LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • fg phunzilo 13 Mafunso. 1-4
  • Kodi Uthenga Wabwino Wonena za Cipembedzo ndi Uti?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Uthenga Wabwino Wonena za Cipembedzo ndi Uti?
  • Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Zipembedzo Zonyenga Zimaimilako Mulungu Monama
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kanani Cipembedzo Conama!
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Kodi Mulungu Amavomeleza Zipembedzo Zonse?
    Njila ya Kumoyo Wamuyaya—Kodi Mwaipeza?
Onaninso Zina
Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
fg phunzilo 13 Mafunso. 1-4

PHUNZILO 13

Kodi Uthenga Wabwino Wonena za Cipembedzo ndi Uti?

1. Kodi zipembedzo zonse n’zabwino?

Munthu aŵelenga Baibo

Mu zipembedzo zonse muli anthu oona mtima. Ndi uthenga wosangalatsa kudziŵa kuti Mulungu amawaona anthu amenewo ndipo amawasamala. Koma comvetsa cisoni n’cakuti, anthu amagwilitsila nchito cipembedzo pofuna kucita zinthu zoipa. (2 Akorinto 4:3, 4; 11:13-15) Malinga ndi malipoti a panyuzi, zipembedzo zina zimatenga mbali m’zaucigawenga, kuphana kosankhana mitundu, nkhondo, ndi kuzunza ana acicepele. Zimenezi zimapweteka kwambili anthu oona mtima amene amakhulupilila Mulungu.​—Ŵelengani Mateyu 24:3-5, 11, 12.

Cipembedzo coona cimalemekeza Mulungu. Koma cipembedzo conama sicim’kondweletsa. Cimaphunzitsa zinthu zimene sizipezeka m’Baibo. Zinthu zimenezi zimaphatikizapo ziphunzitso zonama ponena za Mulungu ndi anthu akufa. Koma Yehova amafuna kuti anthu adziŵe coonadi ponena za iye.​—Ŵelengani Ezekieli 18:4; 1 Timoteyo 2:3-5.

2. Kodi uthenga wabwino wonena za cipembedzo ndi uti?

Cokondweletsa n’cakuti, zipembedzo zimene zimati zimakonda Mulungu koma m’ceni-ceni zimakonda dziko la Satana sizingam’namize. (Yakobo 4:4) Mau a Mulungu amati zipembedzo zonse zonama zimapanga “Babulo Wamkulu.” Babulo unali mzinda wakale kumene kunayambila cipembedzo conama pambuyo pa Cigumula ca m’masiku a Nowa. Posacedwa, Mulungu adzathetsa mwadzidzidzi cipembedzo cimene cimanama ndi kupondeleza anthu.​—Ŵelengani Chivumbulutso 17:1, 2, 5, 16, 17; 18:8.

Palinso uthenga wina wabwino. Yehova sanaiŵale anthu oona mtima amene ali m’zipembedzo zonama pa dziko lonse. Iye amagwilizanitsa anthu amenewo mwa kuwaphunzitsa coonadi.​—Ŵelengani Mika 4:2, 5.

3. Kodi anthu oona mtima ayenela kucita ciani?

Anthu akambitsilana pambuyo pa msonkhano wacikristu

Cipembedzo coona cigwilizanitsa anthu

Yehova amasamala anthu amene amakonda coonadi ndi zinthu zabwino. Amawalimbikitsa kuti acoke m’cipembedzo conama. Anthu amene amakonda Mulungu amafuna kusintha kuti am’kondweletse.​—Ŵelengani Chivumbulutso 18:4.

M’zaka za zana loyamba, pamene anthu oona mtima anamva uthenga wabwino kwa atumwi, anakondwela kwambili. Yehova anawaphunzitsa umoyo watsopano wabwino ndi wacimwemwe, wokhala ndi colinga ndi ciyembekezo cabwino. Iwo ndi citsanzo cabwino kwambili kwa ife cifukwa anamvela uthenga wabwino mwa kuika Yehova patsogolo.​—Ŵelengani 1 Atesalonika 1:8, 9; 2:13.

Yehova amalandila anthu amene amacoka m’cipembedzo conama kuloŵa m’banja la olambila ake. Ngati mungalandile ciitano cacikondi ca Yehova, mudzakhala naye paubwenzi. Mudzakhala m’banja latsopano ndi lacikondi la olambila anzanu a Yehova, ndipo mudzapeza moyo wosatha.​—Ŵelengani Maliko 10:29, 30; 2 Akorinto 6:17, 18.

4. Kodi Mulungu adzabweletsa bwanji cimwemwe padziko lonse?

Ciweluzo ca cipembedzo conama cimene cibwela ni uthenga wabwino. Ciweluzo cimeneci cidzabweletsa mpumulo kwa anthu onse. Ndipo cipembedzo conama sicidzasoceletsanso anthu kapena kuwagaŵanitsa. Anthu onse panthawiyo adzagwilizana pa kulambila Mulungu woona mmodzi yekha.​—Ŵelengani Chivumbulutso 18:20, 21; 21:3, 4.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 15 ndi 16 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani