Ndandanda ya Mlungu wa November 11
MLUNGU WA NOVEMBER 11
Nyimbo 119 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jl Phunzilo 23 mpaka 25 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Aheberi 1 mpaka 8 (Mph. 10)
Na. 1: Aheberi 4:1-16 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Tili Ndi “Nzelu Yocokela Kumwamba”?—Yak. 3:17, 18 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Cofunikila Kwa Akristu Ndi Kukonda Anzawo Basi?—rs tsa. 88 ndime 3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 73
Mph. 10: Mmene Tingathandizile Kusamalila Zosoŵa za Ena. Nkhani yokambidwa ndi mkulu yocokela mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2013, tsamba 8 ndi 9.
Mph. 10: Mmene Tingathetsele Mantha Polalikila. Kukambitsilana kozikidwa pa mafunso otsatilawa: (1) Kodi pemphelo lingatithandize bwanji tikacita mantha pamene tilalikila pakhomo? (2) N’cifukwa ciani kukonzekela bwino kumatithandiza kucepetsa mantha? (3) N’ciani cingatithandize kucepetsa mantha pamene tilalikila ndi woyang’anila dela? (4) Kodi kulalikila mokhazikika kumatithandiza bwanji kucepetsa mantha? (5) N’ciani cakuthandizani kuthetsa mantha?
Mph. 10: “Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Hoseya.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo 113 ndi Pemphelo