Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kugaŵila Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa
Cifukwa Cake Kuli Kofunika: Buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa ndi limodzi mwa zida zimene timagwilitsila nchito pophunzitsa anthu Baibulo. Komabe, timafunika kugaŵila munthu buku limeneli tisanayambe kuphunzila naye. Conco, tonse tifunika kuyesetsa kukhala aluso tikamagaŵila buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa mu ulaliki. (Miy. 22:29) Pali njila zambili zogaŵila bukuli, ndipo ofalitsa angaseŵenzetse njila imene aona kuti ingakhale yothandiza.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Pa kulambila kwanu kwa pabanja, yesezani mmene mungagaŵilile bukuli.
Mukakhala mu ulaliki, uzani mnzanu ulaliki umene mwakonzekela. (Miy. 27:17)Mukaona kuti ulaliki umene mwakonza si wogwila mtima, mungasinthe.