CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MIYAMBO 22-26
“Phunzitsa Mwana m’Njila Yomuyenelela”
M’buku la Miyambo muli malangizo othandiza kwa makolo. Kuwongola mtengo ukali waung’ono kumathandiza kuti ukule woongoka. Mogwilizana na zimenezi, makolo afunika kuphunzitsa ana awo akali aang’ono. Akacita conco, adzathandiza anawo kuti akadzakula akakhale na mtima wofuna kutumikila Yehova.
22:6
Kuphunzitsa bwino ana kumafuna nthawi na khama
Makolo afunika kupeleka citsanzo cabwino kwa ana awo. Afunikanso kuwalangiza, kuwacenjeza, kuwalimbikitsa, ndi kuwapatsa cilango
22:15
Cilango ndi kuphunzitsa kwacikondi kumene kumathandiza mwana kusintha maganizo na mtima
Cilango cimene ana amafunikila cimakhala cosiyana-siyana