufunitsitsa kwa Hoseya kuti akhululukile mkazi wake kumaonetsa cifundo cacikulu cimene Yehova anaonetsa kwa Aisiraeli pamene analapa. (Hos. 3:1; Aroma 9:22-26) Kodi ndife ofunitsitsa kudzimana zinthu zina kuti tidziŵikitse cifundo ca Yehova kwa anthu osiyana-siyana?—1 Akor. 9:19-23.

4. Kodi tingadzimane zinthu zotani kuti titumikile Yehova?

4 Atumiki ena a Yehova anasiya nchito zao zapamwamba kuti azithela nthawi yambili mu utumiki. Ena akhalabe mbeta kapena opanda ana kuti aike zinthu za Ufumu patsogolo. Pamene tiganizila zimene Hoseya anacita, tinganene kuti, ‘Ine sindikanakwanitsa kucita zimenezo.’ Komabe, ngati tipitilizabe kuyamikila cisomo ca Yehova ndi kudalila mphamvu ya mzimu wake woyela, iye angatigwilitsile nchito m’njila zimene sitinayembekezele, monga mmene Hoseya analili.—Mat. 19:26; Afil. 2:13.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani