CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 11-16
Dziko Lapansi Lidzadzala na Ŵanthu Odziŵa Yehova
11:6-9
Kukwanilitsika kwa ulosiwu kwa Aisiraeli
Aisiraeli paulendo wawo wocoka ku ukapolo ku Babulo, ndiponso pamene anafika ku dziko lakwawo, sanafunikile kucita mantha ndi nyama za m’sanga, kapena anthu olusa monga nyama za m’sanga.—Ezara 8:21, 22.
Kukwanilitsika kwake masiku ano
Anthu asintha umunthu wawo cifukwa codziŵa Yehova. Anthu amene kale anali aciwawa akhala amtendele. Kudziŵa Mulungu kwacititsa kuti tikhale m’paradaiso wauzimu padziko lonse lapansi.
Kukwanilitsika kwa ulosiwu mtsogolo
Monga mmene Mulungu anali kufunila paciyambi, dziko lonse lidzasinthiwa na kukhala malo otetezeka, paradaiso wa mtendele. Palibe colengedwa cimene cidzayofya cinzake, munthu kapena nyama.
Paulo anasintha cifukwa codziŵa Mulungu
Pamene anali mfalisi, anali na makhalidwe monga a cilombo. —1 Tim. 1:13.
Kudziŵa zinthu molongosoka kunasintha umunthu wake. —Akol. 3:8-10.