Nyimbo 118
Landiranani
1. Takulandirani inu nonse.
Mwasonkhana kuti m’phunzire.
Cho’nadi M’lungu amatipatsa
Timavomera akamatiitana.
2. Tikuyamikira abalewa
Chifukwa amatilandira.
Ndi amenewa tizikondana,
Tilandirenso ena odzasonkhana.
3. Aliyense akuitanidwa
Ndi M’lungu kudzaphunzitsidwa.
M’lungu watikokera kwa Iye
Choncho landiranani ndi mtima wonse.
(Onaninso Yoh. 6:44; Afil. 2:29; Chiv. 22:17.)